Mutu 4
1?Zichokera kuti nkhondo ndipo zichokera kuti zolimbana pakati panu? Sizichokera kodi, — m’zikhumbitso zanu, zimene zimachita nkhondo m’ziwalo zanu? 2Mulakalaka ndipo mulibe: mumapha ndipo mwadzala ndi nsanje, ndipo simungazipeze; mulimbana ndi kuchita nkhondo; mulibe chifukwa simupempha. 3Mupempha ndipo simulandira, chifukwa mumapempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu. 4Akazi achigololo inu, simudziwa kuti ubwenzi ndi dziko lapansi ndi udani ndi Mulungu1? Pamenepo iye amene alingalira kukhala bwenzi la dziko lapansi akuzikhazika kukhala mdani wa Mulungu2. 5Mukuganiza kuti malemba analankhula m’dela? Kodi Mzimu amene anamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje? 6Koma iye apereka chisomo chochuluka. Pamenepo malemba anena, Mulungu3 akaniza odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa. 7Ziperekeni nokha pamenepo kwa Mulungu. Mkanizeni mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. 8Yandikirani kwa Mulungu4, ndipo iye adzayandikira chifupi ndi inu. Sambani m’manja [mwanu], ochimwa inu, ndipo yeretsani mitima yanu, inu a malingaliro a pawiri. 9Mukhale ndi tsoka, ndi kubuma, ndi kulira: kuseka kwanu kusanduke kubuma, ndipo chimwemwe [chanu] kulemedwa. 10Dzichepetseni nokha pamaso pa Ambuye, ndipo iye adzakukwezani inu.
11Musalankhulirane zoipa wina ndi mzake, abale. Iye amene alankhula zoipa kwa m’bale wake, kapena kumuweruza m’bale wake, alankhula motsutsana ndi lamulo ndipo aweruza lamulolo. Koma ngati muweruza lamulo, simuli akuchita lamulo, koma woweruza. 12M’modzi ndiye wopereka lamulo ndi kuweruza, amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga: koma ndiwe ndani wakuweruza mzako?
13Pita uko tsopano, iwe amene umati, Lero kapena mawa ndizapita ku mzinda wakuti ndi kukhalako kwa chaka kumeneko, ndipo ndidzayenda ndi kubwerako, 14iwe amene sudziwa zochitika mawa, ([pakuti] moyo wako [uli] wotani? Uli ngati mpweya, uwonekera kanthawi kochepa, ndipo kenako usowa,) 15m’malo mwake udzilankhula, Ngati Ambuye alola [kotero] ndipo tikakhala ndi moyo, tipanganso ichi kapena icho. 16Koma tsopano mudzitamandira m’kudzikuza kwanu: kudzitamandira konse kotere ndi koipa. 17 Kwa iye pamenepo wakudziwa kuchita chabwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu