Mutu 28
1Ndipo pamene tinapulumukira [ku mtunda] pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinali chotchedwa Melita. 2Komatu akunja anationetsera ife chifundo chosowa; pakuti, anakoleza moto, natilowetsa ife mkati chifukwa cha mvula imene imagwa komanso chifukwa cha kuzizira. 3Ndipo Paulo anali kusonkhetsa nkhuni m’mitolo naziyika pamoto, njoka inatuluka mu mtolomo chifukwa cha kutentha ndipo inaluma dzanja lake. 4Ndipo pamene akunjawo anaona chilombocho chikulendewera pa dzanja lake, anati kwa wina ndi mzake, Munthu uyu ndithu ndi chigawenga, amene, [ngakhale] wapulumuka pa nyanja, Nemesisi sanamulole akhale ndi moyo. 5Pamenepo iye, anakutumulira chilombocho pamoto, osapwetekedwa. 6Koma iwo anayembekezera kuti iye adzatupa ndi kufa mwadzidzidzi. Koma iwo atadikira kwa nthawi yaitali ndipo palibe chimene chinachitika chachilendo kwa iye, anasintha malingaliro awo, ndipo anati uyu ndi mulungu1.
7Tsopano m’dziko lozungulira malowo panali minda imene mwini wake anali mkulu wa chisumbucho, dzina lake Pobliyo, amene anatilandira ife natichitira zabwino kwa masiku atatu mwa chifundo. 8Ndipo kunachitika kuti atate wake a Pobliyo anadwala malungo ndi kamwazi; kwa ameneyu Paulo analowa, nampempherera ndi kusanjika manja pa iye ndipo anamchiritsa. 9Koma zitachitika zimenezi, ena onse anabweretsanso odwala pa chisumbucho ndipo anachiritsidwa: 10amenenso anatichitira ulemu waukulu, ndipo pamene timachokako anatipatsa mphatso ife zimene zinatumikira zosowa zathu.
11Ndipo pakutha pa miyezi itatu tinayenda m’ngalawa ya m’Alesandriyo pamene pa chisumbupo pamazizira, ndi chisonyezo cha mphepo ya Dioskuri kutanthauza [Ana a mapasa]. 12Ndipo pamene tinafika ku Surakusa tinakhalako masiku atatu. 13Kumeneko, pozungulira tinafika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi, mphepo inatembenukira ku m’mwera, pa tsiku lachiwiri tinafika ku Potiyolo, 14kumeneko, tinapeza abale, ndipo anatipempha kuti tikhale nawo kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo pamenepo tinapita ku Roma. 15Ndipo kumeneko abale, pamene anamva za ife, anabwera kudzakumana nafe kuchokera ku Apiyo Foramu ndi Tresi Tabanayo, amene Paulo powaona, analemekeza Mulungu2 nalimbikitsidwa.
16Ndipo pamene tinafika ku Roma, [kenturiyo anawapereka andende kwa mkulu wa bwalo, koma] Paulo anamulola akhale payekha ndi msilikali amene amamuyang’anira. 17Ndipo kunachitika kuti pakutha masiku atatu, kuti anayitana pamodzi iwo amene anali akulu a Ayuda; ndipo pamene iwo anabwera pamodzi anati kwa iwo, Abale, ine ngakhale sindinachimwire anthuwa kapena miyambo ya makolo athu, ndaperekedwa ngati wandende kuchokera ku Yerusalemu kupita m’manja mwa Aroma, 18amene pondifunsa ine anaganiza kuti andimasule, chifukwa panalibe mwa ine kanthu koyenera kuti ndiphedwe. 19Koma Ayuda poyankhula motsutsana nazo, ndinakakamizika kuzadandaula kwa Kaisara, osati kuti ndili ndi kanthu kotsutsana nalo fuko langa. 20Pamenepo chifukwa cha ichi ndakuitanitsani kuti ndionane nanu ndi kulankhula nanu; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israyeli ndamangidwa unyolo uwu. 21Ndipo iwo anati kwa iye, Kumbali yathu sitinalandire makalata kuchokera ku Yudeya okhudza iwe, kapenanso wina wa abale amene afikawa kukuneneza koipa kokhudza iwe. 22Koma ife tikufuna kumva kuchokera kwa iwe chimene ukuganiza, zokhudza mpatuko uwu umene wamveka kwa ife umene paliponse akulankhula motsutsana nawo. 23Ndipo pamene anampangira tsiku ambiri anabwera kwa iye kumene amakhala, ameneyo anawafotokozera, kuwachitira umboni za ufumu wa Mulungu3, ndipo anawakopa iwo zokhudza Yesu, kuchokera ku chilamulo cha Mose ndi aneneri, kuyambira m’mawa mpaka madzulo. 24Ndipo ena anakopeka pa zinthu zimene zinanenedwa, koma ena sanakhulupilire. 26Ndipo posagwirizana pakati pawo iwo anachokapo; Paulo analankhula mau amodzi, Mzimu woyera analankhula bwino mwa mneneri Yesaya kwa makolo athu, nanena, Pitani kwa anthu awa, ndi kunena, Kumva mudzamva ndipo simuzazindikira, ndipo kupenya mudzapenya koma osaona. 27Pakuti mtima wa anthu awa wanenepa, ndipo amamva kwambiri ndi makutu awo, ndipo iwo atseka maso awo; kuti angapenye ndi maso awo, ndi kumva ndi makutu awo, ndi kuzindikira ndi mtima wao, ndi kutembenuka, ndipo ndidzawachiritsa iwo. 28Pamenepo kudziwike kwa inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu4 chatumizidwa kwa amitundu; kuti iwo adzamvanso [zimenezi]. 29 [Ndipo iye atalankhula izi, Ayuda anachokapo, nakambirana kwakukulu pakati pawo.] 30Ndipo iye anakhala zaka ziwiri zathunthu mnyumba yake yobwereka, ndipo analandira onse amene anabwera kwa iye, 31nalalikira ufumu wa Mulungu5, ndi kuphunzitsa zinthu zokhudza Ambuye Yesu Khristu, mwa ufulu popanda womletsa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu