Mutu 6

1Zitapita zinthu izi Yesu anapita kutsidya la nyanja ya Galileya [kapena kuti] ya Tiberiya, 2ndipo khamu lalikulu linamutsatira Iye, chifukwa iwo anaona zizindikiro zimene Iye anachita pa odwala. 3Ndipo Yesu anakwera kupita ku phiri, ndipo kumeneko anakhala pansi pamodzi ndi ophunzira ake: 4koma pasaka, phwando la Ayuda linawandikira. 5Pamenepo Yesu, pokweza maso ake naona khamu lalikulu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, Kodi tikagula kuti mikate kuti anthu awa adye? 6Komatu analankhula izi kumuyesa iye, pakuti anadziwa chimene adzachita. 7Filipo anamyankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siokwanira kwa iwo, kuti aliyense atengeko [gawo] pang’ono. 8M’modzi wa ophunzira ake, Andreya, m’bale wake wa Simoni, anati kwa Iye, 9Pali mnyamata pano amene ali ndi mikate isanu ya barele ndi nsomba ziwiri; koma izi, ndi chiyani ku unyinjiwu? 10 [Ndipo] Yesu anati, Akhalitseni pansi. Tsopano panali udzu ochuluka pamalopo: pamenepo amuna anakhala pansi, chiwerengero chao chokwanira pafupifupi zikwi zisanu. 11Ndipo Yesu anatenga mikateyo, ndipo atayamika, anaigawa [iyo] kwa iwo amene anakhala pansi; ndipo chimodzimodzinso nsomba zija monga iwo anafuna. 12Ndipo pamene iwo anakhuta, anati kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani pamodzi makombo amene ali ponsepo, kuti kasatayike kanthu. 13Iwo anasonkhanitsa makombowo pamodzi, ndipo anadzadza mitanga khumi ndi iwiri ya makombo a mikate isanu, amene anali ponsepo kwa iwo amene anadya. 14Pamenepo amuna aja, pakuona chizindikiro chimene Yesu anachita, anati, Uyudi ndi mneneri amene akubwera m’dziko lapansi. 15Pamenepo Yesu pakudziwa kuti iwo akubwera kudzamugwira, kuti amulonge ufumu, anachoka napita ku phiri kwa yekha.

16Koma pamene madzulo anafika, ophunzira ake anatsikira kunyanja, 17ndipo pamene analowa m’ngalawa, iwo anaoloka nyanja kupita ku Kapernao. Ndipo mdima unayambapo, ndipo Yesu sanabwere kwa iwo, 18ndipo nyanja inawinduka ndi mphepo ya mkuntho imene imaomba. 19Atapalasa pamenepo monga ma stadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, iwo anamuona Yesu akuyenda pa nyanja ndipo amabwera kufupi ndi ngalawayo; ndipo iwo anachita mantha. 20Koma Iye anati kwa iwo, Ndine amene: musachite mantha. 21Iwo anali ofunitsitsa pamenepo kumulandira m’ngalawa; ndipo nthawi yomweyo ngalawa inali kumtunda kumene iwo amapita.

22M’mawa mwake khamu limene linayima mbali ina ya nyanja, pakuona kuti panalibe ngalawa ina yaing’ono pamenepo kupatula imene ophunzira ake anakwera, ndi kuti Yesu sanapite ndi ophunzira ake m’ngalawa, koma [kuti] ophunzira ake anapita okha; 23 (koma ngalawa zina zing’onozing’ono zochokera ku Tiberiya zinafika pafupi ndi pamalo pamene iwo anadya mkate Ambuye atayamika;) 24pamene khamulo linaona kuti Yesu sali pamenepo, ngakhale ophunzira ake, anakwera m’ngalawa, nafika ku Karpenao, kufunafuna Yesu. 25Ndipo pamene anamupeza mbali ina ya nyanja, anati kwa Iye, Rabi, mwafika kuno liti? 26Yesu anawayankha iwo nanena, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, simukundifuna ine chifukwa chakuti munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mikate ija ndi kukhuta. 27Musagwire ntchito [pa] chakudya chimene chimaonongeka, koma [pa] chakudya chimene chikukhalitsani m’moyo wosatha, chimene Mwana wa munthu adzakupatsani inu; pakuti pa Iye Atate anasindikiza chizindikiro, [ndiye] Mulungu1. 28Pamenepo iwo anati kwa Iye, Tichite chiyani kuti tikagwire ntchito za Mulungu2? 29Yesu anayankha nati kwa iwo, Iyi ndi ntchito ya Mulungu3, kuti mukakhulupilire Iye amene anamtuma. 30Pamenepo iwo anati kwa Iye, Chizindikiro chanji chimene ife tingaone ndi kukhulupilira Inu? Muchita chiyani? 31Makolo athu anadya mana m’chipululu, monga kunalembedwa, Iye anawapatsa mkate wochoka kumwamba kuti adye. 32Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wochokera kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate weniweni wochokera kumwamba. 33Pakuti mkate wa Mulungu4 ali Iye amene atsika kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo kudziko lapansi. 34Kotero iwo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni mkate umenewu nthawi zonse. 35 [Ndipo] Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wa moyo: iye wobwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye wokhulupilira pa Ine sadzamva ludzu nthawi iliyonse. 36Koma Ine ndanena kwa inu, kuti mwandionanso Ine ndipo simukhulupilira. 37Zonse zimene Atate andipatsa Ine zidzabwera kwa Ine, ndipo iye wobwera kwa Ine sindidzamtaya konse kunja. 38Pakuti Ine ndatsika kuchokera kumwamba, osati kuti ndidzachite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine. 39Ndipo chimenechi ndi chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, kuti pa zonse zimene Iye wandipatsa ndisatayeko kanthu, koma ndikachiukitse m’tsiku lotsiriza. 40Pakuti ichi ndi chifuniro cha Atate wanga, kuti aliyense wakuona Mwana, ndi kukhulupilira pa Iye, akhale nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa patsiku lomaliza. 41Ayuda pamenepo anang’ung’uza za Iye, pakuti anati, Ndine mkate umene watsika kuchokera kumwamba. 42Ndipo iwo anati, Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene atate wake ndi mayi wake tiwadziwa? Nanga bwanji akunena, Ine ndatsika kuchokera kumwamba? 43Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang’ung’uze pakati panu. 44Palibe akhoza kubwera kwa Ine pokhapokha Atate amene anandituma amkokere kwa Ine, ndipo ndidzamuukitsa patsiku lomaliza. 45Chinalembedwa mwa mneneri, Ndipo iwo adzaphunzitsidwa za Mulungu5. Aliyense amene wamva kuchokera kwa Atate [mwini], ndipo waphunzira [za Iye], adza kwa Ine; 46osati kuti aliyense anaona Atate, kupatula Iye amene ali wa Mulungu6, waona Atate. 47Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, Iye wokhulupilira [pa Ine] ali nawo moyo wosatha. 48Ine ndine mkate wa moyo. 49Makolo anu anadya mana m’chipululu ndipo anafa. 50Ameneyu ndi mkate umene uchokera kumwamba, kuti wina akadyeko ndipo sadzafa. 51Ine ndine mkate wa moyo umene watsika kuchokera kumwamba: ndipo ngati wina akadya mkate umenewu adzakhala ndi moyo nthawi zonse; komatu mkate umene ndidzapatsa inu ndilo thupi langa, limene ndidzapereka likhale moyo wadziko lapansi. 52Ayuda pamenepo anatsutsana pakati pawo, nanena, Kodi adzatipatsa bwanji thupi lake kuti tidye? 53Yesu pamenepo anati kwa iwo, Zoonadi, zoonadi, ndinena kwa inu, pokhapokha ngati mudzadya thupi la Mwana wa munthu, ndi kumwera magazi ake, mulibe moyo mwa inu nokha. 54Iye amene akadya thupi langa ndi kumwera magazi anga ali nawo moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa patsiku lomaliza: 55pakuti thupi langa ndi chakudyadi ndi magazi anga chakumwadi. 56Iye wakudya thupi langa ndi kumwa magazi anga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye. 57Monga Atate wanga wamoyo wandituma Ine ndipo ndikhala ndi moyo chifukwa cha Atate, iyenso wakudya Ine adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58Umenewu ndi mkate umene watsika kuchokera kumwamba. Osati monga makolo anu anadya ndi kufa: iye wakudya mkate umenewu adzakhala ndi moyo nthawi zonse. 59Zinthu izi analankhula m’sunagoge, naphunzitsa m’Kapernao.

60Kotero ambiri mwa ophunzira ake pakumva [ichi] anati, Mau awa ndi ovuta; ndani angakwanitse kuwamva? 61Koma Yesu, podziwa mwa Iye yekha kuti ophunzira ake anang’ung’uza zokhudza izi, anati kwa iwo, Kodi izi zakukhumudwitsani inu? 62Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali kale? 63Pakuti ndi Mzimu wakupereka moyo, thupi silipindula kanthu: mau amene ndalankhula nanu ndi mzimu komanso moyo. 64Koma mulipo ena mwa inu amene simukhulupilira. Pakuti Yesu anadziwa kuchokera pachiyambi iwo amene anali osakhulupilira, ndi iye amene adzampereka Iye. 65Ndipo Iye anati, Kotero ndinena kwa inu, kuti palibe wakudza kwa Ine pokhapokha ngati chapatsidwa kwa iye kuchokera kwa Atate. 66Kuchokera [nthawi] imeneyo ophunzira ake ambiri anabwerera m’mbuyo ndipo sanayendenso ndi Iye. 67Pamenepo Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Kodi nanunso muchoka? 68Simoni Petro anamuyankha Iye, Ambuye, kodi tidzapita kwa ndani? Inu muli ndi mau a moyo wosatha; 69ndipo ife takhulupilira ndi kudziwa kuti ndinu woyerayo wa Mulungu7. 70Yesu anawayankha iwo, Kodi sindinasankhe inu khumi ndi awiri? Ndipo m’modzi wa inu ndi mdierekezi. 71Tsopano analankhula za Yudase [mwana] wa Simoni, Iskariote, pakuti iye [anali amene] adzampereka Iye, pokhala m’modzi wa khumi ndi awiriwo.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu