Mutu 15
1Koma ife tikuyenera, amene tili olimba, tinyamule zofooka za iwo amene ali opanda mphamvu, ndipo tisazisangalatse tokha.2Tiyeni aliyense wa ife asangalatse mnasi wake ndi machitidwe abwino, kulimbikitsana.3Pakutinso Khristu sanazisangalatse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene amakunyozani inu yandigwera Ine.4Pakuti monga zinthu zambiri zinalembedwa kale kutilangiza ife, kuti kudzera m’chipiliro ndi chilimbikitso cha malemba tikhale ndi chiyembekezo.5Tsopano Mulungu1 wa chipiliro ndi chilimbikitso akupatseni mukhale ndi malingaliro amodzi kwa wina ndi mzake, molingana ndi Khristu Yesu;6kuti ndi mtima umodzi, ndi kamwa limodzi, mulemekeze Mulungu2 ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.7Pamenepo mulandirane wina ndi mzake, monga Khristunso anakulandirani ku ulemelero wa Mulungu3.
8Pakuti ndinena kuti Yesu Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe pa choonadi cha Mulungu4, kutsimikizira malonjezano a makolo;9ndi kuti a mitundu alemekeze Mulungu5 chifukwa cha chifundo; monga kunalembedwa, Pa chifukwa ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa amitundu, ndipo ndidzayimbira dzina lanu.10Ndiponso anati, Sangalalani, amitundu, pamodzi ndi anthu ake.11Ndiponso, lemekezani Ambuye, inu nonse amitundu, ndipo anthu onse muyimbireni Iye.12Ndiponso, Yesaya akuti, padzaphuka muzu wa Yese, ndi Iye wakuuka kulamulira amitundu: mwa Iye amitundu onse adzakhala ndi chiyembekezo.13Tsopano Mulungu6 wa chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m’kukhulupilira, cholinga kuti mukachulukire m’chiyembekezo mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.
14Koma ine ndikutsimikizika, abale, ndi inenso mwini, zokhudza inu, kutinso inu eni mwadzala ndi ubwino, kudzazidwa ndi chidziwitso chonse, okhonzanso kulangizana wina ndi mzake.15Koma ndakulemberani inu molimba mtima, [abale,] mu mfundo zina, monga kukukumbutsani, chifukwa cha chisomo choperekedwa kwa ine ndi Mulungu7,16pakuti kwa ine kukhala mtumiki wa Khristu Yesu kwa amitundu, kunyamula monga nsembe ya utumiki [mau a] uthenga wabwino wa Mulungu8, cholinga kuti kupereka kwa amitundu kukhale kolandirika, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.17Pamenepo ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu mu zinthu zimene zikulunjika kwa Mulungu9.
18Pakuti ine sindidzayesera kulankhula kalikonse mwa zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine, pa kuzimvera amitundu, mwa mau ndi ntchito,19mu mphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa, mu mphamvu ya Mzimu wa Mulungu10; cholinga kuti ine, wochokera ku Yerusalemu, ndi kuzungulira ku Iluriko, ndalalikira mokwana uthenga wabwino wa Khristu;20ndipo chotero ndilakalaka kulalikira uthenga wabwino, osati kumene Khristu anadziwikako kale, kuti ndisamange pamwamba pa maziko ena;21koma molingana ndi momwe kunalembedwera, Kwa iwo amene kalikonse sikananenedwe kokhudza Iye, adzaona; ndipo iwo amene sanamve adzazindikira.22Pameneponso ndakhala ndikuletsedwa kuti ndisabwere kwa inu.23Koma tsopano, pokhala wopanda malo ku zigawo zino, ndi kukhala ndi chikhumbokhumbo chachikulu kubwera kwa inu kwa zaka zambiri,24pamene ndidzapita ku Spaniya; (pakuti ine ndikuyembekezera kukuonani pamene ndikudutsa, ndipo poperekezedwa pamenepo, poyamba ndidzakhutitsidwa ndi kukhala nanu pamodzi;)25koma tsopano ine ndipita ku Yerusalemu, kukatumikira oyera mtima;26pakuti aku Makedoniya ndi aku Akaya anali osangalala kupereka thandizo lina kwa osauka mwa oyera mtima amene ali mu Yerusalemu.27Iwo analidi osangalala, ndipo anali nawo ngongole; pakuti ngati amitundu atenga nawo gawo mu zinthu zawo za uzimu, akuyenera iwo kuwatumikiranso mu zinthu za kuthupi.28Pamenepo ndikamaliza izi, ndi kuwasindikiza iwo chipatso ichi, ndidzanyamuka kudutsa kwanuko popita ku Spaniya.29Koma ine ndikudziwa kuti, kubwera kwa inu, ndidzabwera ndi mdalitso onse wa Khristu.30Komatu ine ndikupemphani, abale, mwa Ambuye Yesu Khristu, komanso mwa chikondi cha Mzimu, kuti mulimbike nane pamodzi m’mapemphero kwa Mulungu11 chifukwa cha ine;31kuti ndipulumutsidwe kwa iwo amene sakhulupilira mu Yudeya; ndi kuti utumiki wanga umene ndili nawo pa Yerusalemu ulandiridwe kwa oyera mtima;32cholinga kuti ndikabwere kwa inu m’chimwemwe mwa chifuniro cha Mulungu12, ndi kuti ndidzapumule pamodzi ndi inu.33Ndipo Mulungu13 wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu