Mutu 11
1Ndipo kunachitika kuti pamene anali pamalo pena kupemphera, pamene anamaliza, m’modzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, ngakhalenso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake. 2Ndipo Iye anati kwa iwo, Pamene mupemphera, muziti, Atate, dzina lanu lilemekezedwe; ufumu wanu udze; 3mutipatse ife mkate wathu wofunikira wa tsiku ndi tsiku; 4ndipo mutikhululukire machimo athu, pakuti ifenso tikhululukira wina aliyense amene ali ndi mangawa kwa ife; ndipo musatitsogolere ife m’mayesero. 5Ndipo Iye anati kwa iwo, Ndani mwa inu amene adzakhala naye mzake, ndipo adzapita kwa iye pakati pa usiku nati kwa iye, Mzanga ndigawireko mikate itatu, 6pakuti mzanga amene ali pa ulendo wandifikira, ndipo ndilibe kanthu kakumkonzera iye; 7ndipo iye amene ali mkati ayankhe kuti, Usandisokoneze iwe; khomo langa ndi lotseka, ndipo ana anga ndili nawo limodzi nkugona; Inetu sindingathe kudzuka kukupatsa iwe zimenezi? 8Inetu ndinena kwa inu, Ngakhale iye sazadzuka ndi kuwapatsa [iwo] kwa iye chifukwa chakuti ndi mzake, chifukwa cha manyazi, mwanjira ina iliyonse, azadzuka ndi kumupatsa zochuluka monga iye afunira. 9Ndipo ndinena kwa inu, Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu. 10Pakuti aliyense amene apempha adzalandira; ndipo amene agogoda chidzatsegulidwa. 11Koma ndani wa inu amene ali tate pamene mwana apempha mkate, ndipo [tate] ampatsa mwala? Kapenanso nsomba, ndipo m’malo mwa nsomba adzampatsa njoka? 12kapenanso ngati apempha dzira, adzampatsa chinkhanira? 13Kotero ngati inu, okhala oipa, mudziwa momwe muperekere mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani nanga Atate amene ali kumwamba adzapereka Mzimu Woyera kwa iwo amene amupempha Iye.
14Ndipo Iye anali kutulutsa chiwanda, ndipo chinali chosalankhula; ndipo kunachitika, chiwanda chitatuluka, [munthu] wosalankhula uja analankhula. Ndipo makamu anali odabwa. 15Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mfumu ya ziwanda Iyeyu amatulutsa ziwanda. 16Ndipo ena pomuyesa [Iye] anafuna chizindikiro chochokera kumwamba. 17Koma Iye, podziwa malingaliro awo, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika paokha umapasuka: ndipo nyumba ikaukira nyumba imagwa; 18ndipo ngatinso Satana wagawanika pa iye yekha, nanga ufumu wake udzayimikika bwanji? Popeza munena kuti Ine nditulutsa ziwanda mwa Beelzebule. 19Koma ngati Ine mwa Beelzebule nditulutsa ziwanda, ana anu — amatulutsa [izo] mwa ndani? Pachifukwa chimenechi iwo adzakhala oweruza inu. 20Koma ngati ndi dzanja la Mulungu Ine ndimatulutsa ziwanda, pamenepo ufumu wa Mulungu wadza pa inu. 21Pamene [munthu] wa mphamvu ndi zida m’manja ayang’anira nyumba yake, katundu wake ali mu mtendere; 22koma ngati wamphamvu kuposa iye abwera kwa [iye] namgonjetsa, amatenga zake zonse zimene amadalira, ndipo adzagawa zolandidwazo [zimene anazitenga] kwa iye. 23Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane, ndipo iye amene sasonkhanitsa ndi Ine amamwaza. 24Pamene mzimu woipa utuluka mwa munthu, umapita ku malo owuma kukafuna mpumulo; ndipo ngati supeza malowo umati, Ndibwerera kunyumba kwanga kumene ndinatuluka. 25Ndipo pobwera, umapeza mosesa ndi mokonzedwa. 26Pamenepo umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa kuposera iye mwini, ndi kulowa m’menemo, imakhazikika m’menemo; ndipo chikhalidwe cha munthu uyu chimakhala choipa kusiyana ndi choyamba. 27Ndipo kunachitika kuti pamene amalankhula zinthu izi, mkazi wina, pokweza mau ake m’khamulo, anati kwa Iye, Yodala mimba imene inabereka inu, ndi mabere amene munayamwa. 28Koma Iye anati, Inde komabe, odala amene amamva mau a Mulungu1 ndi kuwachita.
29Koma pamene makamu anasonkhana pamodzi, Iye anayamba kulankhula, M’badwo uno ndi m’badwo woipa: umafuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzaperekedwa koma chizindikiro cha Yona. 30Pakuti monga Yona anali chizindikiro kwa Anineve, chimodzimodzinso Mwana wa munthu ku m’badwo uyu. 31Mfumukazi yaku m’mwera idzayimilira pa chiweruziro ndi anthu a m’badwo uno, ndipo adzawatsutsa: pakuti iye anabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo taonani, woposa Solomo ali pano. 32Amuna aku Nineve adzayimilira mu chiweruzo ndi m’badwo uwu, ndipo adzautsutsa: pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo taonani, woposa Yona ali pano. 33Komatu palibe amene amayatsa nyali m’seri, kapena pansi pa muyeso, koma pa choikapo nyali, kuti iwo akulowa mkati akathe kuona kuwalako. 34Nyali ya thupi ndilo diso: pamene diso lako lili langwiro, thupi lako lonse limawala; koma pamene lili loipa, thupi lakonso limakhala lakuda. 35Onetsetsani pamenepo kuti kuwala kumene kuli mwa inu kusakhale mdima. 36Ngati pamenepo thupi lako lonse [lili] kuwala, losakhala nalo malo akuda, lidzakhala lowala lonse monga momwe nyali iwunikira inu ndi kuwala kwake.
37Koma Iye akali chilankhulire, Mfarisi wina anamufunsa Iye kuti akadye naye; ndipo polowa Iye mnyumba anakhala pa gome. 38Koma Mfarisi powona [ichi] anali wodabwa kuti Iye sanayambe kusamba m’manja asanadye chakudya. 39Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma [magawo] a mkati mwanu ali odzadza ndi zolanda ndi zoipa. 40Opusa inu, kodi wopanga kunja sangathenso kupanga mkati? 41Koma m’malo mwake perekani za chifundo zimene muli nazo, ndipo taonani, zinthu zonse zili zoyera kwa inu. 42Koma tsoka kwa inu, Afarisi, pakuti mumapereka chakhumi cha timbeu tonunkhira ndi timbeu tokometsa chakudya ndi zamizu zonse, ndipo mumasiya chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu2: izi zimene munayenera kuchita, ndipo simunasiye izo osachita. 43Tsoka kwa inu, Afarisi, pakuti mumakonda mipando yoyambilira ya m’masunagoge ndi kulandira maulemu m’misika. 44Tsoka kwa inu, pakuti muli ngati manda osema amene saoneka, ndipo anthu amene amayenda pamwamba pake sawadziwa [iwo]. 45Ndipo m’modzi wa akatakwe a chilamulo pomuyankha anati, Mphunzitsi, ponena zinthu zimenezi mukutinyozanso ife. 46Ndipo Iye anati, Kwa inunso muli ndi tsoka, akatakwe a chilamulo, pakuti mumasenzetsa anthu mtolo wolemetsa kunyamula, koma inu eni simungathe kukhudza mtolowo ndi chala chanu. 47Tsoka kwa inu, pakuti mumanga pa manda osema a aneneri, koma makolo anu anawapha iwo. 48Inu mumachitira umboni pamenepo, ndi kuvomereza ku ntchito za makolo anu; pakuti anawapha iwo, ndipo inu mumawamangira [manda awo osema]. 49Pachifukwanso chimenechi nzeru ya Mulungu3 inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi, ndipo mwa amenewa adzawapha ndi kuwathamangitsa ndi chizunzo, 50kuti mwazi wa aneneri onse umene unakhetsedwa kuyambira pa chiyambi cha dziko lapansi ukafunidwe pa m’badwo uwu, 51kuchokera ku mwazi wa Abele kufika ku mwazi wa Zakariya, amene anafa pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya kachisi; indetu, ndinena kwa inu, udzafunidwa ndi m’badwo uno. 52Tsoka kwa inu, akatakwe a chilamulo, pakuti mwachotsa chifungulo cha chidziwitso; inu eni simunathe kulowamo, ndipo iwo amene amalowa mwawaletsa. 53Ndipo pamene amanena zinthu izi kwa iwo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kwambiri, ndi kumpangitsa Iye kuti alankhule zinthu zambiri; 54namuyang’anira Iye, [nafuna] kuti akamkole ndi mau ochokera m’kamwa mwake, [kuti apeze chomuneneza Iye].
1Elohimu2Elohimu3Elohimu