Mutu 9
1Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi ine sindinamuone Yesu Ambuye wathu? Kodi inu sintchito yanga mwa Ambuye? 2Ngati sindine mtumwi kwa ena, komabe mwa mlingo ulionse ndine mtumwi kwa inu: pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inuyo mwa Ambuye. 3Kuziteteza kwanga kwa iwo amene akundifunsa ine ndi uku: 4Kodi tilibe ufulu wakudya ndi kumwa? 5kodi tilibe ufulu wakuzitengera mlongo kukhala mkazi wathu, monga achitiranso atumwi ena, ndi abale mwa Ambuye, ndi Kefa? 6Kapena ine ndi Barnaba, tilibe ufulu wosagwira ntchito? 7Ndani amene apita ku nkhondo namadzilipira yekha? Ndani amene adzala munda wa mpesa ndipo osadya chipatso chake? Kapena ndani amene aweta gulu la ziweto ndipo sakumwa mkaka wa ziweto zake? 8Kodi ndikulankhula zinthu izi ngati munthu, kapenanso lamulo silinena za zinthu izi? 9Pakuti mu lamulo la Mose mwalembedwa, Musamamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu. Kodi Mulungu1 amasamala za ng’ombe, 10kapena akulankhula izi chifukwa cha ife? Pakuti pachifukwa cha ife kunalembedwa, kuti wolima alime mwachiyembekezo, ndipo iye amene apuntha tirigu, mwachiyembekezo achite mwa kugawana nawo. 11Ngati ife takufetserani kwa inu zinthu za uzimu, kodi sichinthu chachikulu kuti ife tidzakolole zanu zakuthupi? 12Ngati ena apindula ndi ufulu woterewu pa inu, kodi ife sitikuyeneranso kutero? Komatu ife sitinagwiritse ufulu umenewu, koma timapilira zinthu zonse, kuti tisayike chotchinga pa uthenga wabwino wa Khristu. 13Kodi simudziwa kuti iwo amene agwira ntchito mu zinthu zoyeretsedwa amadya [zoperekedwa] m’kachisi; iwo amene asamalira pa guwa amatenga za paguwa? 14Chomwechonso Ambuye anawakhazikitsa iwo amene alalikira uthenga wabwino kuti adye za uthenga wabwino. 15Koma ine sindinagwiritseko kalikonse ka izi. Tsopano ine sindinalembe zinthu izi kuti zichitike kwa ine; pakuti kunali kwabwino kwa ine kufa kusiyana kuti wina wa inu ayese chabe kuzitamandira kwanga. 16Pakuti ngati ndilalikira uthenga wabwino, palibe chozitamandira nacho; pakuti chofunikiracho chayikidwa pa ine; pakuti ndili watsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino. 17Pakuti ngati ndichita izi mongozipereka, ndili nayo mphoto; koma ngati sindichita mwa kufuna kwanga, ndiye kuti ndinakhulupilidwa ndi m’dindo. 18Kodi mphoto yanga ndi chiyani pamenepo? Kuti polalikira uthenga wabwino ndiyesa uthenga wabwino kukhala waulere [kwa ena], kotero kuti ndisagwiritse ntchito, monga ndi wanga, mwa ufulu wanga pakulalikira uthenga wabwino. 19Pokhala mfulu kwa onse, ndazipanga ndekha kukhala kapolo kwa onse, kuti ndikapindule ochuluka [monga ndingathere]. 20Ndipo kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda, cholinga kuti ndikapindule Ayuda: kwa iwo okhala pansi pa lamulo, monga wokhala pansi pa lamulo, cholinga kuti ndikapindule iwo amene ali pansi pa lamulo: 21kwa iwo amene alibe lamulo, monga wopanda lamulo, (osati monga wopanda lamulo kwa Mulungu2, koma womvera lamulo kwa Khristu,) cholinga ndikapindule [iwo] opanda lamulo. 22Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, cholinga kuti ndikapindule ofooka. Kwa onse ndinakhala zinthu zonse, kuti pa zochitika zonse ndikapulumutsepo ena. 23Ndipo ndimachita zonse izi chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale wochita nawo pamodzi.
24Kodi inu simudziwa kuti iwo othamanga liwiro athamanga onse, koma m’modzi ndi amene amawina mphoto? Chotero thamangani cholinga kuti mukapeze mphoto. 25Koma aliyense wakupikisana [mphoto] azikaniza zinthu zonse: pamenepo iwo amenewa akalandira korona owonongeka, koma ife osawonongeka. 26Kotero ine ndithamanga, simonga mokayikakayika; kotero ndikalimbane, osati ngati ndikumenya mphepo. 27Komatu ndipumuntha thupi langa, ndi kulilamulira, kuti pamene ndalilikira ena ineyo ndingakanidwe.
1Elohimu2Elohimu