Mutu 4
1Tiyeni pamenepo tiope, kapena, likatsala lonjezo lakulowa mu mpumulo wake, aliyense wa inu akaoneka kuti analilephera. 2Pakutidi ife takhala nawo uthenga wabwino operekedwa kwa ife, monganso kwa iwo; koma mau operekedwa sanawapindulire, sanasakanizidwe ndi chikhulupiriro mwa iwo akuwamva. 3Pakuti ife tilowa mu mpumulo wa iwo okhulupirira; monga iye ananena, Monga ndinalumbira mu mkwiyo wanga, Ngati iwo adzalowa mu mpumulo wanga; ngakhale ntchito inatsirizika kuchokera pa maziko a dziko lapansi. 4Pakuti iye analankhula pena pake za tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti, Ndipo Mulungu1 anapuma patsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito zake zonse: 5ndipo m’menemonso, Ngati iwo adzalowa mu mpumulo wanga. 6Poona pamenepo patsala kuti ena akalowa m’menemo, ndipo iwo amene koyamba analandira uthenga wabwino sanathe kulowa pachifukwa chosamvera mau, 7iye anakhazikitsa tsiku lina, nanena, m’Davide, 'Lero,' patapita nthawi yaitali; (molingana ndi m’mene ananenera kale), Lero, ngati udzamva mau ake, usaumitse mtima wako. 8Pakuti ngati Yesu anawabweretsa iwo mu mpumulo, sakanalankhulanso pambuyo pake zokhudza tsiku lina. 9Pamenepo utsalira mpumulo wa sabata kwa anthu a Mulungu2. 10Pakuti iye amene alowa mu mpumulo wake, wapumanso ku ntchito zake, monga Mulungu3 anachitira pa iye yekha. 11Tiyeni ife pamenepo tigwiritse ntchito khama kulowa mu mpumulo umenewo, kuti wina asagwe mu chitsanzo chomwecho chosamvera mau. 12Pakuti mau a Mulungu4 ali amoyo ndi ochitachita, ndi akuthwa kuposa lupanga lakuthwa mbali zonse ziwiri, napsoza kugawanitsa moyo ndi mzimu, molumikizira mafupa ndiponso mafuta a m’mafupa, ndi kuzindikiritsa malingaliro zitsimikizo za mtima. 13Ndipo palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake; koma zinthu zonse zili za maliseche ndipo zili pa mbalambanda pamaso pake, ndi iye ifenso tikuyenera kuchita.
14Pokhala naye pamenepo mkulu wansembe wamkulu amene anadutsira m’miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu5, tiyeni tigwiritsitse chivomerezocho. 15Pakuti ife tilibe mkulu wansembe amene sakhoza kumva chifundo ndi zofooka zathu, koma anayesedwa mu zinthu zonse monga ife, koma opanda tchimo. 16Tiyeni ife pamenepo tiwandikire ndi chilimbiko ku mpando wachifumu wa chisomo, kuti tikalandire chifundo, ndi kupeza chisomo cha mnyengo yakusowa.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu