Mutu 15

1Ndipo anthu ena, pamene amatsika kuchokera ku Yudeya, anawaphunzitsa abale, Ngati simunadulidwe molingana ndi mwambo wa Mose, simudzapulumuka. 2Pomwepo kutsutsana kunabuka, ndipo panalibe zokambirana ndi pang’ono pomwe zimene zinachitika kumbali ya Paulo ndi Barnaba zotsutsana nawo, komatu iwo anapanga chikonzero kuti Paulo ndi Barnaba, ndi ena ochokera pakati pawo, apite ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu zokhudza funso limeneli. 3Pamenepo iwo atatumidwa ndi mpingo, anadutsira ku Foinike ndi Samariya, nafotokoza za kutembenuka mtima kwa [iwo amene] anali amitundu. Ndipo iwo anabweretsa chisangalalo pakati pa abale. 4Ndipo pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi mpingo, ndi atumwi, ndi akulu, ndipo anafotokoza zonse zimene Mulungu1 anachita nawo. 5Ndipo ena mwa iwo amene anali a gulu la Afarisi, amene anakhulupilira, anauka pakati [pawo], nanena kuti akuyenera kuti awadule iwo ndi kuwakakamiza kusunga lamulo la Mose. 6Ndipo atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuona za nkhani imeneyi. 7Ndipo zokambirana zazikulu zitachitika, Petro, anayimilira, nati kwa iwo, Abale, inu mukudziwa kuti kuyambira pa chiyambi Mulungu2 anasankha pakati panu kuti amitundu ndi pakamwa panga adamva mau a uthenga wabwino ndi kukhulupilira. 8Ndipo Mulungu3 wodziwa za mumtima anawachitira iwo umboni, nawapatsa [iwo] Mzimu Woyera monganso kwa ife, 9ndipo sanayike kusiyana pakati pa ife ndi iwo, atawayeretsa mitima yawo mwa chikhulupiliro. 10Pamenepo tsopano chifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu4, poyika goli pakhosi la ophunzira, limene makolo athu ngakhale ifeyo sitinakwanitse kulisenza? 11Koma timakhulupilira kuti ife tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu, monga iwonso munjira yomweyo. 12Ndipo khamu lonse linakhala chete ndi kumvera Barnaba ndi Paulo akufotokozera zizindikiro zonse ndi zodabwitsa zimene Mulungu5 anachita pakati pa amitundu mwa iwo. 13Ndipo pamene iwo anakhala bata, Yakobo anayankha, nati, abale, tandimverani: 14Simoni wafotokozera m’mene Mulungu6 poyamba anayendera ndi kutulutsa amitundu kukhala anthu otchedwa dzina lake. 15Ndipo mwa ichi zivomerezana ndi mau a aneneri; monga analembedwa: 16Zikazapita zinthu izi, ndidzabweranso, ndipo ndidzamanganso chihema cha Davide chimene chinagwa, ndipo ndidzamanganso bwinja lake, ndipo ndizalidzutsa, 17kotero kuti anthu otsalira amfunefune Ambuye, ndi mitundu yonse imene dzina langa limatchulidwa, atero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi 18zodziwika kwamuyaya. 19Pamenepo Ine ndiweruza, osati kuti ndivutitse iwo wochokera kwa amitundu atembenukira kwa Mulungu7; 20koma kuwalembera kuti apewe kuzidetsa ku mafano, ku chigololo, komanso ku zimene zili zopotola, ndi za mwazi. 21Pakuti Mose, kuchokera ku mibadwo yakale, anali nawo m’mizinda yonse iwo amene amalalikira iye, nawerengedwa m’masunagoge la sabata lililonse.

22Pamenepo zinaoneka zabwino kwa atumwi ndi akulu, ndi mpingo onse, kutumiza amuna osankhidwa pakati pawo ndi Paulo ndi Barnaba ku Antiokeya, Yuda wotchedwa Barsaba ndi Sila, kutsogolera amuna pakati pa abale, 23atatenga zolembedwa ndi manja awo [kuti]: Atumwi, ndi akulu, ndi abale, kwa abale amene ali ochokera pakati pa amitundu ku Antiokeya, ndi [mu] Siriya ndi Kilikiya, tikulonjerani: 24Popeza monga tamva kuti ena anatuluka pakati pathu ndi kukuvutani inu ndi mau, kusokoneza miyoyo yanu, [kunena kuti mukuyenera kudulidwa ndi kusunga lamulo]; kumene ife sitinapereke lamulo; 25chinaoneka chabwino kwa ife, kubwera ndi lingaliro lofanana, kutumiza amuna awa kwa inu ndi m’bale wathu Barnaba ndi Paulo, 26amuna amene anapereka miyoyo yawo pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu. 27Kotero ife tatumiza Yuda ndi Sila, amenenso mwa iwo okha akuuzani mau [a pakamwa] zinthu zomwezi. 28Pakuti zaoneka zabwino kwa Mzimu Woyera ndi kwa ife kuti tisakuyikireni goli lalikulu kuposera zinthu zofunikazi: 29kusakhudza zinthu zimene zaperekedwa nsembe kwa mafano, ndi za magazi, komanso zimene zapotoledwa, ndi chigololo; kuzisunga nokha ku zimene mungathe kuchita bwino. Tsalani bwino. 30Pamenepo iwo, anawalola kuti apite, nafika ku Antiokeya, ndipo atasonkhanitsa khamulo anapereka kwa [iwo] kalatayo. 31Ndipo atayiwerenga, iwo anasangalala ndi chitonthozocho. 32Ndipo Yuda ndi Sila, iwonso pokhala aneneri, anawasangalatsa abalewo ndi mau ambiri, nawalimbikitsa iwo. 33Ndipo pamene anakhala nthawi [kumeneko], anawalola iwo kuti apite mu mtendere kuchokera kwa abale amene anawatumako. 35Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhalira ku Antiokeya, kuphunzitsa ndi kulalikira uthenga wabwino, mau a Ambuye, ndi ena ambirinso.

36Koma atapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, Tiyeni tibwerere tsopano ndi kuwayendera abale m’mizinda yonse imene talalikira mau a Ambuye, [ndi kuona] kuti akukhala motani. 37Ndipo Barnaba anafuna kutenganso Yohane, wotchedwa Marko; 38koma Paulo anaganiza kuti sikwabwino kumutenga iye amene anawasiya iwo, [nabwerera] kuchoka ku Pamfuliya, ndipo sanapite nawo kukatumikira. 39Pamenepo panabuka kutsutsana kwakukulu, kotero kuti anasiyana wina ndi mzake; ndipo Barnaba anatengana ndi Marko nayenda pa ngalawa kupita ku Kupro; 40koma Paulo anasankha Sila napita, naikizidwa ndi abale ku chisomo cha Mulungu8. 41Ndipo iye anadutsira ku Siriya ndi ku Kilikiya, nakhazikitsa mipingo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu