Mutu 1

1Paulo, mtumwi wa Yesu Khristu mwa chifuniro cha Mulungu1, ndi m’bale Timoteo, kwa mpingo wa 2Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali mu Akaya yense. 2Chisomo kwa inu, ndi mtendere zochokera kwa 3Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

3Alemekezeke 4Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo, ndi 5Mulungu wa chilimbikitso chonse; 4amene amatilimbikitsa ife m’masautso athu onse, kuti tikakhoze kulimbikitsa iwo amene ali m’masautso alionse, kudzera m’chilimbikitso chimene ife timalimbikitsidwa nacho mwa 6Mulungu. 5Chifukwa, ngakhale masautso a Khristu atichulukira ife, chomwechonso mwa Khristu chilimbikitso chathunso chichuluka. 6Komatu kaya muli m’masautso, chimenechi ndi chilimbikitso ndi chipulumutso chanu, chochititsa kupilira mwa chisautso chomwecho chimene ifenso tinadutsamo, 7(ndipo chiyembekezo chathu pa inu ndi choonadi;) kapena mwina ife tilimbikitsidwa, zili chomwecho chifukwa cha chilimbikitso ndi chipulumutso chanu: podziwa kuti monga inu mwatenga nawo gawo m’masautsowa, chimodzimodzinso mu chilimbikitso. 8Pakuti ife sitifuna kuti inu mukhale mbuli, abale, monga mwa m’sautso umene unationekera mu Asiya, kuti tinavutika kwambiri kuposera mphamvu zathu, kotero kuti tinada nkhawa za moyo wathu. 9Koma ife eni tinakhala nacho chitsutso cha imfa mkati mwathu, koma kuti tilimbike mwa 7Mulungu amene amaukitsa kwa akufa; 10amene anatiombola ife ku imfa yayikulu, natipulumutsa; mwa amene ife tiyembekezeranso kuti adzatipulumutsa; 11inunso muvutikira pamodzi nafe potipempherera kuti mphatso yobwera kwa ife, kudzera munjira ya anthu ambiri, ikakhala nkhani ya kuyamika kwa ambiri a ife. 12Pakuti kudzitamandira kwathu ndi uku, umboni wa chikumbumtima chathu, umene m’kudzichepetsa ndi nkuona konse pamaso pa 8Mulungu, (osati mu nzeru za kuthupi koma mu chisomo cha 9Mulungu,) ife takakhala tikukambitsana m’dziko lapansi, ndipo maka mochuluka pa inu. 13Pakuti ife sitilemba zinthu zina kwa inu koma zimene inu mukuzidziwa bwino ndi kuzizindikira; ndipo ndili ndi chiyembekezo kuti muzindikira chimenechi kufikira mapeto, 14ngakhale inu mwatizindikira ife mbali ina, kuti ndife chonyadira chanu, ngakhale kuti ndinu anthu athu m’tsiku la Ambuye Yesu. 15Ndipo ndi chilimbikitso chimenechi ndinafunitsitsa kubwera kwa inu kale, kuti mukakhale nako kukonderedwa kwachiwiri; 16ndipo podutsa panu kupita ku Makedoniya, ndiponso pochoka ku Makedoniya kubwera kwa inu, ndi kuperekezedwa ndi inu kupita ku Yudeya. 17Pamenepo pokhala ndi cholinga chimenechi, kodi sindinagwiritse ntchito kuunikiridwa? Kapena chimene ndinalinga, kodi ndinalinga ichi molingana ndi thupi, kuti mwa ine inde akhale inde ndipo ayi akhale ayi? 18Tsopano 10Mulungu ndi wokhulupirika, kuti mau athu kwa inu sakakhala inde ndi ayi. 19Pakuti Mwana wa 11Mulungu, Yesu Khristu, amene walalikidwa ndi ife pakati panu (walalikidwa ndi ine ndi Silvano ndi Timoteo), sanakhale inde ndi ayi, komatu inde ali mwa Iye. 20Pakuti malonjezano a 12Mulungu [alipo], mwa Iye ndi inde, ndipo mwa Iye Amen, pa ulemelero wa kwa 13Mulungu mwa ife. 21Tsopano Iye amene anatikhazikitsa ife ndi inu mwa Khristu, ndipo anatizodza ife, [ndiye] 14Mulungu, 22amenenso watisindikiza ife, ndipo anapereka chikole cha Mzimu m’mitima mwathu.

23Koma ine ndiyitana 15Mulungu kukhala mboni pa mzimu wanga pokusungani sindinabwere ku Korinto. 24Osati kuti tikuchita ulamuliro pa chikhulupiliro chanu, koma ndife antchito amzanu a chimwemwe chanu: pakuti mwa chikhulupiliro inu mwaima.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu8Elohimu9Elohimu10Elohimu11Elohimu12Elohimu13Elohimu14Elohimu15Elohimu