Mutu 3
1Kodi pamenepo kuposa kwa Myuda ndi kuti? Kapena mdulidwe uli ndi phindu lanji? 2Zambiri mosemose: ndipo choyamba, zoonadi, kuti kwa iwo mau a Mulungu1 anaperekedwa kwa iwo. 3Nanga zili bwanji? Ngati ena sanakhulupilire, kusakhulupilira kwao kwapangitsa chikhulupiliro cha Mulungu2 kukhala chabe? 4Musaganize choncho: koma lolani Mulungu3 kukhala woona, ndipo munthu aliyense wabodza; molingana ndi momwe kunalembedwera, Kuti inu mukalungamitsidwe m’mau anu, ndi kuti mukagonjetse pamene inu mukaweruzidwa. 5Koma ngati kusalungama kwathu kutsimikizira kulungama kwa Mulungu4, tikanena chiyani? Kodi Mulungu5 ali wosalungama amene abweretsa mkwiyo? Ine ndilankhula molingana ndi munthu. 6Musaganize choncho: adzaweruza bwanji Mulungu6 dziko lapansi? 7Pakuti ngati choonadi cha Mulungu7, mwa kunama kwanga, chachulukitsa kwambiri ku ulemelero wake, chifukwa chiyani inenso ndiweruzidwa ngati wochimwa? 8ndipo osati, molingana ndi momwe tilankhulidwira mowawa, ndi momwe ena atsimikiza kuti ife tinena, Tiyeni tichite zinthu zoipa, kuti zabwino zibwere? Amene chiweruzo chawo ndi cholungama.
9Titani pamenepo? Kodi ndife oposa ena? Ayi ndithu, mwanjira ina iliyonse: pakuti ife tinalankhula kale kuti Ayuda ndi Ahelene onse ali pansi pa uchimo: 10molingana ndi m’mene kunalembedwera, Palibe [munthu] wolungama, ngakhale m’modzi; 11palibe [munthu] amene ali wozindikira, palibe ndi m’modzi yemwe wakufuna Mulungu8. 12Onse anasochera mnjira yawo, onse pamodzi anakhala opanda pake; palibe munthu amene amachita zabwino, palibe ndi m’modzi yemwe: 13M’mero wawo ndiwo manda apululu; ndi lilime lawo amaligwiritsa ntchito mwachinyengo; ululu wa mamba uli pansi pa lilime lawo: 14amene kamwa lawo ladzadza ndi matemberero ndi kuwawidwa; 15mapazi awo achita liwiro kukakhetsa mwazi; 16kusakaza ndi chisoni zili m’njira zawo, 17ndipo m’njira ya mtendere iwo sanayidziwe: 18palibe kumuopa Mulungu9 pamaso pawo. 19Tsopano ife tikudziwa kuti chilichonse chimene lamulo linena, limalankhula kwa iwo amene ali pansi pa lamulo, kuti kamwa lililonse litsekedwe, ndipo dziko lonse lapansi likhale pansi pa chiweruzo cha Mulungu10. 20Pamenepo mwa ntchito ya lamulo palibe thupi limene lidzalungamitsidwa pamaso pake; pakuti mwa lamulo uchimo udziwika.
21Koma tsopano popanda lamulo kulungama kwa Mulungu11 kwaonekera, kochitidwa umboni ndi lamulo ndi aneneri; 22kulungama kwa Mulungu12 mwa chikhulupiliro cha Yesu Khristu pa onse, ndi pa iwo onse okhulupilira: pakuti palibe kusiyana; 23pakuti onse anachimwa, ndipo anaperewera pa ulemelero wa Mulungu13; 24kulungamitsidwa mwaulere mwa chisomo kudzera mu chiombolo chimene chili mwa Khristu Yesu; 25amene Mulungu14 anakhazikitsa mpando wa chisomo, mwa chikhulupiliro m’mwazi wake, pakuonetsera kulungama kwake, potengera machimo amene anachitika kale, kudzera m’kuleza mtima kwa Mulungu15; 26poonetsa kulungama kwake mu nthawi yino, cholinga kuti akakhale wolungama, ndi kumulungamitsa amene ali mwa chikhulupiliro cha Yesu. 27Pamenepo kudzitama kuli pati? kwachotsedwa. Lamulo lake liti? La ntchito? Ayi ndithu, koma ndi lamulo la chikhulupiliro; 28pakuti ife tiyesa kuti munthu alungamitsidwa mwa chikhulupiliro, popanda ntchito za lamulo. 29Kodi [Mulungu] ndi Mulungu16 wa Ayuda okha? Kodi sali wa amitundunso? Inde, wa amitundunso: 30popezadi ndi Mulungu17 m’modzi amene adzalungamitsa mdulidwe pa mfundo ya chikhulupiliro, ndi kusadulidwa mwa chikhulupiliro. 31Kodi pamenepo tilipanga lamulo kukhala lopanda ntchito mwa chikhulupiliro? Musaganize choncho: [ayi,] ife tikukwaniritsa lamulo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15ElohimuElohimu16Elohimu17Elohimu