Mutu 12
1?Koma zokhudza mphatso za mzimu, abale, sindifuna inu mukhale osadziwa. 2Mudziwa kuti pamene munali amitundu munatsogozedwa ku mafano osalankhula, munatsogozedwa njira ina iliyonse. 3?Pamenepo ndikupatsani inu kuti mudziwe, kuti palibe munthu, wolankhula mu mphamvu ya Mzimu wa Mulungu1, nanena kuti, Wotembereredwa Yesu; ndipo palibe munthu wakunena, Ambuye Yesu, pokhapokha mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 4?Komatu pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo; 5?ndiponso pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo; 6?ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu2 yemweyo amene amachita zinthu zonse mwa onse. 7?Koma kwa aliyense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule. 8?Pakuti kwa wina, mwa Mzimu, anapatsidwa mau a nzeru; ndipo kwa wina mau a chidziwitso, kolingana ndi Mzimu yemweyo; 9?ndipo kwa wina chikhulupiliro china, mu mphamvu ya Mzimu yemweyo; ndipo kwa wina mphatso za machiritso mu mphamvu ya Mzimu yemweyo; 10?ndipo kwa wina machitidwe a zozizwa; ndipo kwa wina uneneri; ndipo kwa wina kuyesa mizimu; ndipo kwa wina malilime amitundumitundu; ndipo kwa wina kumasulira malilime. 11?Koma zonsezi zichitika ndi Mzimu m’modzi yemweyo, kugawira wina aliyense monga Iye afunira. 12?Pakuti ngakhale thupi lili limodzi ndipo lili nazo ziwalo zambiri, koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi, chimodzimodzinso Khristu. 13?Pakutinso mu mphamvu ya Mzimu m’modzi tonsefe tabatizidwa m’thupi limodzi, kaya Myuda kapena Mhelene, kaya ndi kapolo kapena mfulu, ndipo tonse tapatsidwa kumwa mwa Mzimu m’modzi. 14?Pakutinso thupi sichiwalo chimodzi koma zambiri. 15?Ngati phazi likati, Chifukwa sindine dzanja sindili wa thupili, kodi silili lathupi pachifukwa chimenechi? 16?Ndipo ngati khutu likati, Chifukwa sindine diso sindili wa thupili, kodi silili lathupi pachifukwa chimenechi? 17?Ngati thupi lonse likanakhala diso, kodi tikanamvera chiyani? Ngati thupi lonse likanakhala khutu, kununkhiza kukanakhala kuti? 18?Koma tsopano Mulungu3 anakhazikitsa ziwalo, chilichonse m’thupilo, monga mwa kufuna kwake. 19?Koma ngati zonsezi zikanakhala chiwalo chimodzi, thupi likanakhala kuti? 20?Komatu tsopano ziwalo zili zambiri, ndipo thupi ndi limodzi. 21?Diso silinganene kwa dzanja, Sindikufuna iwe; kapenanso, mutu kunena kwa phazi, Sindikufuna iwe. 22?Koma makamaka, ziwalo za thupi zimene zioneka zofooka zili zofunika; 23?ndipo ziwalo za thupi zimene zikuoneka zopanda ulemu, zimenezi timaziveka ndi ulemelero wopambana; ndipo ziwalo zathu zosaoneka bwino zikhala nacho chokometsera; 24?koma ziwalo zathu zooneka bwino zikhala zosasowa kathu. Koma Mulungu4 analumikizitsa thupi pamodzi, napereka ulemu waukulu ku chiwalo chimene chili chosowa; 25?kuti pasakhale kugawikana m’thupi, koma kuti ziwalo zikakhale ndi kukhudzika kofanana pa wina ndi mzake. 26?Ndipo ngati chiwalo chimodzi chivutika, ziwalo zonse zivutike nacho pamodzi; ndipo ngati chiwalo chimodzi chikwezedwa, ziwalo zonse zikondwere nacho pamodzi. 27?Tsopano ndinu thupi la Khristu, ndipo ndinu chiwalo cha thupilo. 28?Ndipo Mulungu5 anakhazikitsa ena mu mpingo: koyamba, atumwi; kachiwiri, aneneri; kachitatu, aphunzitsi; kenako mphamvu za zozizwa; kenanko mphatso za machiritso; zothandiza ena; zolamulia; malilime amitundumitundu. 29?Kodi onse ali atumwi? Kodi onse ali aneneri? Kodi onse ali aphunzitsi? Kodi onse ali nayo mphamvu ya kuchita zozizwa? 30?kodi onse ali nazo mphatso za machiritso? Kodi onse amalankhula malilime? Kodi onse amamasulira malilime? 31?Koma funitsitsani mphatso zikuluzikulu, ndipo pamenepo ndizakuonetsani inu njira yabwino ndi yopambana.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu