Mutu 9
1Ndipo atawaitanitsa pamodzi khumi ndi awiriwo, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi kuchiritsa matenda, 2ndi kuwatumiza iwo kukalalikira ufumu wa Mulungu1 ndi kuchiritsa odwala. 3Ndipo Iye anati kwa iwo, Musatenge kanthu kalikonse ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; kapena kukhala nawo malaya awiri. 4Ndipo nyumba iliyonse imene mudzalowe, khalani m’menemo ndipo muzikachokera m’menemo. 5Ndipo onse amene sakakulandirani, potuluka mu mzinda umenewo, sasani ngakhale fumbi la kumapazi kwanu pochitira umboni otsutsana nawo. 6Ndipo popita iwo anadutsa m’midzi, nalengeza uthenga wabwino ndi kuchiritsa paliponse.
7Ndipo Herode chiwangacho anamva zinthu zonse zimene zinachitidwa [ndi Iye], ndipo anathedwa nzeru, chifukwa kunanenedwa ndi ena kuti Yohane wauka kwa akufa, 8ndipo ena kuti Eliya waonekera, ndipo ena kuti m’modzi wa aneneri akale waukanso. 9Ndipo Herode anati, Yohane ine ndinamdula mutu, koma uyu ndi ndani amene ndikumva zinthu zotere? Ndipo anafunitsitsa kumuona Iye.
10Ndipo atumwi pobwerera anamfotokozera Iye zonse zimene iwo anazichita. Ndipo Iye anawatenga iwo napatuka nawo [kumalo a chipululu] mu mzinda wotchedwa Betsaida. 11Koma makamu podziwa [ichi] anamtsatira Iye; ndipo Iye anawalandira nalankhula kwa iwo za ufumu wa Mulungu2, ndi kuchiritsa iwo amene amafunika machiritso. 12Koma tsiku linali nkupita, ndipo khumi ndi awiriwo anadza nati kwa Iye, Liuzeni khamu la anthuwa kuti lipite kumidzi yozungulira, ndi kuminda, ndi kumiraga ndi kupeza chakudya, pakuti kuno kumene tili ndi kuchipululu. 13Ndipo Iye anati kwa iwo, Apatseni chakudya inuyo. Ndipo iwo anati, Tilibe mikate yopitilira isanu ndi nsomba ziwiri, pokhapokha ife tipite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa; 14pakuti analipo amuna pafupifupi zikwi zisanu. Ndipo anati kwa ophunzira ake, Akhalitseni pansi m’magulu a anthu makumi asanu. 15Ndipo anachita chomwecho, nawakhalitsa iwo pansi. 16Ndipo pamene anatenga mikate isanu ndi nsomba ziwiri, anayang’ana kumwamba nazidalitsa izo, ndi kuzinyema napereka kwa ophunzira ake nagawira khamulo. 17Ndipo iwo onse anadya nakhuta; ndipo anatolera makombo mitanga khumi ndi iwiri.
18Ndipo kunachitika kuti pamene Iye yekha amapemphera, ophunzira ake anali naye pamodzi, ndipo anawafunsa nati, Kodi makamu amati ndine ndani? 19Koma iwo poyankha anati, Yohane m’batizi; koma ena amati, Eliya; ndipo ena amati, kuti m’modzi wa aneneri akale waukanso. 20Ndipo Iye anati kwa iwo, Koma inu, mumati ndine ndani? Ndipo Petro poyankha anati, Khristu wa Mulungu3. 21Koma Iye anawauza mowalamulira, kuti asauze munthu wina aliyense, 22nanena, Mwana wa munthu azazunzika zinthu zambiri, ndipo adzakanidwa ndi akulu ndi akulu ansembe ndi alembi, ndipo adzaphedwa, ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwa. 23Ndipo Iye anati kwa [iwo] onse, Ngati wina adza pambuyo panga, azikanize yekha nasenze mtanda wake tsiku ndi tsiku ndi kunditsata Ine; 24pakuti amene akhumba kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine, iyeyu adzaupulumutsa. 25Pakuti munthu adzapindula chiyani ngati apeza dziko lonse lapansi, ndi kuonongeka, kapena kutayika iye mwini? 26Pakuti aliyense wakuchitira Ine manyazi ndi mau anga, ameneyo Mwana wa munthu adzachita naye manyazi pamene Iye adzabwera mu ulemelero wake, komanso wa Atate, ndi wa angelo oyera. 27Komatu ndinena kwa inu m’choonadi, Alipo ena akuyimilira pano amene sadzalawa imfa kufikira adzaona ufumu wa Mulungu4.
28Ndipo kunachitika kuti atangolankhula mau awa, popita masiku asanu ndi atatu, anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo anapita ku phiri kukapemphera. 29Ndipo pamene Iye amapemphera maonekedwe a nkhope yake anasandulika ndipo chovala chake chinawala [ndi] kunyezimira. 30Ndipo taonani, anthu awiri amalankhula ndi Iye, amene anali Mose ndi Eliya, 31amene powonekera mu ulemelero, analankhula za kuchoka kwake kumene Iye adzakwaniritsa mu Yerusalemu. 32Koma Petro ndi iwo amene anali naye analemedwa ndi tulo: koma atayera m’maso anaona ulemerero wake, ndi anthu awiri amene anayima pamodzi ndi Iye. 33Ndipo kunachitika kuti pamene anachoka kwa Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, Zili bwino kuti ife tili pano; ndipo tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya: osadziwa zimene iye amalankhula. 34Koma pamene amalankhula zinthu izi, panadza mtambo ndipo unawaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene amalowa mu mtambomo: 35ndipo panali mau ochokera mu mtambomo nanena, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa: mvereni Iye. 36Ndipo pamene mau [amamveka] Yesu anapezeka kuti ali yekha: ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu wina aliyense m’masiku amenewo zinthu zimene iwo anaziona.
37Ndipo kunachitika kuti tsiku lotsatira, pamene anatsika pa phiri, khamu lalikulu linakumana ndi Iye. 38Ndipo taonani, munthu wina mu khamulo anafuula nanena, Mphunzitsi, ndikupemphani muone mwana wanga, pakuti ndi mwana wanga yekhayo: 39ndipo taonani, mzimu umamutenga, ndipo modzidzimuka amafuula, ndipo umamung’amba iye ndi thovu kukamwa, ndipo movutikira umachoka mwa iye utampweteka. 40Ndipo ine ndinawapempha ophunzira anu kuti awutulutse, ndipo sanakwanitse. 41Ndipo Yesu poyankha anati, M’badwo wosakhulupilira ndi wamphulupulu, ndidzakhala ndi inu ndi kukupilirani kufikira liti? M’bweretse kuno mwana wako. 42Koma pamene amabwera naye, chiwanda chinamung’amba ndi kumugwetsa pansi. Ndipo Yesu anadzudzula mzimu woipawo, ndi kumchiritsa mwanayo nampereka kwa atate wake. 43Ndipo onse anali ozizwa ndi ulemelero wa ukulu wa Mulungu5.
Ndipo pamene onse anali odabwa ku zinthu zonse zimene [Yesu] anachita, Iye anati kwa ophunzira ake, 44Lolani inu mau awa alowe m’makutu mwanu. Pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu. 45Koma iwo sanazindikire kulankhula uku, ndipo chinabisidwa kwa iwo kuti asazindikire ichi. Ndipo iwo anaopa kumufunsa zokhuza malankhulidwe awa. 46Ndipo kutsutsana kunadza pakati pawo, ndani amene akuyenera kukhala wamkulu pakati pawo. 47Ndipo Yesu, poona kutsutsanaku mkati mwao, anatenga mwana wamng’ono namuika pambali pake, 48ndipo anati kwa iwo, Amene adzalandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandira Ine, ndipo amene walandira Ine walandira Iye amene anandituma Ine. Pakuti iye amene ali wamng’ono pakati pa inu nonse, iyeyo ndi wamkulu. 49Ndipo Yohane poyankha anati, Ambuye, ife tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndipo tinamuletsa iye, chifukwa satsatana nafe. 50Ndipo Yesu anati kwa iye, Musamukanize [iye], pakuti amene satsutsana ndi inu ali nanu.
51Ndipo kunachitika kuti pamene masiku akuti alandiridwe anali kukwaniritsidwa, Iye anatsimikiza kupenya nkhope yake ku Yerusalemu. 52Ndipo Iye anatuma a mithenga patsogolo pake. Ndipo pakupita iwo analowa m’mudzi wa Asamariya kuti akamukonzere Iye malo. 53Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali [itatembenukira ngati] akupita ku Yerusalemu. 54Ndipo ophunzira ake Yakobo ndi Yohane pakuona [ichi] anati, Ambuye, kodi mufuna tilankhule [kuti] moto utsike kumwamba ndi kuwatentha iwowa, monganso anachitira Eliya? 55Koma Iye potembenuka anawadzudzula iwo [ndipo anati, Simudziwa mzimu umene muli nawo]. 56Ndipo iwo anapita kumudzi wina.
57Ndipo kunachitika kuti pamene amayenda panjira, wina anati kwa Iye, Ndidzakutsatirani kwina kulikonse kumene mudzapita, Ambuye. 58Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nawo mapanga ndi mbalame zakumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe poti akhoza kugoneka mutu wake. 59Ndipo Iye anati kwa wina, Nditsate Ine. Koma iye anati, Ambuye, mundilole kupita kaye kukaika bambo anga. 60Koma Yesu anati kwa iye, Asiye akufa aike akufa awo, koma iwe pita ukalengeze uthenga wa Mulungu6. 61Ndipo winanso anati, Ine ndidzakutsatani, Ambuye, koma poyamba mundilole ndikatsanzikane ndi akunyumba kwanga. 62Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu amene amagwira khasu ndi kuyang’ana m’mbuyo amakhala woyenera pa ufumu wa Mulungu7.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu