Mutu

1Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteyo m’baleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzanthu, 2ndiponso kwa Apiya ndi kwa Arkipo msilikali mzathu, komanso kwa mpingo umene uli mnyumba yako. 3Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu1 Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

4Ine ndiyamika Mulungu2 wanga, nthawi zonse kukutchula iwe m’mapemphero anga, 5pakumva chikondi chako ndi chikhulupiriro chimene uli nacho pa Ambuye Yesu, komanso kwa oyera mtima onse, 6kuti m’menemo chiyanjano cha chikhulupiriro chikakhale chogwira ntchito m’chidziwitso cha zinthu zonse zabwino zimene zili mwa ife kulunjika kwa Khristu [Yesu]. 7Pakuti ife tili nako kuyamika kwakukulu ndi chilimbikitso kudzera m’chikondi chako, chifukwa chifundo cha oyera mtima chatsitsimutsidwa ndi iwe, m’bale.

8Pamenepo pokhala nako kulimbika mtima mwa Khristu kukulamulira iwe chimene chili choyenera, 9pakuti chifukwa cha chikondi ndikudandaulira iwe, pokhala ngati Paulo wokalamba, ndi amenenso ali wandende wa Yesu Khristu. 10Ndikudandaulira iwe chifukwa cha mwana wanga, amene ndinabereka mu msinga zanga, Onesimo, 11amene anali osapindulitsa kwa iwe, koma tsopano wakhala wa phindu kwa iwe ndi ine: 12ameneyo ndam’bwezeretsa kwa iwe: [koma umlandire] iye, kunena kuti, mwa chifundo changa: 13ameneyo ndinafunitsitsa kumsunga ine ndekha, kuti kwa inu akatumikire mwa ine msinga zanga za uthenga wabwino; 14koma sindinafune kuchita kanthu popanda maganizo ako, kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza koma mwa ufulu: 15pakuti kapena pachifukwa chimenechi walekanitsidwa [kwa iwe] kwa kanthawi, kuti akakhale mwathunthu wakowako nthawi zonse; 16osatinso ngati kapolo, koma woposera kapolo, m’bale wokondedwa, wapadera kwa ine, komanso makamaka kwa iwe, mthupi komanso mwa Ambuye? 17Pamenepo ngati iwe ugwiritsitsa ine kukhala woyanjana naye, mlandire monga ine; 18koma ngati anakulakwira kalikonse kapena ali nawe ngongole iliyonse, zimenezo uwerengere pa ine. 19Ine Paulo ndalemba ichi ndi dzanja langa; ndidzabwenza ndithu: sindinena ichi kwa iwe poti nawe uli nayo ngongole kwa ine. 20Inde, m’bale, ndikhala nalo phindu pa iwe mwa Ambuye: utsitsimutse chifundo changa mwa Khristu. 21Pokhala nacho chilimbikitso pa kumvera kwako, ndakuIembera iwe, podziwa kuti uchita mwinanso kuposera m’mene ndanenera. 22Koma undikonzerenso malo ogona; pakuti ndiyembekezera kuti ndidzafika kwa iwe kudzera m’mapemphero ako. 23Epafra akukulonjera iwe, wandende mzanga mwa Khristu Yesu; 24ateronso Marko, Aristako, Dema, Luka, antchito amnzanga. 25Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.

1Elohimu2Elohimu