Mutu 7
1Ndipo mkulu wa ansembe anati, Kodi zinthu zimenezi zili choncho? 2Ndipo Stefano anati, Abale ndi atate inu, tamverani. Mulungu1 wa ulemelero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu pamene anali m’Mesopotamiya, asanakhale iye m’Harana, 3ndipo anati kwa iye, Tuluka m’dziko lako komanso pakati pa abale ako, ndipo bwera m’dziko limene ndidzakuonetsa iwe. 4Pamenepo potuluka m’dziko la Alkadayo anakhala m’Harana, ndipo kumeneko, atamwalira atate wake, anawatengera m’dziko ili limene iye amakhala tsopano. 5Ndipo sanampatse iye cholowa m’menemo, ngakhale pamene phazi lake linapondapo; ndipo anamulonjeza iye kumpatsa ilo cholowa, ndi mbeu yake yomtsatira, pamene iye analibe mwana. 6Ndipo Mulungu2 analankhula chotero: Mbeu yake idzakhala alendo m’dziko la eni, ndipo adzawachita iwo ukapolo ndi kuwazunza kwa zaka mazana anayi; 7ndipo mtundu umene iwo udzawachita ukapolo ndidzauweruza Ine, atero Mulungu3; ndipo pakutha pa izi iwo adzabwera ndi kunditumikira Ine m’malo muno. 8Ndipo anampatsa iye pangano la mdulidwe; ndipo pamenepo anabereka Isake ndi kumdula iye tsiku lachisanu ndi chitatu; ndipo Isake anabereka Yakobo, ndipo Yakobo anabereka akuluakulu a mafuko khumi ndi awiriwo. 9Ndipo akuluakuluwo, pochitira nsanje Yosefe, anamgulitsa kwa Aigupto. Ndipo Mulungu4 anali naye, 10ndipo anampulumutsa ku mazunzo ake onse, ndipo anampatsa kukonderedwa ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anamusankha iye kukhala kazembe wa Aigupto ndi nyumba yake yonse. 11Koma chilala chinadza m’dziko la Aigupto ndi Kenani, ndi chisautso chachikulu, ndipo makolo athu sanapeze chakudya. 12Koma Yakobo, pakumva iye kuti kuli tirigu m’Aigupto, anatumiza makolo athu poyamba; 13ndipo kachiwiri Yosefe anadziulula yekha kwa abale ake, ndipo banja la Yosefe linadziwika kwa Farao. 14Ndipo Yosefe anatumiza nayitana atate wake ndi banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu. 15Ndipo Yakobo anatsikira m’Aigupto namwalira, iye pamodzi ndi makolo athu, 16ndipo anawanyamula kupita nawo ku Sukemu ndipo anawayika m’manda osema amene Abrahamu anawagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Emori [tate] wawo wa Sukemu. 17Koma pamene nthawi ya lonjezano inawandikira imene Mulungu5 analonjeza kwa Abrahamu, anthuwo anakula ndi kuchulukana mu Aigupto, 18kufikira mfumu ina inauka mu Aigupto imene sinamdziwe Yosefe. 19Iye anachita mochenjera ndi mtundu wathu, ndipo choipa chinawachitikira makolo athu, anawatayitsa ana awo kuti asakhale ndi moyo. 20M’nyengo imeneyi Mose anabadwa, ndipo anali wooneka bwino kwambiri, amene analeredwa miyezi itatu m’nyumba mwa atate wake. 21Ndipo atatayidwa, mwana wa mkazi wa Farao anamtenga iye, ndipo anamlera mwa iye yekha [kukhala] mwana wake. 22Ndipo Mose anaphunzitsidwa mwa nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu m’malankhulidwe ake ndi m’machitidwe ake. 23Ndipo pamene nyengo ya zaka makumi anayi inakwaniritsidwa kwa iye, chinamufikira mu mtima mwake kuyang’anira abale ake, ana a Israyeli; 24ndipo poona wina kuti akuchitiridwa choipa, anamuteteza [iye], ndipo anam’bwezera chilango wozunzidwayo, nakantha m’Aigupto. 25Pakuti amaganiza kuti abale ake amvetsetsa kuti Mulungu6 mwa dzanja lake akuwapatsa chiombolo. Koma iwo sanazindikire ichi. 26Ndipo m’mawa mwake anadzionetsera yekha kwa iwo pamene amalimbana ndeu, ndipo anati awayanjanitse mwa mtendere, nanena, Ndinu pachibale, chifukwa chiyani mukuyambana wina ndi mzake? 27Koma iye amene amamyamba mzakeyo anamkankha iye, nanena, Ndani amene anakuyika iwe kukhala wolamulira ndi woweruza wathu? 28Kodi iwe ukufuna undiphe monga unamuphera dzulo m’Aigupto uja? 29Ndipo Mose anathawa pa kulankhula uku, ndipo anakhala mlendo m’dziko la Midyani, kumene anaberekako ana amuna awiri. 30Ndipo pamene zaka makumi anayi zinakwaniritsidwa, mngelo wa Mulungu anaonekera kwa iye m’chipululu cha phiri la Sinayi, m’lawi la moto la tchire. 31Ndipo Mose poona izi anadabwa ndi masomphenyawa; ndipo iye pokwera kuti apenyetsetse, panamveka mau a Ambuye, 32Ine ndine Mulungu7 wa makolo anu, Mulungu8 wa Abrahamu, ndi wa Isake, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose anathunthumira, osalimba mtima kuti awonenso [ichi]. 33Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nkhwayira ku mapazi ako, pakuti malo amene wayimawo ndi malo woyera. 34Ine ndaona kuzunzika kwa anthu anga ali m’Aigupto, ndipo ndamva kubuula kwao, ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, bwera, ndidzakutuma iwe ku Aigupto. 35Mose uyu, amene iwo anamkana, nanena, Ndani amene anakuyika wolamulira ndi woweruza? Ameneyu Mulungu9 anamtuma [kukhala] wolamulira ndi momboli ndi dzanja la mngelo amene anaonekera kwa iye m’tchire. 36Iye anawatsogolera iwo, atachita zozizwa ndi zizindikiro m’dziko la Aigupto, ndi m’nyanja yofiira, ndiponso m’chipululu kwa zaka makumi anayi. 37Ameneyu ndi Mose amene anati kwa ana a Israyeli, Mneneri amene Mulungu10 adzamuukitsa kwa inu pakati pa abale anu monga ine [ameneyo mudzamumvera]. 38Ameneyu ndi amene anali mu mpingo m’chipululu, ndi mngelo amene analankhula kwa iye m’phiri la Sinayi, ndi makolo athu; amene analandira mawu amoyo kutipatsa ife; 39amene makolo athu sanawafune, koma iwo anamusatsa [iye], ndipo m’mitima mwao anatembenukira ku Aigupto, 40nanena kwa Aloni, utipangire ife milungu11 imene idzatitsogolera ife; pakuti Mose uyu, amene anatitulutsa m’dziko la Aigupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira. 41Ndipo iwo anapanga mwana wa ng’ombe m’masiku amenewo, ndipo anapereka nsembe kwa fanolo, ndipo anasangalala ndi ntchito za manja awo. 42Koma Mulungu12 anatembenuka ndi kuwapereka iwo atumikire zolengedwa zakumwamba; monga kunalembedwa m’buku la aneneri, Kodi munapereka kwa ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anayi m’chipululu, inu nyumba ya Israyeli? 43Indedi, inu munatenga chihema cha Moloki, komanso nyenyezi ya mulungu13 [wanu] Refani, zinthu zimene munazipanga kuzilambira izo; ndipo ine ndidzakuyendetsani kudutsa Babulo. 44Makolo athu anali ndi chihema cha umboni m’chipululu, monga iye amene analankhula kwa Mose analamulira kuchita monga chithunzi chimene adachiona; 45chimenenso makolo athu, polandira kuchokera kwa makolo awo, anachibweretsa pamodzi ndi Yoswa pamene analowa m’dziko la amitundu, amene Mulungu14 anawathamangitsa kuchoka pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide; 46amene anapeza kukonderedwa pamaso pa Mulungu15, ndipo anapeza chihema chokhalamo Mulungu16 wa Yakobo; 47koma Solomo anam’mangira Iye nyumba. 48Komatu Wam’mwambamwambayo samakhala pamalo wopangidwa ndi manja; monga ananena mneneri, 49Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu ndipo dziko lapansi chopondera mapazi anga: kodi ndi nyumba yotani imene inu mukhoza kundimangira Ine? Atero Ambuye, kapena ali kuti malo anga opumulira? 50kodi manja anga sanakonze zinthu zonse izi? 51Ouma makosi inu ndi osadulidwa mu mtima ndi m’makutu, nthawi zonse mumakana Mzimu Woyera; monga makolo anu, inunso chimodzimodzi. 52Ndani wa aneneri amene sanazunzidwe ndi makolo anu? Ndipo anapha iwo amene ananeneratu zokhudza kubweranso kwa Wolungamayo, amene inu mwakhala omupereka ndi kumupha! 53amene munalandira chilamulo monga anachiyikira mwa utumiki wa angelo, ndipo sanachisunge.
54Ndipo pakumva zinthu izi anasweka mtima, ndipo anamkukutira mano iye. 55Koma pozadzidwa ndi Mzimu Woyera, popenyetsetsa maso ake kumwamba, iye anaona ulemelero wa Mulungu17, ndipo Yesu anali kuyimilira kudzanja lamanja la Mulungu18, 56ndipo anati, Taonani, ndipenya kumwamba kotseguka, ndipo Mwana wa munthu akuyima kudzanja lamanja la Mulungu19. 57Ndipo iwo anafuula ndi mau okweza, ndipo anatseka makutu awo, ndipo anakhamukira kwa iye ndi cholinga chimodzi; 58ndipo atamtulutsa [iye] kunja kwa mzinda, anamgenda [iye]. Ndipo mboni zinayika zovala zawo pa mapazi a mnyamata wotchedwa Saulo. 59Ndipo iwo anamgenda Stefano, napemphera, ndipo anati, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga. 60Ndipo pogwada pansi, iye anafuula ndi mau okweza, Ambuye, musayikire tchimo ili kwa iwo. Ndipo atalankhula izi, iye anagona tulo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu16Elohimu17Elohimu18Elohimu19Elohimu