Mutu 14

1Nthawi imeneyo Herode anamva za kutchuka kwa Yesu, 2ndipo ananena kwa antchito ake, Ameneyu ndi Yohane m’batizi: iye wauka kwa akufa, ndipo chifukwa cha chimenechi ntchito zimenezi za mphamvu zionekera molimba mwa iye. 3Pakuti Herode anamgwira Yohane. Ndipo anamumanga, ndipo anamuponya m’ndende pa chifukwa cha Herodiya mkazi wa Filipo ndi m’bale wake. 4Pakuti Yohane ananena kwa iye, sikoyenera kwa iwe kuti ukhale naye. 5Ndipo [pamene] anafunitsitsa kumupha iye, anaopa khamu la anthu, chifukwa anamuyesa iye mneneri. 6Koma pamene anali kukondwerera tsiku la kubadwa kwa Herode, mwana wa Herodiya anavina pamaso pawo, ndipo zinamkondweretsa Herode; 7pomwepo iye anamlonjeza ndi lumbiro kumpatsa iye kalikonse kamene adzapempha. 8Koma iye, pakupangiridwa ndi mayi wake, ananena, Ndipatseni ine mu chotengera mutu wa Yohane m’batizi. 9Ndipo mfumu inagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha lumbiro, komanso iwo amene anali pa gome limodzi ndi [iye], analamulira kuti [mutuwo] uperekedwe. 10Ndipo anatumiza anthu ndi kukadula mutu wa Yohane m’ndende; 11ndipo mutu unatengedwa mu chotengera, ndipo unaperekedwa kwa buthulo, ndipo anaunyamula [mutuwo] naupititsa kwa mayi wake. 12Ndipo ophunzira ake anabwera nanyamula thupi la Yohane ndi kukalikwilira, ndipo anabwera iwo namufotokozera Yesu.

13Ndipo Yesu, pakumva chimenechi, anachoka pa ngalawa napita ku chipululu kwa yekha. Ndipo makamu atamva [za chimenechi] anamulondola Iye wa pansi kuchokera ku mizinda. 14Ndipo pakutuluka anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anagwidwa chifundo ndi iwo, ndipo anachiritsa kufooka kwao. 15Koma pamene kunali madzulo, ophunzira ake anabwera kwa Iye nanena, Malo ano ndi a chipululu, ndipo [nthawi yochuluka] ya [tsiku] yapita kale; auzeni makamuwo anyamuke, kuti azipita kumidzi ndipo akazigulire okha chakudya. 16koma Yesu anati kwa iwo, Iwowa sakuyenera kupita: apatseni inuyo chakudya. 17Koma iwo anati kwa Iye, Ife tilibe kanthu kupatula mikate isanu ndi nsomba ziwiri. 18Ndipo Iye anati, bweretsani zimenezo kwa Ine. 19Ndipo atawalamulira makamu aja kuti akhale pa udzu, atatenga mikate isanu ndi nsomba ziwiri, Iye anayang’ana kumwamba, ndipo anadalitsa: ndipo atanyema mkate uja, Iye anapereka [mkatewo] kwa ophunzira ake, ndipo ophunzira [anapereka] kwa makamuwo. 20Ndipo onse anadya nakhuta, ndipo iwo anatolera makombo otsala ndipo anakwana mitanga khumi ndi iwiri yodzadza.

22Ndipo nthawi yomweyo Iye anakakamiza ophunzira kukakwera ngalawa, ndi kupita naye kutsidya lina, kufikira atauza makamu kuti achoke. 23Ndipo atawachotsa makamu aja, Iye anapita ku phiri kwa yekha kukapemphera. Ndipo pakufika madzulo, Iye anali yekha kumeneko, 24komatu ngalawa inali kale pakati pa nyanja ikuombedwa ndi mafunde, pakuti mphepo imaomba motsutsana ndi ngalawayo. 25komatu pakufika ulonda wa chinayi wa usiku Iye anapita kwa iwo, akuyenda panyanja. 26Ndipo ophunzira, pakuona Iye akuyenda panyanja, anasautsika, nanena, umenewu ndi mzukwa. Ndipo anafuula ndi mantha. 27Koma Yesu nthawi yomweyo analankhula kwa iwo, nanena, limbani mtima; ndine ndithu: musachite mantha. 28Ndipo Petro pakumuyankha Iye anati, Ambuye, ngatidi ndinu, ndilamulireni ine ndibwere kwa Inu pamadzipo. 29Ndipo anati, Bwera. Ndipo Petro, pakutsika m’ngalawa, anayenda pamadzi napita kwa Yesu. 30Koma pakuona mphepo ya mphamvu iye anachita mantha; ndipo pakuyamba kumira iye anafuula, nanena, Ambuye, ndipulumutseni ine. 31Ndipo pomwepo Yesu anatambasula dzanja lake namgwira iye, nanena naye, Iwe wachikhulupiriro chochepa, chifukwa chiyani ukukayikira? 32Ndipo iwo atapita kukalowa m’ngalawa, mphepo inaleka. 33Koma iwo amene anali m’ngalawa anafika namlambira Iye, nanena, Zoonadi inu ndinu Mwana wa Mulungu1.

34Ndipo atawoloka anafika ku malo wotchedwa Genesareti. 35Ndipo pamene anthu akumeneko anamzindikira Iye, anatumiza konse kudziko lozungulira, ndipo anabweretsa kwa iye onse amene anali odwala, 36ndipo anampempha iye kuti angokhudza mphonje ya chovala chake; ndipo onse amene anakhudza anachiritsidwa.

1Elohimu