Mutu 5

1Pakuti zamveka ponsepo kuti pali chigololo pakati panu, ndipo chigololo chimene sichinachitikepo ngakhale pakati pa amitundu, kotero kuti wina agonana ndi mkazi wa atate wake. 2Ndipo inu mukhala odzitukumula, ndipo inu simunabume n’komwe, cholinga kuti amene wachita ichi akachotsedwe pakati panu. 3Pakuti ine, monga kuthupi kulibeko koma ndili nanu mu mzimu, ndaweruza kale monga ndili nanu, 4[kuweruza,] m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu (inuyo ndi mzimu wanga kusonkhana pamodzi, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu Khristu), iye amene wakonza ichi: 5kumpereka iye, ndinena wotereyu, kwa Satana kuti akaonongeke kuthupi, kuti mzimu ukapulumutsidwe m’tsiku la Ambuye Yesu. 6Kudzitukumula kwanu sikwabwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda onse? 7Chotsani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, molingana muli osatupitsidwa. Pakutinso pasaka wathu, Khristu, waperekedwa nsembe; 8kotero kuti tikakondwerere phwando, osati ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo ndi kuipa mtima, komatu ndi mkate wopanda chotupitsa woona mtima ndi choonadi.

ver>9Ndakulemberani m’kalata kuti musakhale pamodzi ndi anthu achigololo; 10osati pamodzi ndi achigololo adziko ili lapansi, kapena ndi osilira, ndi okwatula, kapena, opembedza mafano, kukanatero mukanangochoka padziko lapansili. 11Koma tsopano ndakulemberani inu, ngati wina wotchedwa m’bale akhala wachigololo, kapena wosilira, kapena wopembedza mafano, kapena wotukwana, kapena woledzera, kapena wolanda, musakhale naye pamodzi [iye]; wotereyu ngakhale musadye naye pamodzi. 12Pakuti ndipindulanji kuweruzanso iwo amene ali akunja? Musaweruze iwo amene ali pakati panu? 13Komatu iwo amene alibe Mulungu1 amaweruza. Chotsani woyipayo pakati panu.

1Elohimu