Mutu 20
1Ndipo [tsiku] loyamba la sabata Mariya wa Magadala anabwera m’mamawa kwambiri kumanda, kudakali m’bandakucha, ndipo anaona mwala utachotsedwa kumanda. 2Pamenepo iye anathamanga nafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu anamukonda, ndipo anati kwa iwo, Amutenga Ambuye kuchoka kumanda, ndipo ife sitikudziwa kuti akamuyika kuti. 3Pamenepo Petro anapitako, ndi wophunzira wina uja, ndipo anafika kumandako. 4Ndipo awiriwa anathamanga pamodzi, ndipo wophunzira wina uja anathamanga kwambiri kuposa Petro, ndipo anafika koyambilira kumanda, 5ndipo posuzumira anaona nsalu za bafuta zili pansi; komabe iye sanalowe mkati. 6Pomwepo Simon Petro anafika, ndipo analowa m’mandamo, ndipo anaona nsalu za bafuta zili pansi, 7ndipo mlezo umene unakulungidwa kumutu kwake, umene sunali pamodzi ndi nsalu ya bafuta, koma wopindidwa paokha pamalo pena. 8Pamenepo analowa mkati ndipo ophunzira wina ujanso amene anayambilira kufika kumanda, anaona ndipo anakhulupilira; 9pakuti iwo anali asanadziwe lemba, kuti Iye adzauka pakati pa akufa. 10Pamenepo ophunzira anapita kunyumba zawo.
11Koma Mariya anayimilira kunja kwa manda akulira. Pamene iye amalira, anasuzumira m’manda, 12ndipo taonani angelo awiri atakhala ovala [zovala] zoyera, wina atakhala kumutu ndi wina ku miyendo, pamalo pamene thupi la Yesu linayikidwa. 13Ndipo iwo anati kwa iye, Mkaziwe, kodi ukulira chiyani? Iye anati kwa iwo, Chifukwa amutenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene amuyika Iye. 14Atanena zinthu zimenezi anayang’ana kumbuyo ndipo taonani Yesu anayimilira [pamenepo], ndipo sanadziwe kuti anali Yesu. 15Yesu anati kwa iye, Mkaziwe, chifukwa chiyani ukulira? Ukufuna ndani? Iye, poganiza kuti anali mlimi, anati kwa Iye, Ambuye, ngati mwamutenga kuno, ndiuzeni kumene mwamuyika Iye, ndipo ine ndikamutenge. 16Yesu anati kwa iye, Mariya. Potembenuka iye, anati m’Chiheberi, Raboni, kutanthauza Mphunzitsi. 17Yesu anati kwa iye, Usandikhudze, pakuti sindinakwere kupita kwa Atate wanga ndi Atate wako, ndi [kwa] Mulungu1 wanga ndi Mulungu2 wako. 18Mariya wa Magadala anapita nabweretsa mau kwa ophunzira kuti anawona Ambuye, ndipo [kuti] ananena zinthu izi kwa iye.
19Pamenepo pokhala madzulo tsiku limenelo, lomwe linali [tsiku] loyamba la sabata, ndipo zitseko zinali zotseka kumene kunali ophunzira, poopa Ayuda, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati kwa iwo, Mtendere [ukhale] kwa inu. 20Ndipo atalankhula izi, Iye anawaonetsa manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera, poona Ambuye. 21Pameneponso [Yesu] anati kwa iwo, Mtendere [ukhale] kwa inu: monga Atate anandituma, Inenso ndituma inu. 22Ndipo atanena zimenezi, anapumira mwa [iwo], Landirani Mzimu Woyera: 23zochimwa zilizonse zimene inu muwakhululukira anthu, zikhululukidwa kwa iwo; [zochimwa] zilizonse zimene mugwiritsa, zigwiritsidwa.
24Koma Tomasi, m’modzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanali nawo pamodzi pamene Yesu anabwera. 25Pamenepo ena mwa ophunzira anati kwa iye, Ife tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Pokhapokha nditaona m’manja mwake zipsera za misomali, ndi kuyika chala changa pa chipsera cha misomali, ndi kuyika dzanja langa mu nthiti mwake, sindikhulupilira. 26Ndipo pakutha pa masiku asanu ndi atatu, ophunzira ake analinso mnyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo pamodzi. Yesu anabwera, chitseko chili chitsekere, ndipo anayima pakati pawo nati, Mtendere [ukhale] kwa inu. 27Pamenepo Iye anati kwa Tomasi, Bweretsa chala chako ndipo uwone manja anga; ndipo bweretsa dzanja lako ndipo uliyike mu nthiti mwanga; ndipo usakhale wosakhulupilira, koma wokhulupilira. 28Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga ndi Mulungu3 wanga. 29Yesu anati kwa iye, Chifukwa wandiona Ine wakhulupilirano: odala iwo amene sanaone koma akhulupilira.
30Pamenepo zizindikiro zina Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwe m’buku ili; 31Komatu izi zalembedwa kuti inu mukhulupilire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu4, ndipo kuti pokhulupilira mukakhale nawo moyo m’dzina lake.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu