Mutu 8

1[Palibe tsopano] pamenepo kutsutsika kwa iwo amene ali mwa Khristu Yesu.2Pakuti lamulo la Mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu landimasula ine kuchoka ku lamulo la tchimo ndi imfa.3Pakuti chimene lamulo silikanatha kuchita, m’menemo linali lofooka mwa thupi, Mulungu1, anatumiza Mwana wake yemwe, m’chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, anatsutsa tchimo m’thupi,4cholinga kuti kufunikira kwa kulungama kwa lamulo kukwaniritsidwe mwa ife, amene sitiyenda monga mwa thupi koma monga mwa Mzimu.5Pakuti iwo akukhala monga mwa thupi amasamalira zinthu za thupi; ndipo iwo okhala monga mwa Mzimu, asamalira zinthu za Mzimu.6Pakuti malingaliro a thupi [ndiwo] imfa; koma malingaliro a Mzimu ndiwo moyo ndi mtendere.7Chifukwa malingaliro a thupi ndi mdani wotsutsana ndi Mulungu2: pakuti samagonjera ku lamulo la Mulungu3; pakuti sakhoza kutero:8ndipo iwo amene ali m’thupi sangasangalatse Mulungu4.9Koma inu simuli m’thupi koma mu Mzimu, pokhapokha ngatidi Mzimu wa Mulungu5 akhalira mwa inu; koma ngati wina wa inu alibe Mzimu wa Khristu sakhala mwa Iye:10koma ngati Khristu akhala mwa inu, thupi lanu ndi lakufa pa nkhani ya uchimo, koma Mzimu akhala ndi moyo pa nkhani ya kulungama.11Koma ngati Mzimu wa Iye amene anamuukitsa Yesu kwa akufa akhalira mwa inu, Iye amene anamuukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa pa chifukwa cha Mzimu wake amene akhalira mwa inu.12Choncho pamenepo, abale, ndife amangawa, osati ku thupi, kukhala monga mwa thupi;13pakuti ngati mukhala monga Mzimu, mufetse machitachita a thupi, mudzakhala ndi moyo:14pakuti ambiri amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu6, amenewa ali ana a Mulungu7.15Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuti mukachite mantha, koma munalandira mzimu wa umwana, umene timafuula Abba, Atate.16Mzimu mwini yekha achitira umboni ndi mzimu wathu, kuti ndife ana a Mulungu8.17Ndipo ngati ana, olowanso m’malo: olowa m’malo a Mulungu9, ndi olowa amzake a Khristu; ngatidi timva zowawa pamodzi ndi [Iye], kuti ife tikalandirenso ulemelero pamodzi ndi [Iye].

18Pakuti ine ndiyesa zowawa za nthawi yino zosayenera [kufanizira] ndi ulemelero ukubwera umene udzavumbulutsidwa kwa ife.19Pakuti chiyembekezo cha cholengedwa chikulindira vumbulutso la ana a Mulungu10:20pakuti chilengedwe chagonjetsedwa ku zopanda pake, osati ku cholinga chake, koma pa chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, m’chiyembekezo21kuti cholengedwacho pochokha chikamasulidwenso ku ukapolo wa chivundi kupita ku ufulu wa ulemelero wa ana a Mulungu11.22Pakuti ife tidziwa kuti chilengedwe chonse chibuula pamodzi ndi kumva zowawa pamodzi kufikira pano.23Ndipo osati chimenecho chokha, koma ife tokha, amene tili nazo zipatso zoyambilira za Mzimu, ifenso pa ife tokha tibuula mkati mwathu, kudikilira umwana wathu, [ndiwo] chiombolo cha thupi lathu.24Pakuti ife tinapulumutsidwa m’chiyembekezo, pakuti chimene aliyense achipenya, achiyembekezeranso bwanji?25Koma ngati chimene sitichiona timachiyembekezera, timachilindilira m’chipiliro.26Ndipo chomwechonso Mzimu amakhala nafe natithandiza ku zofooka zathu; pakuti ife sitidziwa chimene tikuyenera kupempherera monga chiyenera, koma Mzimu mwini atipembedzera ndi zobuula zosaneneka.27Koma Iye amene asanthula mitima adziwa malingaliro a Mzimu, chifukwa apembedzera oyera mtima molingana kwa Mulungu12.28Koma ife tidziwa kuti zinthu zonse zichitira ubwino kwa iwo omukonda Mulungu13, kwa iwo oyitanidwa kulinga ku cholinga.29Chifukwa iwo amene Iye anawadziwiratu, anawayikiratunso kukhala ofanana ndi chifanizo cha Mwana wake, kotero kuti akakhale oyamba kubadwa pakati pa abale ambiri.30Koma iwo amene anawayikiratu, amenewanso Iye anawayitana; ndipo iwo amene Iye anawayitana, amenewanso anawalungamitsa; koma iwo amene anawalungamitsa, amenewanso anawapatsa ulemelero.

31Nanga tidzanena chiyani pamenepo ku zinthu izi? Ngati Mulungu14 [akhala] ndi ife, ndani amene adzatsutsana nafe?32Iye amene, sanatimane Mwana wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranjinso ndi Iye kutipatsa ife zinthu zonse?33Ndani adzaneneza wosankhidwa wa Mulungu15? [ndi] Mulungu16 amene amalungamitsa:34ndani amene amatsutsa? [ndi] Khristu amene anafa, koma anaukanso; amenenso ali kudzanja lamanja la Mulungu17; amenenso akutipembedzera ife.35Ndani adzatilekanitsa ife ku chikondi cha Khristu? Nsautso kapena kupsinjika mtima kodi, kapena kuzunza, kapena chilala, kapena usiwa, kapena zoopsa, kapena lupanga kodi?36Molingana ndi momwe kunalembedwera, chifukwa cha inu tikuphedwa tsiku lonse; ife tatengedwa ngati nkhosa zokaphedwa.37Koma mu zinthu zonse izi tili oposa agonjetsi mwa Iye amene atikonda ife.38Pakuti ndatsimikizika mtima kuti ngakhale imfa, kapena moyo, kapena angelo, kapena maukulu, kapena zinthu zimene zili nkudza, kapena zimphamvu,39kapena kutalika, kapena kuya, kapena cholengedwa chilichonse, sichingatilekanitse ku chikondi cha Mulungu18, chimene chili mwa Khristu Ambuye wathu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu>6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu>11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu>16Elohimu17Elohimu18Elohimu