Mutu 13

1Ndipo tsiku [lomwelo] Yesu anatuluka m’nyumba nakhala mphepete mwa nyanja. 2Ndipo khamu lalikulu la anthu linakhala pamodzi ndi Iye, kotero kuti analowa m’ngalawa nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaimilira m’mbali mwa nyanja. 3Ndipo analankhula nawo zinthu zambiri m’mafanizo, nanena, Taonani, wofesa mbeu anapita kukafesa: 4ndipo pamene anali kufesa, [mbeu] zina zinagwera panjira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya; 5ndipo zina zinagwera pa malo a miyala pamene panalibe nthaka yochuluka, ndipo nthawi yomweyo zinatuluka [mu nthaka] koma chifukwa chosowa nthaka [iliyonse] yozama, 6pamene dzuwa linawomba zinapselera; 7ndipo zina zinagwa pa minga, ndipo minga zinakula nizitsamwitsa izo; 8ndipo zina zinagwera pa nthaka yabwino, ndipo zinabereka chipatso, zina makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu. 9Iye amene ali nawo makutu, amve.

10Ndipo ophunzira anabwera nanena kwa Iye, Chifukwa chiyani mwalankhula kwa iwo m’mafanizo? 11Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa kwa inu kunapatsidwa kudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba, koma kwa iwo sikunapatsidwe; 12pakuti kwa iye amene ali nazo, kwa iye kudzapatsidwa, ndipo adzapangidwa kukhala nazo zochuluka; koma iye amene alibe, ngakhale kamene ali nako kadzachotsedwa kwa iye. 13Pachifukwa chimenechi ndalankhula nawo m’mafanizo, pakuti pakuona iwo sakupenya, ndi pakumva iwo sakutha kumva komanso sakumvetsetsa; 14ndipo mwa iwo mwadzala uneneri wa Eliya, umene umati, Kumva mudzamva koma simudzamvetsetsa, kupenya mudzapenya koma simudzaona konse; 15pakuti mtima wa anthu awa wanenepa, ndipo amva kwambiri ndi makutu awo, ndipo atseka maso awo monga ali mtulo, kuti iwo apenye ndi maso, ndi kumva ndi makutu awo, ndi kumvetsetsa ndi mtima, ndipo akadzatembenuka, ndidzawachiritsa iwo. 16Komatu odalitsika ali maso anu chifukwa aona, ndi makutu anu chifukwa amva; 17pakuti ndinenetsa kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi [anthu] olungama anafunitsitsa kuona zinthu izi zimene mwaona ndipo simunazipenya [izo].

18Inuyo, kotero, mwamvera fanizo la wofesa aja. 19Kwa munthu aliyense amene anamva mau a ufumu ndipo sanawamvetse [iwo], woipayo amabwera ndi kuchotsa chimene chinafesedwa mu mtima mwake: ameneyu ndiye mbeu yofesedwa panjira. 20Koma iye wofesedwa pa malo a miyala — ameneyu ndi munthu amene amamva mau ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe, 21komatu alibe mizu mwa iye yekha, ndipo amakhala mwa kanthawi kochepa kokha; ndipo pakudza msautso ndi mazunzo chifukwa cha mauwo, iye amakhumudwa nthawi yomweyo. 22Ndipo iye amene amafesedwa pa minga — ameneyu ndi munthu amene amamva mau, koma zosangalatsa za moyo uno, ndi chinyengo cha chuma zitsamwitsa dziko lapansi, ndipo iye amakhala wosabereka chipatso. 23Koma iye amene afesedwa pa nthaka yabwino — ameneyu ndi munthu amene amamva mau ndi kuwamvetsetsa, amenenso amabereka chipatso, china zana limodzi, ndi china makumi asanu ndi limodzi, ndi china makumi atatu.

24Fanizo lina linanenedwa kwa iwo, ndi kuti, Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene wafesa mbeu yabwino m’munda mwake; 25koma pamene anthu ali mtulo, adani ake anabwera nafesaso namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. 26Koma pamene m’mera unakula ndi kubereka chipatso, pamenepo namsongole anaonekeranso. 27Ndipo anyamata a mwini mundawo anabwera nanena kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu yabwino m’munda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti? 28Ndipo anati kwa iwo, Munthu [amene ali] mdani wachita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna kuti tipite ndi kusonkhanitsa izo pamodzi? 29Koma iye anati, Ayi; mwina pamene musonkhanitsa namsongole mukazula limodzi ndi tirigu. 1330?Ziloleni zonse zikulire pamodzi kufikira nthawi yokolola, ndipo nthawi yokolola ndidzanena kwa okololawo, Sonkhanitsani poyamba namsongole, ndi kumutentha; koma tirigu mumsonkhanitse pamodzi mu nkhokwe yanga.

31Ananenanso fanizo lina kwa iwo, nanena, Ufumu wakumwamba uli ngati [mbeu] ya mpiru imene munthu anatenga nafesa m’munda mwake; 32mbeuyi ndi yaing’ono kuposa mbeu zonse, koma pamene imera ikula kuposa zomera zakuthengo, ndipo imasanduka mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimabwera ndi kumanga chisa mu nthambi zake.

33Iye analankhula fanizo lina kwa iwo: Ufumu wa kumwamba uli ngati chotupitsa mkate, chimene mzimayi anatenga nabisa m’milingo itatu ya chakudya kufikira yonse inafufuma.

34zinthu zonse izi Yesu analankhula m’mafanizo ku khamu la anthu, ndipo popanda fanizo Iye sanalankhule ndi iwo, 35kuti chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa mwa mneneri, kunena kuti, Ine ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; Ine ndidzalankhula zinthu zobisika ku maziko a dziko lapansi.

36Kenako, atawachotsa makamuwo, Iye analowa m’nyumba; ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye, nanena, Titanthauzireni fanizo la namsongole wa m’munda. 37koma Iye poyankha anati, Iye amene amafesa mbeu yabwino ndi Mwana wa munthu, 38ndipo munda ndi dziko lapansi; ndipo mbeu yabwino, amenewa ndi ana a ufumu, komatu namsongole ndi ana a mdierekezi; 39ndipo mdani amene anafesa mbeuyi ndi mdierekezi; ndipo kukolola ndicho chimaliziro cha nthawi yino, ndipo okololawo ndiwo angelo. 40Ndipo monga momwe namsongole asonkhanitsidwa natenthedwa pamoto, chimodzimodzinso chidzakhala chimaliziro cha nthawi yino. 41Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi ndi kuchotsa milandu yonse, ndi iwo amene achita kusaweruzika; 42ndipo adzawaponya iwo mu ng’anjo ya moto; kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. 43Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wao. Iye amene ali nalo khutu, amve.

44Ufumu wakumwama uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza nachibisa, ndipo m’chimwemwe chake achoka nagulitsa zonse zimene anali nazo, nagula munda umenewo.

45Komanso, ufumu wa kumwamba uli ngati munthu wa malonda amene akufuna ngale zokongola; 46ndipo pamene wapeza ngale imodzi ya mtengo wake, iye anapita nagulitsa zonse zimene anali nazo ndi kugula ngaleyo.

47Komanso, ufumu wakumwamba uli ngati khoka loponyedwa mnyanja, limene lasonkhanitsa pamodzi mitundu yonse, 48limene podzala, analivuulira kumtunda ndipo atakhala pansi, iwo anasonkhanitsa zabwino m’zotengera ndipo zoipa anazitaya. 49Zimenezi zizakhala chimodzimodzi pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzapita nadzasankhula oipa pakati pa olungama, 50ndipo adzawaponya iwo mu ng’anjo ya moto; kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

51Yesu ananena kwa iwo, Kodi mwamvetsetsa zinthu zonsezi? Iwo anati kwa Iye, inde, [Ambuye]. 52Ndipo ananena kwa iwo, Pachifukwa chimenechi mlembi aliyense amene waphunzitsidwa ku ufumu wa kumwamba ali ngati munthu mwini nyumba amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano zomwe.

53Ndipo kunachitika kuti pamene Yesu atatsiriza kunena mafanizo amenewa anachopa pamenepo. 54Ndipo atafika ku dziko lake lomwe, Iye anawaphunzitsa iwo m’masunagoge mwao, kotero kuti anali odabwa, ndipo anati, Kodi [munthu] uyu anazitenga kuti nzeru izi ndi ntchito za mphamvuzi? 55Kodi uyu si mwana wa mpalamatabwa? Kodi amayi wake satchulidwa Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, ndi Yosefe, ndi Simoni, ndi Yuda? 56Ndipo alongo ake, kodi onse siali ndi ife? Nanga [munthu] uyu adzitenga kuti zonse izi? 57Ndipo iwo anakhumudwa mwa Iye, ndipo Yesu anati kwa iwo, Mneneri salemekezeka, makamaka m’dziko la kwao komanso m’nyumba mwake momwe. 58Ndipo Iye sanachite ntchito za mphamvu zambiri kumeneko, chifukwa cha kusakhulupilira kwao.