Mutu 3
1Chimodzimodzi, akazi, mverani amuna a inu nokha, kuti, ngakhale kuti ena samvera mau, akhoza kukopeka popanda mau koma chifukwa cha khalidwe la akazi awo, 2pochitira umboni khalidwe lanu loyera [lochitidwa] mwa mantha; 3limene kukongola kwake kusakhale kwa kunja kwa kuluka tsitsi, ndi kuvala golide, kapena kuvala zovala zokongola; 4koma munthu wobisika wa mu mtima, mu chokometsera chosawonongeka cha kudekha ndi mzimu wa chete, umene m’maso mwa Mulungu1 ndi wamtengo wake wapatali. 5Pakuti chomwechonso akazi oyera mtima amene ayembekezera mwa Mulungu2 adadzikongoletsa kale okha, kukhala omvera amuna awo a iwo okha; 6monga Sara anamvera Abrahamu, namtchula iye ambuye; amene inu mwakhala ana ake, kuchita zabwino, ndi kusachita mantha ndi mtundu ulionse wa mantha. 7Chimodzimodzi [inu] amuna, khalani nawo akazi monga mwa chidziwitso, monga chotengera chofooka, kuwapatsa [iwo] ulemu, monganso olowa nawo m’chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu asalandilidwe.
8Pomaliza, khalani nonse ndi mtima umodzi, achifundo, odzala ndi chikondi cha pa abale, okoma mtima, a mtima odzichepetsa; 9osabwezera choipa ku choipa, kapena chipongwe pa chipongwe; koma posiyanitsa, dalitsani [ena], chifukwa mwayitanidwa kuchita zimenezi, kuti mukalandire mdalitso. 10Pakuti iye amene akonda moyo ndi kuona masiku abwino, lilime lake lisiye kunena choipa ndi milomo yake kuti isalankhule chinyengo. 11Ndipo apewe choipa, ndi kuchita chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola; 12chifukwa maso a Ambuye ali pa olungama, ndipo makutu ake ali pa mapemphero awo; koma nkhope ya Ambuye ili motsutsana ndi iwo akuchita choipa. 13Ndipo ndani amene adzakuchitirani choipa ngati mwakhala otsanza chimene chili chabwino? 14Koma ngatinso mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala [ndinuyo]; koma musaope ndi mantha awo, kapena kusautsidwa; 15koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m’mitima mwanu, ndi kukhala nthawi zonse okonzeka kupereka yankho kwa aliyense amene angafunse inu kuyankhapo za chiymbekezo chimene chili mwa inu, koma ndi kudzichepetsa ndi mantha; 16ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino, kuti [monga ku chimene] iwo alankhula zotsutsana ndi inu monga ochita zoipa, akachititsidwe manyazi amene amakunenezani za khalidwe lanu labwino mwa Khristu. 17Pakuti ndi kwabwino, ngati chifuniro cha Mulungu3 chitero, kuzunzika monga ochita zabwino kusiyana ngati ochita zoipa; 18pakuti Khristu anavutikanso chifukwa cha machimo, wolungama chifukwa cha osalungama, kuti akatibweretse kwa Mulungu4; kuikidwa ku imfa m’thupi, koma kukhala wamoyo mu Mzimu, 19m’menemonso popita analalikira kwa mizimu imene ili mndende, 20osamvera kuyambira kale, pamene kupilira kwa Mulungu5 kunadikira mu nthawi ya Nowa pamene chingalawa chimakonzedwa, chimene anthu ochepa, ndiyo, miyoyo isanu ndi itatu, inapulumutsidwa mwa madzi: 21chithunzithunzi chimenenso tsopano chikupulumutsani inu, [ndicho] ubatizo, osati kuchotsedwa kwa zonyansa za mthupi, komatu monga mwa zofuna Mulungu6 wa chikumbumtima chabwino, mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu, 22amene ali kudzanja lamanja la Mulungu7, atapita kumwamba, angelo ndi a maulamuliro ndi zimphamvu kukhala zogonjera iye.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu