Mutu 2

1Tsopano atabadwa m’Betelehemu wa Yudeya, m’masiku a mfumu Herode, taonani anzeru a kum’mawa anafika ku Yerusalemu, nanena, 2Ali kuti mfumu ya Ayuda amene wabadwa? Pakuti taona nyenyezi yake kum’mawa, ndipo tabwera kudzamlambira Iye.

3Koma mfumu Herode pakumva [za ichi], anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye; 4ndipo, anasonkhanitsa pamodzi akulu ansembe onse ndi alembi a anthu, ndipo anafunsira kwa iwo kumene Khristu adzabadwira. 5Ndipo iwo ananena naye, ku Betelehemu wa Yudeya; pakuti kwalembedwa kudzera mwa mneneri: 6Ndipo iwe Betlehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wa nzeru zochepa pakati pa akulu a Ayuda ; pakuti wotsogolera adzachokera mwa iwe amene adzaweta anthu anga a Israyeli.

7Pamenepo Herode, anawaitana anzeruwo m’tseri, nawafunsisitsa iwo nthawi yeniyeni idaoneka nyenyeziyo; 8ndipo atawatumiza ku Betelehemu, ananena, pitani, kafufuzeni bwino zokhudza Mwanayo, ndipo pamene mwamupeza [Iye] mundibwezere mau, kuti nanenso ndikadze ndi kumlambira. 9Ndipo iwo pakumva mfumu anapita njira yawo; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum’mawa, inawatsogolera iwo kufikira inadza niyima pamwamba pamalo pamene panali Kamwanako. 10Ndipo pamene iwo anaona nyenyeziyo anasangalala ndi kukondwera kwambiri. 11Ndipo atalowa mnyumbamo iwo anaona Kamwanako ndi Mariya mayi wake, ndipo anagwa pansi namlambira. Ndipo atatsegula chuma chawo, anapereka kwa iye mphatso, golide, ndi libano ndi mure. 12Ndipo iwo pakulangizidwa mwa umulungu m’maloto kuti asabwerere kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwao pogwiritsa ntchito njira ina.

13Tsopano iwo, atachoka, taonani, mngelo [wa] Ambuye anaonekera m’maloto kwa Yosefe, nanena, Tauka, uzitengere [wekha] Kamwanako ndi mayi wake, ndipo uthawire ku Aigupto, ndipo ukakhale komweko kufikira Ine ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna Kamwanako kuti akaononge. 14Ndipo atauka, iye anadzitengera [yekha] Kamwanako ndi mayi wake usiku nathawira ku Aigupto. 15Ndipo anakhala kumeneko kufikira Herode atamwalira, kuti chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa ndi Ambuye mwa mneneri, kunena kuti, Kuchoka mu Aigupto ndinaitana mwana wanga. 16Pamenepo Herode, pakuona kuti wapusitsidwa ndi anzeruwo, anakwiya kwambiri; ndipo anatuma ena kukapha ana onse amuna amene [anali] mu Betelehemu, komanso m’malire ake, kuyambira a zaka ziwiri kutsika m’musi, molingana ndi nthawi imene iye anafufuza kwa anzeruwo. 17Pamenepo chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa ndi Yeremiya mneneri, kunena kuti, 18Mau anamveka m’Rama, kulira, ndi kubuma kwakukulu: Rakele kulilira ana ake, ndipo satheka kutonthozeka, chifukwa iwo palibepo.

19Komatu Herode atamwalira, taonani, mngelo wa Ambuye anaonekera m’maloto kwa Yosefe ku Aigupto, nanena, 20Nyamuka, zitengere [wekha] Kamwanako ndi mayi wake, ndipo upite mdziko la Israyeli: pakuti iwo amene amafuna moyo wa Kamwanako wafa. 21Ndipo ananyamuka natenga [iye] Kamwanako ndi mayi wake, nabwera m’dziko la Israyeli; 22koma pakumva kuti 'Arikelao analamulira pa Yudeya, m’malo mwa atate wake Herode,' anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pakulangizidwa mwa umulungu m’maloto, anapita ku magawo a Galileya, 23ndipo anabwera nakhala m’mudzi dzina lake Nazareti; kuti chikakwaniritsidwe chimene chinalankhulidwa kudzera mwa aneneri, Iye adzatchedwa Mnazarayo.