Mutu 1

1Paulo, kapolo wa Mulungu1, ndi mtumwi wa Yesu Khristu molingana ndi chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu2, ndi chidziwitso cha choonadi monga mwa chipembedzo; 2mu chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu3, amene sanganame, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba, 3koma anaonetsera yekha mnyengo yake mau ake, m’kulalikira kumene ine ndinapatsidwa, molingana ndi lamulo la Mulungu4 Mpulumutsi wathu; 4kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro chodziwika [kwa ife]: Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu5 Atate, ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.

5Pachifukwa chimenechi ndinakusiya m’Krete, kuti iwe ukathe kukonza chimene chinatsalira osakonzedwa, ndi kukhazikitsa akulu mu mzinda ulionse, monga ndinakulamulira iwe: 6Ngati wina ali omasuka ku milandu yonse [yomutsutsa iye], mwamuna wa mkazi m’modzi, opanda mbiri yoledzera kapena yosamvera. 7Pakuti woyang’anira akhale wopanda mlandu ulionse [womutsutsa iye] monga mdindo wa Mulungu6; wosati wa makani, wosakhumba zonyansa, wosasokonezeka ndi vinyo, wosachita ndewu, wosakhumba phindu mu njira yoipa; 8koma akhale wochereza alendo, wokonda zabwino, wa nzeru, wolungama, wopembedza, wotentha mu uzimu, 9kukagwiritsitsa mau okhulupirika molingana ndi chiphunzitso chophunzitsidwacho, kuti akakhoze kulimbikitsa ndi chiphunzitso chabwino ndi kukaniza iwo akuphunzitsa zonyenga. 10Pakuti alipo ambiri ophunzitsa zonyenga ndi opusitsa malingaliro a anthu, maka iwo a kumdulidwe, 11amene akuyenera kutsekedwa pakamwa, amene amasocheretsa banja lonse, kuphunzitsa zinthu zimene sizikuyenera kuphunzitsidwa cholinga akapeze phindu mnjira yolakwika. 12Wina mwa iwo, mneneri waowao, ananena, Akrete amanena bodza nthawi zonse, zilombo zoipa, alesi adyera. 13Umboni uwu ndi woona; pachifukwa ichi uwadzudzule iwo koopsa, kuti akhale olimba m’chikhulupiriro, 14asayike malingaliro awo pa nthano za Chiyuda ndi malamulo a anthu kuchoka ku choonadi. 15Zinthu zonse ndi zoyera kwa oyera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira palibe choyera; koma malingaliro awo ndi chikumbumtima chawo zadetsedwa. 16 Amavomereza kuti amamudziwa Mulungu7, koma mu ntchito amukana [iye], pokhala onyazitsa, ndi osamvera, ndi kupezedwa opanda pake mu ntchito zonse zabwino.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu