Mutu 11

1Ndipo pamenepo ndinapatsidwa bango ngati ndodo, nanena, Tamuka, ndipo uyese kachisi wa Mulungu1, ndi guwa, ndi iwo amene amalambira m’menemo. 2Ndipo bwalo limene [lili] kunja kwa kachisi ulisiye padera, usaliyese; chifukwa linaperekedwa kwa amitundu, ndipo mzinda woyera adzaupondereza pansi pamapazi kwa miyezi makumi anayi ndi mphambu ziwiri. 3Ndipo ndidzapereka [mphamvu] kwa mboni zanga ziwiri, ndipo zidzachitira umboni kwa masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri kudza mphambu makumi asanu ndi limodzi zitavala ziguduli. 4Zimenezi ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi nyali ziwili zimene zimayima pamaso pa Ambuye wadziko lapansi; 5ndipo ngati wina afuna kuwaononga iwo, moto umatuluka mkamwa mwao, ndipo umalikhwira adani awo. Ndipo ngati wina afuna kuwaononga iwo, momwemo iye aphedwe. 6Amenewa ali ndi mphamvu yakutseka kumwamba kuti mvula isagwe m’masiku a uneneri wao; ndipo ali ndi mphamvu pa madzi kuwasandutsa mwazi, ndi kukantha dziko lapansi monga afunira ndi mliri wa mtundu uliwonse. 7Ndipo pamene iwo adzamaliza umboni wao, chirombo chotuluka ku phompho chidzachita nawo nkhondo, ndipo chidzawagonjetsa, ndi kuwapha iwo: 8ndipo matupi awo adzakhala pa msewu wa mzinda waukulu, umene umatchedwa mwa uzimu Sodomu ndi Aigupto, kumenenso Ambuye wao anapachikidwa. 9Ndipo [amuna] a anthu ndi mitundu ndi manenedwe ndi mafuko anaona matupi awo masiku atatu ndi theka, ndipo sanalole matupi awo ayikidwe m’manda. 10Ndipo iwo akukhala padziko lapansi anakondwera nawo, ndipo ali odzala ndi chisangalalo, ndipo adzatumizirana mphatso wina ndi mzake, chifuwa awa, aneneri awiriwa, anawazunza iwo akukhala padziko lapansi. 11Ndipo atapita masiku atatu ndi theka mzimu wa moyo wochokera kwa Mulungu2 unafika mwa iwo, ndipo anayimilira pa mapazi awo; ndipo mantha akulu anagwa pa onse anawapenya iwo. 12Ndipo ndinamva mau akulu kuchoka kumwamba nanena kwa iwo, Bwerani kuno; ndipo iwo anakwera kumwamba m’mitambo, ndipo adani awo anawapenya iwo. 13Ndipo mu ola lomwelo panali chivomezi chachikulu, ndipo gawo limodzi la magawo khumi a mzindawo linagwa, ndipo anthu zikwi zisanu ndi ziwiri anafa ndi chivomezichi. Ndipo otsalawo anazadzidwa ndi mantha, ndipo anapereka ulemelero kwa Mulungu3 wakumwamba.

14Tsoka lachiwiri linadutsa; taonani, tsoka lachitatu lidza mzanga.

15Ndipo mngelo wa chisanu ndi chiwiri anaomba lipenga [lake]: ndipo panali mau akulu m’mwamba, akunena, Ufumu wadziko lapansi wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake wafika, ndipo iye adzalamulira ku nthawi za nthawi. 16Ndipo akulu makumi awiri ndi mphambu anayi, amene anakhala pa mipando yawo ya chifumu pamaso pa Mulungu4, anagwetsa nkhope zawo, ndi kulambira Mulungu5, 17nanena, Tikuthokozani inu, Ambuye Mulungu6 Wamphamvuzonse, [Iye] amene ali, ndipo anali, kuti munatenga mphamvu zanu zazikulu ndipo mulamulira. 18Ndipo mafuko anadzala ndi mkwiyo, ndipo mkwiyo wanu wafika, ndi nthawi ya akufa kuti aweruzidwe, ndi kupereka mphoto kwa atumiki anu aneneri, ndi kwa oyera mtima, ndi kwa iwo akuopa dzina lanu, ang’ono ndi akulu; ndi kuwononga iwo akuwononga dziko lapansi.

19Ndi kachisi wa Mulungu7 m’mwamba anatsegulidwa, ndipo likasa la chipangano linaoneka mkachisi wake: ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala akulu.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu