Mutu 8
1Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa yake. Ndipo pa tsiku limenelo panauka chizunzo chachikulu pa mpingo umene unali mu Yerusalemu, ndipo onse anamwazikana ku maiko a Yudeya ndi Samariya kupatula atumwi. 2Ndipo anthu okonda Mulungu anamuyika m’manda Stefano ndipo anamulira iye kwambiri. 3Koma Saulo anawononga mpingo, nalowa mnyumba zawo nyumba ndi nyumba, ndipo anakokamo amuna ndi akazi omwe nawatsekera mndende.
4Pamenepo iwo amene anabalalitsidwa anapita ku [maiko] nalalikira uthenga wabwino wa m’mau. 5Ndipo Filipo, potsikira ku mzinda wa Samariya, analalikira Khristu kwa iwo; 6ndipo khamulo ndi mtima umodzi anasamalira zinthu zimene analankhula Filipo, pamene anamumva [iye] ndi kuona zizindikiro zimene iye anazichita. 7Pakuti ambiri amene anali ndi mizimu yoipa inatuluka, nifuula ndi mau okweza; ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. 8Ndipo munali chisangalalo chachikulu mu mzindamo.
9Koma munthu wina, dzina lake Simoni, amene kale amachita matsenga, ndi kudabwitsa fuko la Samariya, nanena kuti iye yekha anali wamkulu. 10Kwa uyu anthu onse anamumvera, kuyambira ang’ono kufikira akulu, nanena, Imeneyi ndi mphamvu ya Mulungu1 imene imatchedwa yayikulu. 11Ndipo iwo anamumvera iye, chifukwa kwa nthawi yaitali wakhala akuwadabwitsa iwo ndi matsenga ake. 12Koma pamene anakhulupilira Filipo polalikira uthenga wabwino okhudza ufumu wa Mulungu2 ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi omwe. 13Ndipo Simoninso mwini anakhulupilira; ndipo, atabatizidwa, anakhalabe pamodzi ndi Filipo; ndipo, poona zizindikiro ndi ntchito zazikulu za mphamvu zimene zinachitika, anali ozizwa. 14Ndipo atumwi amene anali m’Yerusalemu, pakumva kuti Samariya analandira mau a Mulungu3, anatumiza kwa iwo Petro ndi Yohane; 15amene, potsikirako, anawapempherera kuti akalandire Mzimu Woyera; 16pakuti anali asanagwe pa wina aliyense wa iwo, anangobatizidwa chabe ku dzina la Ambuye Yesu. 17Pamenepo anawasanjika iwo manja, ndipo analandira Mzimu Woyera. 18Koma Simoni, poona kuti pakusanja manja kwa atumwi Mzimu Woyera amaperekedwa, anafuna kuwapatsa iwo ndalama, 19nanena, Ndipatseninso mphamvu imeneyi, cholinga kuti aliyense amene ndikamusanja manja akalandire Mzimu Woyera. 20Ndipo Petro anati kwa iye, Ndi ndalama zakozo pita nazo ku chionongeko, chifukwa ukuganiza kuti mphatso ya Mulungu4 ikhoza kugulidwa ndi ndalama. 21Ulibe gawo kapena cholowa mu nkhani imeneyi, pakuti mtima wako siowongoka pamaso pa Mulungu. 522Kotero ulape ku choipa chakochi, ndipo upemphere kwa Ambuye, ngatidi malingaliro a mu mtima mwako akhoza kukhululukidwa; 23pakuti ndaona kuti iwe wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi msinga ya kusalungama. 24Ndipo Simoni poyankha anati, Undipempherere ine kwa Ambuye, kuti kasabwere kwa ine koipa kalikonse ka zinthu walankhulazi.
25Pamenepo iwo, atachitira umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwerera ku Yerusalemu, nalalikira uthenga wabwino kumidzi yambiri ya Asamaliya.
26Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka ndipo upite mbali ya kum’mwera panjira yochoka ku Yerusalemu kupita ku Gaza: yomwenso ndi ya chipululu. 27Ndipo iye ananyamuka napita. Ndipo taonani, munthu waku Aitiopiya, mdindo, munthu wa ulamuliro pansi pa Kandake mfumukazi ya Aitiopiya, wakusunga chuma chake chonse, amene anabwera kudzapembedza ku Yerusalemu, 28akubwerera anakhala pa galeta wake: ndipo amawerenga mneneri Yesaya. 29Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira ndi kudziphatika ku galeta uyu. 30Ndipo Filipo, anathamanga, namumva iye akuwerenga mneneri Yesaya, ndipo anati, Kodi ukudziwa zimene ukuwerengazi? 31Ndipo iye anati, Ndingathe bwanji pokhapokha wina atanditsogolera? Ndipo iye anamupempha Filipo akwere ndi kukhala naye. 32Ndipo ndime ya Malembo imene amawerenga inali yotere: Iye anatsogozedwa ngati nkhosa kupita kokaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa wosalankhula pamaso pa womsenga, kuti sanatsegule pakamwa pake. 33M’kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa, ndipo ndani amene adzabukitsa m’badwo wake? Pakuti moyo wake wachotsedwa padziko lapansi. 34Ndipo mdindoyo pomuyankha Filipo anati, Ndikufunse iwe, akunena zokhudza ndani mneneri pa chimenechi? Za iye mwini kapena za ena? 35Ndipo Filipo, potsegula pakamwa pake ndi kuyambira pa lemba limenelo, analengeza uthenga wabwino wa Yesu kwa iye. 36Ndipo pamene iwo anali kuyenda panjira, anafika pamalo pena panali madzi, ndipo mdindo anati, Taonani madzi; chonditchinga ndi chiyani kuti ndisabatizidwe? 38Ndipo iye analamulira galeta kuti ayime. Ndipo iwo anatsikira ku madziwo, onse Filipo ndi mdindoyo, ndipo anamubatiza iye. 39Koma pamene iwo anatuluka m’madzi Mzimu wa Ambuye anamkwatula Filipo, ndipo mdindoyo sanamuonenso, pakuti anapita njira yake wa chimwemwe. 40Ndipo Filipo anapezeka ku Azotu, ndipo podutsa kumeneko analalikira uthenga wabwino ku mizinda yonse kufikira anadza ku Kaisareya.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu