Mutu 10
1Ndipo ponyamuka Iye kumeneko anabwera ku magombe a Yudeya, ndi mbali ina ya Yordano. Ndiponso khamu linadza pamodzi kwa Iye, ndipo, monga Iye anazolowereranso, anawaphunzitsa iwo.
2Ndipo Afarisi pakudza kwa [Iye] anamfunsa, Kodi ndi kololedwa munthu kuchotsa mkazi [wake]? (namuyesa Iye). 3Koma Iye poyankha anati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani chiyani inu? 4Ndipo iwo anati, Mose analola kulemba kalata wachilekaniro, ndi kumchotsa. 5Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu iye analemba lamulo ili kwa inu; 6koma kuyambira pachiyambi pa chilengedwe Mulungu1 anawapanga iwo mwamuna ndi mkazi. 7Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana kwa mkazi wake, 8ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. 9Kotero chimene Mulungu2 anachiphatika pamodzi, munthu wina aliyense asachilekanitse. 10Ndiponso m’nyumba ophunzira anamufunsa Iye zokhudza chimenechi. 11Ndipo Iye anati kwa iwo, Aliyense amene adzachotsa mkazi wake nakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo. 12Ndipo ngati mkazi achotsa mwamuna wake nakwatira wina, achita chigololo iyeyu.
13Ndipo iwo anabweretsa tiana kwa Iye kuti atikhudze ito. Koma ophunzira anawadzudzula iwo amene anabweretsa [ito]. 14Koma Yesu pakuona [ichi] anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatikanize; pakuti Ufumu wa Mulungu3 uli wa totere. 15Ndithudi ndinena kwa inu, Aliyense amene sadzalandira ufumu wa Mulungu4 monga kamwana, sadzalowamo konse. 16Ndipo anatiyangata m’manja mwake, nasanjika manja ake pa ito, natidalitsa.
17Ndipo pamene Iye anali kupita panjira, munthu wina anathamangira kwa [Iye], ndipo anagwada namupempha, Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikalowe moyo wosatha? 18Koma Yesu anati kwa iye, Chifukwa chiyani unditchula Ine Wabwino? Palibe munthu wina Wabwino koma m’modzi, [ndiye] Mulungu5. 19Uwadziwa malamulo: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachitire umboni wonama, usanyenge, lemekeza atate wako ndi amayi wako. 20Ndipo poyankha anati kwa Iye, Mphunzitsi, zinthu zonsezi ndakhala ndikuzisunga kuyambira ndili wamng’ono. 21Ndipo Yesu pomuyang’ana iye anamkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa iwe: pita, kagulitse zonse uli nazo ndipo upereke kwa osauka, ndipo udzakhala nacho chuma m’mwamba; ndipo ubwere, nunditsate Ine, [utasenza mtanda wako]. 22Koma iye, pakumva chisoni ndi mau awa, anachoka wosweka mtima, pakuti anali ndi chuma chambiri. 23Ndipo Yesu pakuunguza anati kwa ophunzira ake, Kudzakhala kovuta kotani kwa iwo amene ali ndi chuma kulowa ufumu wa Mulungu6! 24Ndipo ophunzira anadabwa ndi mau ake. Ndipo Yesu poyankhanso anati kwa iwo, Ana inu, nkovuta kotani kwa iwo amene amatama chuma kulowa mu ufumu wa Mulungu7! 25Nkwapafupi kwa ngamila kudutsa pa bowo la singano kusiyana ndi wolemera kulowa mu ufumu wa Mulungu8. 26Ndipo iwo anaonjeza kudabwa, nanena wina ndi mzake, Ndipo ndani amene adzapulumuka? 27Koma Yesu powayang’ana iwo anati, Ndi anthu nzosatheka, koma osati ndi Mulungu9; pakuti zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu10.
28Petro anayamba kuyankhula kwa Iye, Taonani, ife tasiya zonse ndipo takutsatirani Inu. 29Yesu poyankha anati, Ndithudi ndinena kwa inu, Palibe munthu amene anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amayi, kapena [mkazi], kapena ana, kapena malo, chifukwa cha Ine komanso chifukwa cha uthenga wabwino, 30amene sadzalandira zana limodzi tsopano mu nthawi yino: nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi malo, pamodzi ndi mazunzo, ndi nthawi ilinkudza moyo wosatha. 31Komatu ambiri oyamba adzakhala otsirizira, ndipo otsirizira adzakhala oyamba.
32Ndipo iwo anali m’njira kupita ku Yerusalemu, ndipo Yesu anali patsogolo pawo; ndipo iwo anali odabwitsika, ndipo anachita mantha pamene amalondola. Ndipo pakudzitengera khumi ndi awiriwo kwa [Iye], anayamba kuwauza iwo zimene zizamuchitikira: 33Taonani, ife tipita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akulu ndi alembi, ndipo adzamuweruza Iye kuti aphedwe, ndipo adzamupereka kwa amitundu: 34ndipo iwo adzamnyoza Iye, ndi kumtunduza, ndi kumlavulira malovu, ndipo adzamupha Iye; ndipo pakupita masiku atatu adzaukanso.
35Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena [kwa Iye], Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chilichonse chimene tidzakupemphani Inu, mudzachichite chimenecho kwa ife. 36Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi mukufuna kuti ndidzachite chiyani kwa inu? 37Ndipo iwo anati kwa Iye, Tipatseni kwa ife kuti wina adzakhale kudzanja lamanja, ndi wina kudzanja lamanzere, mu ulemelero wanu. 38Ndipo Yesu anati kwa iwo, Inutu simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kukwanitsa kumwera chikho chimene Ine ndimwera, kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndibatizidwa nawo? 39Ndipo iwo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene Ine ndidzamwera inunso mudzamwera ndipo ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwa inunso mudzabatizidwa nawo, 40koma kukhala kudzanja langa lamanja kapena lamanzere si kwa Ine kupereka, komatu kwa iwo amene ichi chidakonzedweratu. 41Ndipo khumiwo pakumva [za ichi], anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane. 42Koma Yesu pamene anadziyitanira iwo kwa [Iye], anati nawo, Inu mudziwa kuti iwo amene awerengedwa kulamulira mafuko amachita umbuye pa iwo; ndipo anthu a mphamvu achita ulamuliro pa iwo; 43koma sizili choncho pakati panu; komatu aliyense wakukhala wamkulu pakati panu, adzakhala mtumiki wanu; 44ndipo aliyense wakukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. 45Pakutinso Mwana wa munthu sanadze kudzatumikiridwa, komatu kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake nsembe ya ambiri.
46Ndipo anabwera ku Yeriko, ndipo pamene Iye anatuluka ku Yeriko, ndi ophunzira ake pamodzi ndi khamu lalikulu, mwana wa Timeyu, Batumeyo, [munthu] wakhungu, anakhala m’mbali mwanjira kupemphetsa. 47Ndipo pakumva kuti ndi Yesu waku Nazarete, iye anayamba kufuula nanena, Inu Mwana wa Davide, Yesu, mundichitire chifundo ine. 48Ndipo ambiri anam’dzudzula iye, kuti akhale chete; komatu anafuulirabe kwambiri, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo ine. 49Ndipo Yesu, pakuyima chilili, nakhumbitsitsa iye ayitanidwe. Ndipo anamuyitana [munthu] wakhunguyo, nanena kwa iye, Limba mtima, tayimilira, Iye akukuyitana iwe. 50Ndipo, pakutaya chofunda chake, iye anayambapo nabwera kwa Yesu. 51Ndipo Yesu poyankha anati kwa iye, Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo [munthu] wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, kuti ndipenye. 52Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita, chikhulupiliro chako chakuchiritsa. Ndipo pomwepo anapenya, namtsatira Iye panjira.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu