Mutu 13

1 ndipo ndinaona chirombo chikuvuuka mnyanja, chokhala nazo nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri, ndipo pamwamba pa nyanga zake panali nduwira khumi, ndipo pamwamba pa mitu yake panali maina a ochitira mwano. 2Ndipo chilombo chimene ndinaona chinali ngati kambuku wathazi, ndipo mapazi ake ngati a chimbalangondo, ndipo kamwa lake ngati kamwa la mkango; ndipo chinjoka chinampatsa mphamvu yake, ndi ufumu wake, ndi ulamuliro waukulu; 3ndipo umodzi wa mitu yake [unali] ngati wodulidwa kufikira imfa, ndipo bala lake la imfa linachiritsidwa: ndipo dziko lonse lapansi linazizwa ndi chirombocho. 4Ndipo iwo anachilambira chinjokacho, chifukwa iye anapereka ulamuliro kwa chirombocho; ndipo iwo anachilambira chirombocho, nanena, Ndani amene angafanane ndi chilombochi? Ndipo ndi ndani amene angamenyane nacho nkhondo? 5Ndipo chinapatsidwa kamwa, kulankhula zinthu zazikulu ndi za mwano; ndipo chinapatsidwa ulamuliro kugwira ntchito yake kwa miyezi makumi anayi ndi iwiri. 6Ndipo chinatsegula pakamwa pake kunenera mwano Mulungu1, kunenera mwano dzina lake ndi chihema chake kumwamba. 7Ndipo chinapatsidwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwagonjetsa iwo; ndipo chinapatsidwa ulamuliro pa mtundu ulionse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi fuko; 8ndi onse okhala padziko lapansi adzachilambira, [aliyense] amene dzina lake silinalembedwe pa kukhazikitsidwa kwa dziko lapansi m’buku la moyo la Mwanawankhosa wophedwa. 9Ngati wina ali nalo khutu, amve. 10Ngati wina [atsogolera] ku ukapolo, iye adzapita ku ukapoloko. Ngati wina adzapha ndi lupanga, akuyenera kuphedwa ndi lupanga. Pano pali chipiliro ndi chikhulupiliro cha oyera mtima.

11Ndipo ndinaona chirombo china chikutuluka pansi; ndipo chinali ndi nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka; 12ndipo chinagwiritsa ntchito ulamuliro onse wa chirombo choyamba chija, ndipo chinapangitsa dziko lapansi ndi onse akukhalamo kulambira chirombo choyamba chija, chimene bala lake la imfa linachiritsidwa. 13Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu, kuti chinapangitsa ngakhale moto kutsika kuchoka kumwamba kufika padziko lapansi pamaso pa anthu. 14Ndipo chinanyenga iwo akukhala padziko lapansi mwa zizindikiro zimene zinapatsidwa kwa icho kuchita pamaso pa chirombocho, kuuza iwo akukhala padziko lapansi kupanga chifanizo cha chirombocho, chimene chili ndi bala la lupanga, ndipo chinali ndi moyo. 15Ndipo chinapatsidwa kupereka mpweya ku chifanizo cha chirombocho, kuti chifanizo cha chirombocho chidzilankhulanso, ndipo chikapangitse ochuluka amene sangachilambire chifanizocho aphedwe. 16Ndipo chinapangitsa onse, ana ndi akulu, ndi olemera ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, kuti apatsidwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pa mphumi pawo; 17ndipo kuti aliyense asathe kugula kapena kugulitsa pokhapokha akhale ndi chizindikirocho, dzina la chirombocho, kapena chiwerengero cha dzina lake. 18 Pano pali nzeru. Iye amene ali nako kumvetsetsa awerengere chiwerengero cha chirombocho: pakuti ndi chiwerengero cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.

1Elohimu