Mutu 27

1Ndipo pamene kunali ku m’mawa akulu ansembe onse ndi akulu a anthu anatenga upo wotsutsana naye Yesu cholinga kuti akamuphe Iye. 2Ndipo atamumanga Iye anamutsogolera namupereka kwa Pontiyo Pilato, kazembeyo.

3Pamenepo Yudase, amene anampereka Iye, pakuona kuti watsutsidwa, anadzimvera chisoni, nabweza ndalama makumi atatu za siliva zija kwa wamkulu wa ansembe ndi akulu, 4nanena, Ndachimwa ine [pa] kupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Chimenecho ndi chiyani kwa ife? Iwetu uzionera wekha [ku chimenechi]. 5Ndipo pakuponya pansi ndalama za siliva zija m’kachisi, iye anachokapo pamalopo, napita kukadzimangilira yekha. 6Ndipo akulu ansembe anatenga ndalama za silivazo nanena, Sikoyenera kuti tiponye ndalamazi m’chosonkhera, pakuti zimenezi ndiwo mtengo wa mwazi. 7Ndipo pamene anatenga uphungu, iwo anagulira ndalamazo munda wa woumba mbiya kukhala manda a alendo. 8Chifukwa chake mundawo unatchedwa Munda wa mwazi kufikira lero lino. 9Pamenepo chinakwaniritsidwa chimene chinalankhulidwa mwa Yeremiya mneneri, kunena kuti, Ndipo ndinatenga ndalama za siliva makumi atatu, mtengo wa iye amene anawerengedwa mtengo wake, amene [iwo amene anali] ana a Israyeli anaika mtengo wake, 10ndipo anazipereka izo ku munda wa woumba mbiya, kolingana ndi m’mene Ambuye anandilamulira ine.

11Koma Yesu anaimilira pamaso pa kazembe. Ndipo kazembeyo anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero ndinu. 12Ndipo pamene anamnenera akulu ansembe ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu. 13Pamenepo anati Pilato kwa Iye, Kodi sukumva kuti pali zinthu zingati zimene akunena iwo akuchitira umboni wotsutsana ndi iwe? 14Ndipo sanamuyankhe iye ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anali wodabwa kwambiri. 15Tsopano ku phwando la kazembe kunakhazikitsidwa kuti atulutse m’modzi wa andende ku khamulo, amene iwo amamufuna. 16Ndipo iwo anali naye pamenepo wandende wodziwika, dzina lake Baraba. 17Pamenepo iwo pakusonkhana pamodzi, Pilato anati kwa iwo, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu wotchedwa Khristu? 18Pakuti iye anadziwa kuti iwo anampereka Iye mwanjiru. 19Koma, pamene amati azikhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anamuitanitsa iye, nanena, Musachite kanthu kalikonse ndi [munthu] wolungamayo; pakuti ine ndavutika kwambiri kufikira lero m’maloto mwanga chifukwa cha Iyeyu. 20Komatu akulu ansembe ndi akulu anakolezera makamuwo kuti apemphe Baraba, ndi kumuononga Yesu. 21Ndipo kazembe pakuyankha anati kwa iwo, Ndani mwa awiriwa amene inu mufuna kuti ndikumasulireni? Ndipo iwo anati, Baraba. 22Pilato anati kwa iwo, Kodi nanga pamenepo ndidzachita naye chiyani Yesu amene akutchedwa Khristu? Iwo onse anati, Apachikidwe Iye. 23Ndipo kazembe anati, Kodi Iye wachita choipa chanji? Komatu iwo anafuulitsa koposa, nanena, Iye apachikidwe. 24Ndipo Pilato, pakuona kuti sizikuphula kanthu, koma kuti phokoso limakulirakulira, atatenga madzi, anasamba m’manja pamaso pa khamulo, nanena, Ine siwolakwa pa mwazi wa munthu wolungamayu: mudzionere inu [ku ichi]. 25Ndipo anthu onse pakuyankha anati, Mwazi wake [ukhale] pa ife ndi pa ana athu omwe. 26Pamenepo anawamasulira iwo Baraba; koma Yesu, atakwapulidwa [Iye], anampereka kuti apachikidwe.

27Pamenepo asilikali a kazembe, atamutengera [iwo] Yesu kubwalo la milandu, anamsonkhanitsira Iye khamu lawo lonse, 28ndipo atamuvula chovala chake, anamuveka mwinjiro wofiira; 29ndipo ataluka nkhata ya minga, anamveka Iye pamutu pake, ndi bango m’dzanja lake lamanja; ndipo, pakugwada maondo awo pamaso pake, anamchitira Iye chipongwe, nanena, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! 30Ndipo atamulavulira, iwo anatenga bango namkwapula [Iye] pamutu pake. 31Ndipo atamchitira chipongwe Iye, anamvula chovala chija, ndipo anamveka chovala chake, namtsogolera kokamupachika.

32Ndipo pamene iwo anali kupita anapeza munthu wa ku Kurene, dzina lake Simoni; iwo anamkakamiza iye apite [ndi iwo] kuti anyamule mtanda wake. 33Ndipo atafika ku malo otchedwa Gologota, amene amatanthauza Malo a bade, 34anampatsa Iye kumwa vinyo wosakaniza ndi ndulu; ndipo atalawa [ichi], Iye sanakwanitse kumwa. 35Ndipo atamupachika Iye, anagawana zovala zake pakati [pa iwo eni], nachita maere. 36Ndipo pakukhala pansi, iwo anamuyang’anira Iye kumeneko. 37Ndipo iwo anayika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda. 38Pamenepo anapachikidwa pamodzi ndi achifwamba awiri, wina kudzanja lamanja ndi wina lamanzere.

39Komatu anthu odutsa panjira anamchitira iye mwano, napukusa mitu yawo 40nanena, Iwe wakupasula kachisi ndi kum’manganso m’masiku atatu, udzipulumutse wekha. Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu1, tsika pa mtandapo. 41[Ndipo] momwemonso akulu ansembe anamchitira chipongwe, komanso alembi ndi akulu, ananena, 42Anapulumutsa ena, koma Iye mwini sangadzipulumutse. Iye ndi Mfumu ya Israyeli: mlekeni atsike tsopano pa mtandapo, ndipo ife tidzakhulupilira pa Iye. 43Anakhulupilira pa Mulungu2; msiyeni ampulumutse tsopano ngati afuna [kukhala] naye. Pakuti Iye anati, Ndine Mwana wa Mulungu3. 44Ndipo nawonso achifwamba amene anapachikidwa pamodzi ndi Iye ananenanso mau achipongwe pa Iye.

45Tsopano pa ola lachisanu ndi chimodzi panagwa mdima pa dziko lonse kufikira ola lachisanu ndi chinayi; 46koma pa ola lachisanu ndi chinayi Yesu anafuula ndi mau okweza, nanena, Eli, Eli, lama sabakitani? Ndiko kunena kuti, Mulungu4 wanga, Mulungu5 wanga, mwandisiyiranji Ine? 47Ndipo ena mwa iwo amene anaima pamenepo, pamene anamva [chimenechi], anati, [Munthu] uyu akuitana Eliya. 48Ndipo nthawi yomweyo m’modzi mwa iwo anathamanga natenga chinkhupule, nadzadza [icho] ndi vinyo wosasa nachiyika pa bango, nampatsa Iye kuti amwe. 49Koma ena onse anati, Talekani; tione ngati Eliya adzabwera kumpulumutsa Iye.

50Ndipo Yesu, atafuulanso ndi mau okweza, anapereka mzimu wake. 51Ndipo taonani, nsalu ya mkachisi inang’ambika pakati kuchokera kumwamba kufika pansi, ndipo dziko lapansi linagwedezeka, ndipo miyala inang’aluka, 52ndipo manda anatseguka; ndipo matupi ambiri a woyera mtima amene anagona kale anauka, 53ndipo anatuluka m’manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa mu mzinda woyera naonekera kwa ambiri.

54Koma kenturiyo, ndi iwo amene anali naye pakulondera Yesu, pakuona chivomezi ndi zinthu zimene zimachitika, anachita mantha akulu, nanena, Zoonadi [munthu] uyu anali Mwana wa Mulungu6. 55Ndipo analipo akazi ochuluka amene amaonerera patali, amene anamtsatira Yesu kuchokera ku Galileya namatumikira Iye, 56mwa iwo anali Mariya waku Magadala, ndi Mariya mayi wake wa Yakobo ndi Yose, ndi amake a ana amuna a Zebedayo.

57Tsopano atafika madzulo pamenepo panabwera munthu wolemera waku Arimateya, dzina lake Yosefe, amenenso iye mwini anali wophunzira wa Yesu. 58Iye, anapita kwa Pilato, napempha thupi la Yesu. Pamenepo Pilato analamulira kuti thupi lake liperekedwe. 59Ndipo Yosefe anatenga thupi lake, nalikulunga mu nsalu ya bafuta yoyera, 60ndipo analiyika m’manda ake atsopano amene anawasema m’mwala; ndipo atagubuduza mwala waukulu pa khomo la manda anachokapo. 61Koma Mariya wa Magadala anali pomwepo, ndi Mariya wina, wakukhala pansi moyang’anana ndi manda wosemawo.

62Tsopano m’mawa mwake, limene ndi tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzekera, akulu ansembe ndi Afarisi anabwera pamodzi kwa Pilato, 63nanena, Mfumu, ife takumbukira kuti wonyengayo anati pamene anali ndi moyo, Pakutha pa masiku atatu ndidzauka Ine. 64Lamulirani kuti mandawa atetezedwe kufikira tsiku lachitatu, kuti mwina wophunzira ake akhoza kubwera ndi kumuba Iye, namanena kwa anthu, wauka Iye kwa akufa; ndipo kulakwitsa komaliza kudzakhala koipa kusiyana ndi koyambako. 65Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mungathe kulondera: pitani, atetezeni monga mukudziwira. 66Ndipo anapita nawateteza manda wosemawo, atatseka ndi mwalawo, ndi alonda [m’mbalimo].

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu