Mutu 6

1Onse amene ali akapolo monga okhala mgoli awerengere ambuye awo oyenera ulemu, kuti dzina la Mulungu1 ndi chiphunzitso zisanyozeke. 2Ndipo iwo amene ali ndi ambuye okhulupirira, asawanyozetse popeza iwowa ndi abale; koma m’malo mwake awaunikire iwo ndi kumvera konse, chifukwa ali okhulupirika ndi okondedwa, amene amapindula mwa ubwino ndi kukonzekera kutumikira. Zinthu zimenezi uphunzitse ndi kuchenjeza. 3Ngati wina aphunzitsa mosiyana, ndipo savomerezana ndi mau amoyo, amene ali a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitso chimene chili molingana ndi umulungu, 4wadzitukumula, sadziwa kanthu, ndipo amafunafuna mafunso nayambitsa mau a mikangano, m’mene mumatuluka njiru, kulimbana, mau onyoza, kuganizirana zoipa, 5mikangano yosatha ya anthu osokonezeka m’malingaliro ndiponso amene anachoka pa choonadi, nagwiritsitsa chopindulitsa kukhala [chimaliziro cha] umulungu. 6Komatu umulungu okhala ndi kukhutitsidwa kwa mu mtima ndiwo phindu lalikulu. 7Pakuti sitinabweretse kanthu m’dziko lapansi: zaonetsedwa kuti sitidzakhoza kutenga kanthu kutuluka nako. 8Koma pokhala nazo zotisamala ndi zotiphimba, ife tidzakhutira nazo zimenezi. 9Koma iwo amene akhumba kukhala olemera amagwa muyesero ndi mumsampha, ndi zinthu zambiri zopanda nzeru komanso zilakolako zoipa, zimene zimamiza anthu mu chionongeko ndi kugwetsedwa. 10Pakuti chikondi cha pandalama ndiwo muzu wa zoipa zonse; chimene ena pochikhumba, anachoka ku chikhulupiriro, nadzipyoza okha ndi zowawa zambiri. 11Koma iwe, munthu wa Mulungu2, thawa zinthu zimenezi, ndipo tsata kulungama, umulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiliro, chifatso. 12Limbana nako kulimbana kwabwino kwa chikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha, umene iwe wayitanidwako, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zochuluka. 13Ndikulamulira iwe pamaso pa Mulungu3 amene amasamalira zinthu zonse m’moyo, ndi Khristu Yesu amene anachitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato chivomerezo chabwino, 14kuti iwe usunge malamulo mopanda banga, molungama, kufikira kuonekera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu; 15kumene munthawi yake wodalitsika ndi Wolamulira yekhayo adzaonetsera, Mfumu ya iwo akulamulira, ndi Ambuye wa iwo akuonetsera umbuye; 16okhawo amene ali ndi umuyaya, okhala mkuwala kosasimbika; kumene munthu wina aliyense sanakuona, kapena akhoza kukuona; kwa iye kukhale ulemu ndi mphamvu yamuyaya. Amen.

17Lamulira iwo amene ali achuma nthawi yino kuti asakhale ndi malingaliro odzikuza, kapena kukhulupirira pa chuma chosadziwika mapezekedwe ake; koma mwa Mulungu4 amene amatikwanitsira ife tonse zinthu za chuma kuti tikondwere nazo; 18kuchita bwino, kulemera mu ntchito zabwino, kukhala wokondwa pogawira zinthu, kukhala wokonzeka kugawira nzeru ena [pa chuma chawo], 19kuziyalira okha maziko abwino amtsogolo, kuti iwo akagwiritsitse chimene chili moyodi.

20Iwe Timoteyo, sungitsa mokhulupirika zimene wapatsidwa, popewa kunyozetsa zopatulika, usalankhule zopanda pake, ndi kutsutsana ndi ziphunzitso zooneka za nzeru koma zili zabodza, 21 zimene ena pozivomereza anaphoya chikhulupirirocho. Chisomo chikhale ndi inu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu