Mutu 19
1Zitapita zinthu izi ndinamva monga mau ofuula a khamu lalikulu m’mwamba, nanena, Aleluya: chipulumutso ndi ulemelero ndi mphamvu za Mulungu1 wathu: 2pakuti choonadi ndi kulungama [ndizo] chiweruzo chake; pakuti iye waweruza mkazi wa chigololo wamkulu amene naipsa dziko lapansi ndi chigololo chake, ndipo wabwezera mwazi wa akapolo ake kudzanja lake. 3Ndipo kachiwiri iwo anati, Aleluya. Ndipo utsi wake unakwera kwa nthawi za nthawi. 4Ndipo akulu makumi awiri ndi mphambu anayi ndi zolengedwa zamoyo anagwa pansi ndi kuchita malambiro kwa Mulungu2 wakukhala pa mpando wachifumu, nanena, Amen, Aleluya. 5Ndipo mau anatuluka ku mpando wachifumu, nanena, Alemekezeke Mulungu3 wathu, inu nonse akapolo ake, [ndi] inu amene mumuopa iye, ana ndi akulu.
6Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ndi ngati mkokomo wa madzi ochuluka, ndi ngati mau a mabingu amphamvu, nanena, Aleluya, pakuti Ambuye Mulungu4 wathu Wamphamvuzonse wazitengera yekha mphamvu za ufumu. 7Tiyeni tisangalale ndi kukondwera kwambiri, ndi kumpatsa iye ulemelero; pakuti ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wazikonzekeretsa yekha. 8Ndipo kunapatsidwa kwa iye kuti akavale chovala chabwino choyera, chowala [ndi] chopanda banga; pakuti chovala chabwino choyera ndiko kulungama kwa oyera mtima. 9Ndipo iye anati kwa ine, Lemba, odala [ali] iwo amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo iye anati kwa ine, Amenewa ndi mau oona a Mulungu5. 10Ndipo ndinagwa pansi pamapazi ake kumlambira iye. Ndipo iye anati kwa ine, Taona usachite ichi ayi. Ndine kapolo mzako, ndi [kapolo mnzawo] wa abale ako amene ali ndi umboni wa Yesu. Mlambire Mulungu6. Pakuti mzimu wa uneneri ndiwo umboni wa Yesu.
11Ndipo ndinaona kumwamba kutatseguka, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo wokhalapo pamenepo, [wotchedwa] Wokhulupirika ndi Woona, ndipo aweruza nachita nkhondo m’chilungamo. 12Ndipo maso ake ndiwo lawi la moto, ndipo pamutu pake panali nduwira zambiri, zokhala nalo dzina lolembedwa limene palibe akulidziwa koma iye mwini; 13ndipo wavala zovala zoviikidwa m’mwazi; ndipo dzina lake ndilo Mau a Mulungu7. 14Ndipo asilikali amene ali m’mwamba anamtsatira iye pa akavalo oyera, atavala zoyera, zopanda banga, chovala chabwino chopyapyala. 15Ndipo mkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa konsekonse, kuti ndi limenelo akakanthe mitundu; ndipo adzawaweta iwo ndi ndodo ya chitsulo; ndipo aponda moponderamo mpesa mwa nkwiyo waukulu wa Mulungu8 Wamphamvu. 16Ndipo iye ali nalo dzina lolembedwa, pa chovala chake, ndi pa ntchafu yake, Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa Ambuye.
17Ndipo ndinaona angelo atayima m’dzuwa; ndipo anafuula ndi mau okweza, nanena ku mbalame zonse zouluka pakati pa thambo, Bwerani, sonkhanani ku phwando lalikulu la Mulungu9, 18kuti mukadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo ndi ya iwo okhala pa iwo, ndi nyama ya onse, mfulu ndi akapolo omwe, ndi ana ndi akulu.
19Ndipo ndinaona chirombocho ndi mafumu adziko lapansi ndi asilikali awo atasonkhana pamodzi kuchita nkhondo kulimbana naye iye wakukhala pa kavaloyo, ndi asilikali ake. 20Ndipo chirombocho chinatengedwa, ndi mneneri wonyenga amene anali nacho pamodzi, amene anaonetsa naye zizindikiro zimene ananyenga nazo iwo akulandira chizindikiro cha chirombo, ndi iwo akulambira chifanizo chake. Amoyo onse anaponyedwa m’nyanja ya moto umene unayaka ndi sulfure; 21 ndipo otsalawo anaphedwa ndi lupanga la iye wakukhala pa kavalo, limene linatuluka mkamwa mwake; ndi mbalame zonse zinadzala ndi nyama zawo.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu