Mutu 1

1Paulo, mtumwi woyitanidwa wa Yesu Khristu, mwa chifuniro cha Mulungu1, ndi Sositene m’baleyo, 2kwa mpingo wa Mulungu2 umene uli ku Korinto, kwa [iwo] oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, otchedwa oyera mtima, ndi onse ponsepo amene ayitanira pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ndi wao komanso wathu: 3Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu3 Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

4Ine ndiyamika Mulungu4 wanga nthawi zonse chifukwa ka inu, potengera chisomo cha Mulungu5 choperekedwa kwa inu mwa Khristu Yesu; 5kuti m’zonse munalemekezedwa mwa Iye, m’mau onse [a chiphunzitso], ndi chidziwitso chonse, 6(molingana ndi umboni wa Khristu wotsimikizika mwa inu,) 7kotero kuti inu mukaperewere kukhala opanda mphatso, podikilira vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Khristu; 8amenenso adzakutsimikizirani inu kufika chimaliziro, opanda chifukwa m’tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu. 9Mulungu6 [ndi] wokhulupirika, mwa ameneyu inu mwaitanidwa mu chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu Ambuye wathu.

10Tsopano ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti inu nonse mukanene chithu chomwecho, ndi kuti pasakhale pakati panu magawano; koma kuti mukhale ogwirizana m’malingaliro amodzi ndi mtima umodzi. 11Pakuti kwaonetsedwa kwa ine zokhudza inu, abale anga, mwa iwo a [nyumba ya] Kloe, kuti pali kulimbana pakati panu. 12Koma ndilankhula ichi, kuti aliyense wa inu anena, Ndine wa Paulo, ndipo ine ndi wa Apolo, ndipo ine ndi wa Kefa ndipo ine wa Khristu. 13Kodi Khristu wagawanikana? Kodi Paulo anapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena inu munabatizidwa m’dzina la Paulo? 14Ine ndiyamika Mulungu7 kuti sindinabatizeko aliyense wa inu, kupatula Krisipo ndi Gayo, 15kuti aliyense akanene kuti wabatizidwa m’dzina langa. 16Inde, ndinabatizanso a pabanja la Stefana; pakuti ena onsewa sindidziwa ngati ine ndinabatiza wina wa iwo. 17Pakuti Khristu sananditume ine kukabatiza, koma kulalikira uthenga wabwino; osati mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu usapangidwe kukhala wopanda pake. 18Pakuti mau a mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tinapulumutsidwa ndi mphamvu ya Mulungu8. 19Pakuti kwalembedwa, Ine ndidzawononga nzeru za anzeru, ndipo ndidzayika pambali kuzindikira kwa anthu ozindikira. 20Kodi wa nzeru ali kuti? Wozama ndi maphunziro ali kuti? Ali kuti wolitsutsa dziko lapansili? Kodi Mulungu9 sanayipange nzeru ya dziko lapansi kukhala yopusa? 21Pakuti kuyambira kale, mu nzeru ya Mulungu10, dziko lapansi mwa nzeru linamudziwa Mulungu11, Mulungu12 wasangalatsidwa ndi kupusa kwa kulalikira kupulumutsa iwo amene akhulupilira. 22Pakuti Ayuda amafuna zizindikiro, ndipo Ahelene amafuna nzeru; 23koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayuda chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chopusa; 24koma kwa iwo anayitanidwa, Ayuda ndi Ahelene omwe, Khristu mphamvu ya Mulungu ndi nzeru ya Mulungu. 25Chifukwa chopusa cha Mulungu13 ndi chanzeru kuposa anthu, ndipo chofooka cha Mulungu14 ndi champhamvu kuposa anthu. 26Pakuti ganizirani mayitanidwe anu, abale, kuti palibe ambiri anali anzeru molingana ndi kuthupi, siambiri anali amphamvu, siambili anali obadwa pa ulemelero. Koma Mulungu15 anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo Mulungu16 anasankha zinthu zofooka za dziko lapansi kuti akachititse manyazi zinthu zamphamvu; ndipo zinthu zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, Mulungu17 wazisankha, [ndipo] zinthu zimene palibe, kuti asukulutse zinthu zimene zilipo; kuti thupi lililonse lisadzitamandire pamaso pa Mulungu18. Koma chifukwa cha Iye inu muli mwa Khristu Yesu, amene anapangidwa kwa ife kukhala nzeru yochoka kwa Mulungu19, ndi kulungama, ndi chiyero, ndi chiombolo; kuti monga kunalembedwa, Iye wakudzitamandira, adzitamandire mwa Ambuye.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu16Elohimu17Elohimu18Elohimu19Elohimu