Mutu 22

1Abale inu ndi atate, imvani mau akuzitetezera kwanga amene ndikukuuzani inu. 2Ndipo pakumva zimenezi iye anawalankhula iwo m’Chiheberi, iwo anakhala bata lalikulu; ndipo iye anati, 3Ine ndi Myuda, wobadwira m’Tariso wa Kilikiya, koma ndinaleledwa mu mzinda omwe uno, pa mapazi a Gamaliyeli, kuphunzitsidwa molingana ndi chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, pokhala ndi changu pa Mulungu1, monga inu nonse mulili lero; 4wozunzidwa mnjira iyi kufikira imfa, kumangidwa ndi kuponyedwa m’ndende onse amuna ndi akazi omwe; 5monganso mkulu wa ansembe andichitira ine umboni, ndi bwalo lonse la akulu: kwa amenenso, polandira makalata kwa abale, ndinapita ku Damasiko kukawatenganso iwo amene anali kumeneko, omangidwa, kupita nawo ku Yerusalemu, kukalangidwa. 6Ndipo kunachitika kuti pamene ndinkayenda kuwandikira ku Damasiko, chakumasana, kunaoneka kuwala kwakukulu kochokera kumwamba mozungulira ine. 7Ndipo ndinagwa pansi, ndipo ndinamva mau akunena kwa ine, Saulo, Saulo, chifukwa chiyani ukundizunza ine? 8Ndipo ine ndinayankha, Ndinu ndani, Ambuye? Ndipo Iye anati kwa ine, Ndine Yesu m’Nazarayo, amene ukundizunza. 9Koma iwo amene anali nane anaona kuwalako, [ndipo anadzala ndi mantha], koma sanamve mau a Iye amene amalankhula kwa ine. 10Ndipo ine ndinati, Kodi ndichite chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Dzuka, ndipo upite ku Damasiko, ndipo kumeneko zizanenedwa kwa iwe zinthu zonse zimene uyenera kuchita. 11Ndipo pamene sindinathe kuona, kudzera mu ulemelero wa kuwalako, ndinatsogozedwa ndi dzanja la iwo amene anali nane, ndinafika ku Damasiko. 12Ndipo munthu wina Hananiya, munthu wopembedza monga mwa chilamulo, wochitidwa umboni ndi Ayuda onse amene amakhala [kumeneko], 13anadza kwa ine ndipo anayima pafupi nane, nati kwa ine, M’bale Paulo, landira kuona kwako. Ndipo ine, mu ola lomwelo, ndinalandira kuona kwanga ndipo ndinapenya. 14Ndipo iye anati, Mulungu2 wa makolo athu wakusankhiratu iwe kudziwa cholinga chake, ndi kuona wolungamayo, ndi kumva mau ochokera mkamwa mwake; 15pakuti iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waona ndi kumva. 16Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka ndipo ubatizidwe, ndipo machimo ako achotsedwe, poyitanira dzina lake. 17Ndipo kunachitika kuti pamene ndinabwerera ku Yerusalemu, ndipo pamene ndimapemphera m’kachisi, kuti ndinakhala monga wokomoka, 18ndipo ndinamuona Iye akuti kwa ine, Chita changu ndipo tuluka mwachangu mu Yerusalemu, pakuti iwo sadzalandira umboni wako wokhudza Ine. 19Ndipo ine ndinati, Ambuye, iwo eni akudziwa kuti ndimatsekera ndi kumenya iwo amene amakhulupilira pa Inu; 20ndipo pamene mwazi wa mboni Yanu Stefano unakhetsedwa, ine ndinali kuyima pomwepo ndi kuvomereza, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye. 21Ndipo Iye anati kwa ine, Pita, pakuti ndikutuma iwe kwa amitundu akutali. 22Ndipo iwo anamumva kufikira mau awa, ndipo anakweza mau awo, nanena, Achoke munthu wotere padziko lapansi, pakuti sikoyenera kuti akhale ndi moyo. 23Ndipo pamene iwo anafuula, ndi kutaya zovala zawo, ndi kuwaza fumbi mlengalenga, 24kapitao wamkulu analamulira iye kuti abweretsedwe ku linga, nanena kuti afunsidwe pa kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chiyani iwo amafuula motsutsana naye. 25Koma pamene iwo anam’manga ndi nsinga, Paulo anati kwa kenturiyo amene anayima pomwepo, Kodi ndi kololedwa kwa inu kumanga munthu amene ndi m’Roma musanamve mlandu wake? 26Ndipo kenturiyo, pakumva ichi, anapita kukawuza kapitao wamkulu, nanena, Kodi muchita chiyani? Pakuti munthu uyu ndi m’Roma. 27Ndipo kapitao wamkulu anabwera nati kwa iye, Tandiuze, kodi ndiwe m’Roma? Ndipo iye anati, Inde. 28Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine, ndinagula umzika uwu ndi mtengo waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ineyo ndinabadwanso mfulu. 29Pamenepo nthawi yomweyo iwo amene amafuna kumufunsa mafunso anamusiya, ndipo kapitao wamkulu anachitanso mantha pamene anazindikira kuti anali m’Roma, ndi chifukwa kuti anam’manga iye. 30Ndipo m’mawa mwake, pofuna kudziwa chenicheni [cha nkhaniyi] chifukwa chiyani Ayuda anamneneza, anam’masula iye, ndipo analamulira akulu ansembe ndi akulu a bwalo kuti akumane, ndipo anam’bweretsa Paulo namuyika pamaso pawo.

1Elohimu2Elohimu