Mutu 1

1Paulo ndi Silvano ndi Timoteyo kwa mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu1 Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. 2Chisomo kwa inu, ndi mtendere zochokera kwa Mulungu2 Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

3Ife tiyamika Mulungu3 nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera kutero, chifukwa chikhulupiliro chanu chichulukira kukula, ndipo chikondi chanu pa wina ndi mzake chimangilirika; 4chotero kuti ife eni tikhala onyadira mwa inu mu mipingo ya Mulungu4 chifukwa cha chipiliro chanu ndi chikhulupiliro m’mazunzo anu onse ndi masautso, zimene inu mukusungabe; 5chitsimikiziro cha chiweruzo cholungama cha Mulungu5, kuti kumapeto mukawerengedwe oyenera mu ufumu wa Mulungu6, umene inunso munazunzika nawo; 6ngati mwina ndi chinthu cholungama ndi Mulungu7 kubwezera chisautso kwa iwo akusautsa inu, 7ndipo kwa inu amene muli ovutika mukapumule ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu lochokera kumwamba, ndi angelo a mphamvu zake, 8m’lawi la moto kubwezera pa iwo amene samudziwa Mulungu8, ndi iwo amene samvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu Khristu; 9amene adzalipira chilango cha chionongeko chamuyaya kuchokera mkupezeka kwa Ambuye, ndi kuchokera ku ulemelero wa mphamvu yake, 10pamene adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwitsika mwa onse amene anakhulupilira, (pakuti umboni wathu kwa inu wakhulupiridwa,) m’tsiku limenelo. 11Kumapeto kwake ifenso tikupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu9 wathu akuwerengereni inu kukhala oyenera mayitanidwe, ndi kukwaniritsa kukoma konse kwa ubwino wake ndi ntchito ya chikhulupiliro ndi mphamvu, 12cholinga kuti dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu likalemekezedwe mwa inu ndi inu mwa iye, molingana ndi chisomo cha Mulungu10 wathu, ndi cha Ambuye Yesu Khristu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu