Mutu 12
1Ndipo Iye anayamba kunena kwa iwo m’mafanizo, Munthu analima munda wa mpesa, ndipo anamangira mpanda kuzungulira mundawo nakumba moponderamo mpesa, namanga nsanja, ndipo anaubwereketsa kwa olima munda, nachokako ku dzikolo. 2Ndipo anatumiza kapolo kwa olima mundawo munyengo yake, kuti akalandire kuchokera kwa olima mundawo chipatso cha m’munda wa mpesawo. 3Koma iwo anamtenga iye, ndipo anam’menya, ndi kumchotsa wopanda kanthu. 4Ndipo iye anatumanso kwa iwo kapolo wina; ndipo [kwa] iye [anamgenda miyala, ndi] kum’menya m’mutu, namchotsa [iye] ndi mau achipongwe. 5Ndipo [anatumanso] iye wina, ndipo ameneyu iwo anamupha; ndi ena ambiri, kumenyedwa ndi enanso kuphedwa. 6Pokhala naye mwana wake wamwamuna wokondedwa, anamtumanso iye kwa iwo potsiriza, nanena, Iwowa akamchitira ulemu mwana wanga. 7Komatu olima m’munda aja ananena kwa wina ndi mzake, uyu ndiye wolowa m’malo: bwerani, tiyeni timuphe iye ndipo cholowacho chidzakhala chathu. 8Ndipo anamtenga iye namupha, ndipo anamponya kunja kwa munda wa mpesa. 9Kodi pamenepo mbuye wa munda wa mpesawo adzachita chiyani? Adzabwera nadzawononga olima m’munda aja, ndipo adzaupereka mundawo kwa ena. 10Kodi simunawerengeko malemba awa, Mwala umene m’misiri womanga nyumba anaukana, umenewu wasanduka mwala wa pangodya: 11chimenechi ndi cha Ambuye, ndipo ndi chodabwitsa m’maso mwathu? 12Ndipo iwo anafuna kumgwira Iye, ndipo anaopa khamulo; pakuti iwo anadziwa kuti Iye analankhula fanizoli mowatsutsa. Ndipo iwo anamsiya Iye.
13Ndipo anatumiza kwa Iye ena mwa Afalisi ndi Aherode, kuti akamkole Iye nkulankhula kwake. 14Ndipo iwo anabwera nati kwa Iye, Mphunzitsi, ife timadziwa kuti ndinu woona, ndipo simusamala za munthu wina aliyense, koma muphunzitsa njira ya Mulungu1 mu choonadi: Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15Tikuyenera kupereka, kapena tisapereke? Koma Iye podziwa chinyengo chawo anati kwa iwo, Chifukwa chiyani mukundiyesa? Bweretsani rupiya la theka kuti ndiliwone. 16Ndipo iwo analibweretsa. Ndipo anati kwa iwo, Kodi chithunzithunzi ndi chilembo ichi ndi za ndani? Ndipo iwo anati kwa Iye, Za Kaisara. 17Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Perekani za Kaisara kwa Kaisara, ndipo zimene zili za Mulungu2 kwa Mulungu3. Ndipo iwo anadabwa naye.
18Ndipo Asaduki anabwera kwa Iye, amene ankati kulibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye nanena, 19Mphunzitsi, Mose analembera kwa ife kuti ngati wina m’bale wake wamwalira, nasiya mkazi, ndipo sanasiye ana, pamenepo m’bale wake amutenge mkaziyo, naukitse mbeu kwa m’bale wakeyo. 20Analipo abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anatenga mkazi, ndipo pakumwalira sanasiye mbewu; 21ndipo wachiwiri anamutenga namwalira, ndipo nayenso sanasiye mbewu; ndipo chimodzimodzinso wachitatu. 22Ndipo asanu ndi awiriwo [anamutenga iye ndipo] sanasiye mbewu. Kumapeto kwake mkaziyunso anamwalira. 23Pakuuka, pamene adzaukanso, ndani wa iwo adzakhala mkazi wake, pakuti onse asanu ndi awiri anamuyesa mkazi wao? 24Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Kotero musasokonekere inu, posadziwa malemba, kapena mphamvu ya Mulungu4? 25Pakuti iwo pakuuka kwa akufa sakwatira kapenanso kukwatiwa, koma akhala ngati angelo [amene ali] kumwamba. 26Koma zokhudza akufa kuti adzauka, simunawerenge m’buku la Mose, mu [gawo la] chitsamba, m’mene Mulungu5 analankhulira kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu6 wa Abrahamu, ndi Mulungu7 wa Isake, ndi Mulungu8 wa Yakobo? 27Iye si Mulungu9 wa akufa, koma wa amoyo. Inutu mukulakwitsa kwambiri.
28Ndipo m’modzi wa alembi amene anabwera, ndipo anawamva iwo akukambirana pamodzi, kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Kodi lamulo loyamba pa onse ndi liti? 29Ndipo Yesu anamuyakha iye, Lamulo loyamba pa onse ndi [ili], Mvera Israyeli: Ambuye Mulungu10 wathu ndiye Ambuye m’modzi; 30ndipo uzikonda Ambuye Mulungu11 wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse. Limeneli ndilo lamulo loyamba. 31Ndipo lachiwiri lofanana nalo [ndi] ili: Uzikonda mzako monga uzikonda iwe mwini. Palibe lamulo lina lalikulu kuposa awa. 32Ndipo alembi anati kwa Iye, Chabwino, mphunzitsi; mwalankhula molingana ndi choonadi. Pakuti alipo m’modzi, ndipo palibe wina pambali pa Iyeyu; 33ndipo kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru zonse, ndi moyo wonse, ndi mphamvu zonse, ndi kumkonda mzako monga uzikonda iwe mwini, ndiko koposa nsembe zopsereza ndi nsembe zophedwa. 34Ndipo Yesu, poona kuti wayankha mwa nzeru, anati kwa iye, Suli kutali ndi ufumu wa Mulungu12. Ndipo palibe amene anayerekeza kumfunsanso Iye.
35Ndipo Yesu poyankha anati [pamene Iye anali] kuphunzitsa m’kachisi, Nanga bwanji alembi amati Khristu ndi mwana wa Davide? 36[pakuti] Davide mwini yekha anati [pakuyankhula] mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditayika adani ako [ngati] popondapo mapazi ako. 37Davide mwini yekha [pamenepo] anamutchula Iye Ambuye, ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo khamu lalikulu linamumvetsera Iye mokondwera.
38Ndipo Iye anati kwa iwo m’chiphunzitso chake, Chenjerani ndi alembi, amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo yaitali, ndi kulonjeredwa m’misika, 39ndi kukhala malo aulemu ku maphwando; 40amene alusira nyumba za akazi a masiye, ndipo monga mwa chiphiphiritso apemphera mapemphero ataliatali. Amenewa adzalandira chiweruzo choopsya.
41Ndipo Yesu, pokhala pansi moyang’anana ndi mosungiramo chuma, anaonerera momwe anthu amaperekera ndalama mosungiramo chuma; ndipo olemera ambiri anaponyamo zochuluka. 42Ndipo mkazi wa masiye anadza napereka tindalama tiwiri, timene tinali tochepa kwambiri. 43Ndipo pakuitana ophunzira ake anati kwa iwo, Ndithudi ndinena kwa inu, Mkazi wa masiye uyu wapereka koposa onse amene apereka mosungira chuma: 44pakuti onsewa apereka mwa zimene iwo anali nazo zochuluka, koma iyeyu monga mwa kusowa kwake wapereka zonse zimene anali nazo, za moyo wake wonse.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu