Mutu 25

1Pamenepo ufumu wakumwamba ufanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyali zawo, napita kukakumana ndi mkwati. 2Ndipo asanu a iwo anali ochenjera ndi asanu anali opusa. 3Iwo amene anali opusa anatenga nyali zawo koma sanazitengere mafuta; 4koma ochenjera anatenga mafuta m’zotengera ndi nyali zawo. 5Tsopano mkwati pakuchedwa, iwo onse anatopa ndipo anagona. 6Koma pakati pa usiku kunamveka kufuula, Taonani, mkwati; pitani mukakumane naye. 7Pamenepo anamwali onse anadzuka ndi kukonza nyali zawo. 8Ndipo opusawo anati kwa ochenjera, Tipatseniko mafuta anu, pakuti nyali zathu zikuzima. 9Koma ochenjera anayankha nati, [Ife sitingatero,] mwina sangatikwanire ife ndi inu. Pitani m’malo mwake kwa iwo amene amagulitsa, ndi kukazigulira nokha. 10Koma pamene iwo amapita kukagula, mkwati anafika, ndipo [iwo amene] anali okonzeka analowa naye pamodzi kuphwando la ukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa. 11Pambuyo pake anabweranso anamwali ena aja, nanena, Ambuye, Ambuye, titsegulireni ife; 12koma iye pakuyankha anati, Zoonadi ndinena kwa inu, Sindikudziwani inu. 13Khalani tcheru pakuti inu simudziwa tsiku lake ndi nthawi yake.

14Pakuti [zili] ngati [monga] munthu achoka kupita kudziko lakutali naitana akapolo ake nawapatsa iwo chuma chake. 15Ndipo kwa m’modzi iye anampatsa ndalama za matalente zisanu, kwa wina ziwiri, ndiponso kwa wina imodzi; aliyense anampatsa molingana ndi kuthekera kwake, ndipo nthawi yomweyo ananyamuka ulendo wake. 16Ndipo uyo amene analandira ndalama za matalente zisanu anapita kukachita nazo malonda, ndipo anapindula ndalama zina zisanu. 17Chimodzimodzinso iye amene [analandira] ziwiri, [nayenso] anapindula zina ziwiri. 18Koma iye amene analandira imodzi anapita ndipo anayikumbira pansi ndalamayo, ndipo anaibisira ndalamayo mbuye wake. 19Ndipo patapita nthawi yaitali mbuye wa akapoloyo anatulukira nawerengerana nawo. 20Ndipo iye amene analandira ndalama za matalente asanu anabwera kwa [iye] nabweretsa ndalama zina zisanu zoonjezera, nanena, Mbuye [wanga], ngakhale munandipatsa ine ndalama za matalente zisanu; taonani, ndapindulapo zina zisanu pamwamba pa izi. 21Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino ndi wokhulupirika, unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika iwe pa zinthu zochuluka: lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako. 22Ndipo uyonso amene analandira ndalama za matalente ziwiri anabwera kwa [iye] ndipo anati, Mbuye [wanga], inu munandipatsa ine ndalama ziwiri; taonani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri pamwamba pa izi. 23Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino ndi wokhulupirika, unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika iwe pa zinthu zochuluka: lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako. 24Ndipo uyonso amene analandira ndalama ya talente imodzi anabwera kwa [iye] ndipo anati, Mbuye [wanga], Ine ndinadziwa kuti ndinu munthu wouma mtima, mumakolola pamene simunadzale, ndi kusonkhanitsa pamene simunamwaze, 25ndipo pakuopa ine ndinapita ndi kubisa ndalama yanu ya talente mu nthaka; taonani, muli nacho ichi chimene chili chanu. 26Ndipo mbuye wake pakuyankha anati kwa iye, Kapolo woipa ndi waulesi iwe, unadziwa kuti ine ndimakololola pamene sindinafese, ndi kututa pamene sindinawaze; 27unayenerabe kuika ndalama yanga kwa okongola ndalama, ndipo pamene ndidzabwera ndidzapeze zimene zili zanga ndi phindu lake. 28Tengani pamenepo ndalamayo kwa iye, ndipo mupereke kwa iye amene ali nazo ndalama khumi: 29pakuti kwa aliyense amene ali nazo kudzapatsidwa, ndipo adzakhala nazo zochuluka; koma kwa iye amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ayesa kuti ali nacho. 30Ndipo mumponye kapolo wopanda pakeyu mu mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

31Koma pamene Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wake, ndi angelo onse ali naye, pamenepo adzakhala pansi pa mpando wa ulemerero wake, 32ndipo mafuko onse adzasonkhanira pa Iye; ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mzake, monga m’busa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; 33ndipo Iye adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, ndi mbuzi kudzanja [lake] lamanzere. 34Pamenepo Mfumu idzanena kwa iwo akukhala kudzanja lake lamanja, Bwerani, inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu ufumu wokonzedwera kwa inu kuchoka ku maziko ake a dziko lapansi: 35pakuti ndinali ndi njala, ndipo inu munandidyetsa Ine; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo inu munandichereza Ine; 36ndinali wa maliseche, ndipo munandiveka Ine; ndinadwala, ndipo munandichereza Ine; ndinali m’ndende, ndipo munadza kwa Ine. 37Pamenepo olungamawo adzamuyankha Iye nati, Ambuye, kodi tinakuonani liti wa njala, ndi kukudyetsani Inu; kapena wa ludzu, ndi kukumwetsani Inu? 38ndipo tinakuonani liti mlendo, ndi kukucherezani; kapena wa maliseche, ndi kukuvekani Inu? 39ndipo tinakuonani liti wodwala, kapena wa m’ndende, ndi kudza kwa Inu? 40Ndipo Mfumu pakuyankha adzanena kwa iwo, Zoonadi, Ine ndinena kwa inu, Pamene munachitira izi kwa m’modzi wa abale anga awa, munachitiranso Ine. 41Pamenepo Iye adzanenanso kwa iwo akudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine, otembereredwa inu, ndi kupita ku moto wamuyaya, wokonzedwera mdierekezi ndi amithenga ake: 42pakuti ndinali ndi njala, ndipo inu simunandipatse chakudya; ndinaIi ndi ludzu, ndipo simunandimwetse Ine; 43ndinali mlendo, ndipo inu simunandichereze Ine; wa maliseche, ndipo simunandiveke Ine; ndinali wodwala, ndi wa m’ndende, ndipo simunandiyendere Ine. 44Pamenepo iwo adzayankhanso nanena, Ambuye, kodi tinakuonani liti wa njala, kapena wa ludzu, kapena mlendo, kapena wa maliseche, kapena wodwala, kapena wa m’ndende, ndipo ife sitinakutumikireni Inu? 45Pamenepo Iye adzanena kwa iwo, Zoonadi ndinena kwa inu, Pamene simunachitire izi kwa ang’ono awa, ndiye kuti simunachitirenso Ine. 46Ndipo amenewa adzapita ku chilango chamuyaya, ndipo olungama ku moyo wosatha.