Mutu 5
1Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba yathu ya msasa ya dziko lapansi iwonongedwa, tili nayo nyumba kuchokera kwa 1Mulungu, nyumba osati yomangidwa ndi manja, yamuyaya m’mwambamo. 2Pakutidi tibuula ife m’menemo, kufunitsitsa kukhalamo mnyumba yathu imene ili yochokera kumwamba; 3ngatidi tikhalanso wovekedwa sitidzapezeka a maliseche. 4Pakuti ngatidi ife amene tili mu msasa tibuula, kukhala opsinjika; pamene ife sitifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chimene chili chakufacho chikamezedwe ndi moyo. 5Tsopano iye amene ali wotikonzera chinthu chimenechi [ndi] 2Mulungu, amenenso wapereka kwa ife chikole cha Mzimu. 6Pamenepo ife tili nako kulimba mtimba nthawi zonse, ndipo tidziwa kuti pamene tili opezeka m’thupi tili osapezeka pa Ambuye, 7(pakuti tiyenda mwa chikhulupiliro, osati mwa maonekedwe;) 8ife tili nako kulimbika, ndinena, ndipo ndikondwera kukhala wosapezeka m’thupi ndi kukhala wopezeka ndi Ambuye. 9Pameneponso ife tifunitsitsa, kaya m’zopezeka kapena m’zobisika, kukhala womkondweretsa Iye. 10Pakuti ife tikuyenera kuonetsedwa pa mpando wa chiweruzo wa Khristu, kuti aliyense akalandire zinthu [zochitika] mthupi, molingana ndi zomwe iye anachita, kaya ndi zabwino kapena zoipa. 11Pamenepo podziwa kuopsa kwa Ambuye tikopa anthu, koma awonetsedwa kwa 3Mulungu, ndipo ine ndiyembekezanso kuti taonetsedwa m’chikumbumtima chanu. 12[Pakuti] ife sitidzionetsera tokha kwa inu, koma tikupatsani inu cholinga cha kudzitamandira kwathu m’malo mwathu, kuti mukakhale nako kanthu kotsutsana nawo iwo odzitamandira okha poyera, ndipo osati mu mtima. 13Pakuti ngati tili oyaluka tokha, titero kwa 4Mulungu; kapena tikhala a nzeru zathu, [zili] kwa inu. 14Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza ife, popeza taweruza motere: kuti m’modzi anafera tonse, pamenepo onse anafa; 15ndipo Iye anafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakakhale ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene anawafera ndipo anaukitsidwa. 16Kotero kuti ife tisadziwe wina aliyense monga mwa thupi; koma ngakhale kuti tamudziwa Khristu molingana ndi thupi, komabe tsopano sitimzindikiranso monga motero. 17Chomwecho ngati wina akhala mwa Khristu, ali wolengedwa kwatsopano; zakale zapita; taonani zinthu zonse zakhala zatsopano: 18ndipo zinthu zonse ndi za 5Mulungu amene watiyanjanitsa ife kwa Iye yekha mwa [Yesu] Khristu, ndipo kwapatsidwa kwa ife utumiki wa chiyanjanitso: 19m’mene 6Mulungu anali mwa Khristu, kuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawerengera zolakwa zawo; ndi kuyika mwa ife mau a chiyanjanitso. 20Ifeyo pamenepo ndife akazembe a Khristu, monga ngati 7Mulungu akudandaulira ife, monga Khristu, yanjanitsidwani kwa 8Mulungu. 21Iye amene sanachimwe anakhala wochimwa m’malo mwathu, kuti ife tikakhale wolungama kwa 9Mulungu mwa Iye.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu