Mutu 14
1Ndipo kunachitika kuti mu Ikoniyo analowa pamodzi mu sunagoge ya Ayuda, ndipo analankhula kotero kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene onse anakhulupilira. 2Koma Ayuda amene sanakhulupilire anautsa mitima ya [iwo amene ali] a mitundu ndipo anawapangitsa [iwo] kukhala ndi malingaliro oipa pa abale. 3Iwo anakhala kumeneko kwa kanthawi, akulankhula molimba mtima, [nakhulupilira] mwa Ambuye, amene anaperekera umboni ku mau a chisomo chake, kupereka zizindikiro ndi zodabwitsa zochitika ndi manja awo. 4Ndipo khamu la mu mzindamo linagawanikana, ndipo ena anali ndi Ayuda ndi ena anali ndi atumwi. 5Ndipo pamene chinachitika chitonzo, onse [a iwo] amitundu ndi Ayuda ndi olamulira awo, anawachitira iwo choipa ndi kuwagenda,? 6iwo, pakumva ichi, anathawira ku mizinda ya Lukaoniya, Lustra ndi Derbe, ndi maiko ozungulira, 7ndipo iwo analalikira uthenga wabwino.
8Ndipo munthu wina mu Lustra, wolobodoka mapazi, anakhala pansi, [wokhala] wulumala kuchokera m’mimba mwa mayi wake, amene sanayendepo chiyambire. 9[Munthu] uyu anamumva Paulo akuyankhula, amene, pomupenyetsetsa iye chindunji ndi poona kuti anali ndi chikhulupiliro kuti achilitsidwa, 10anati ndi mau akulu, Imilira pa mapazo ako: ndipo iye anayimilira nayenda. 11Koma makamu, amene anaona zimene Paulo anachita, anakweza mau awo mu Lukaoniya, nanena, Milungu1, yokhala ngati anthu, yatsikira kwa ife. 12Ndipo iwo anayitana Barnaba Jupita, ndi Paulo Mekule, chifukwa anatsogolera m’kulankhula. 13Ndipo wansembe wa Jupita amene anali pamaso pa mzinda, pamene anabweretsa ng’ombe ndi maluwa ku chipata, anafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamuwo. 14Koma atumwiwo Barnaba ndi Paulo, pakumva [ichi], anag’amba zovala zawo, nathamangira ku khamulo, nafuula 15ndi kuti, Amuna inu, chifukwa chiyani mukuchita zinthu izi? Ifenso ndi anthu okhala ndi mkhalidwe ngati inu, tilalikira kwa inu kubwerera ku zoipa kupita kwa Mulungu2 wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi zonse zopezeka m’menemo; 16amene mu m’badwo wakale analekerera mitundu yonse kuyenda njira zawo, 17ngakhaledi kuti Iye sanadzisiyira wopanda mboni, kuchita zabwino, ndi kupereka kwa inu kuchokera kumwamba mvula ndi chipatso cha mnyengo yake, kudzadza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo. 18Ndipo ponena zinthu izi, movutikira iwo analetsa makamuwo kuti asapereke nsembe kwa iwo. 19Koma panabwera Ayuda wochokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo, ndipo anakopa makamuwo ndi kumgenda Paulo, namduduluzira kunja kwa mzindawo, poyesa kuti iye wafa. 20Koma pamene ophunzira anamzungulira iye, anadzuka nalowa mu mzindawo. Ndipo m’mawa mwake iye pamodzi ndi Barnaba anapita ku Derbe. 21Ndipo atalalikira Uthenga Wabwino ku mzinda umenewo, ndi kupanga ophunzira ambiri, iwo anabwerera ku Lustra, ndi Ikoniyo, ndi Antiokeya, 22pokhazikitsa miyoyo ya ophunzira, kuwalimbikitsa iwo kukhazikika mu chikhulupiliro, kuti kudzera m’mazunzo tikalowe mu ufumu wa Mulungu3. 23Ndipo pamene anawasankhira iwo akulu a mpingo, atapemphera ndi kusala chakudya, anawapereka iwo kwa Ambuye, amene iwo anamkhulupilira. 24Ndipo pamene anadutsa ku Pasidiya anafika ku Pamfuliya, 25ndipo atalankhula mau mu Perge, iwo anafika ku Ataliya; 26ndipo kuchokera kumeneko iwo anakwera ngalawa kupita ku Antiokeya, kumene anadzipereka ku chisomo cha Mulungu4 pa ntchito imene iwo anayikwaniritsa. 27Ndipo atafika kumeneko, ndi kusonkhanitsa pamodzi mpingo, anawafotokozera iwo zonse zimene Mulungu5 anachita ndi iwo, ndi kuti Iye anatsegula khomo la chikhulupiliro kwa amitundu. 28Ndipo iwo sanakhale nthawi yochepa ndi ophunzirawo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu