Mutu 5

1Ndipo anafika ku mbali ina ya nyanja, kudziko la Agerasa. 2Ndipo nthawi yomweyo pakutuluka Iye mungalawa anakumana naye munthu wotuluka kumanda wodzazidwa ndi mizimu yoipa, 3amene anayesa kumanda kokhalako kwake; ndipo palibe amene anakwanitsa kumumanga iye, ngakhale ndi unyolo; 4chifukwa iye amamangidwa kawirikawiri ndi matangaza ndi unyolo, ndipo maunyolo amamwetulidwa ndi iye ndi matangaza amadulidwa; ndipo palibe amene anatha kumgonjetsa iye. 5Ndipo mowirikiza usiku ndi usana, m’manda komanso m’mapiri, iye amafuula ndi kuzitematema yekha ndi miyala. 6Koma pakuona Yesu patali, anathamanga namgwadira Iye, 7ndipo pakufuula ndi mau okweza anati, Kodi ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu, Mwana wa Mulungu1 Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu mwa Mulungu2, kuti musandizunze ine. 8Pakuti anati kwa iye, Tuluka, mzimu woipa, mwa munthu uyu. 9Ndipo anamufunsa iye, Dzina lako ndani? Ndipo anati kwa Iye, Legio ndilo dzina langa, chifukwa tilipo ambiri. 10Ndipo anampempha Iye kwakukulu kuti asaitumize kunja kwa dziko. 11Tsopano panali pamenepo cha paphiri khamu lalikulu la nkhumba lili nkudya; 12ndipo zinamupempha Iye, zinena, Titumizeni ife mu nkhumbazo kuti tilowe mwa izo. 13Ndipo Yesu [nthawi yomweyo] anazilola. Ndipo mizimu yoipa potuluka inalowa mu nkhumba, ndipo khamulo linatsetserekera mwa liwiro ndi kulowa m’nyanja (pafupifupi zikwi ziwiri), ndipo zinatsamwa mnyanjamo. 14Ndipo iwo amene amadzidyetsa anathawa ndi kukanena ichi mu mzinda ndi m’dzikomo, Ndipo iwo anapita kukaona chimene chinachitikacho. 15Ndipo iwo anabwera kwa Yesu, ndipo anamuona wogwidwa ndi ziwanda uja atakhala pansi [ali] wovala komanso wanzeru zake, [iye] amene anali ndi legio uja: ndipo iwo anachita mantha. 16Ndipo iwo amene anachiona [ichi] anawafotokozera chimene chinachitika kwa [munthu] wogwidwa ndi ziwanda uja, komanso zokhudza nkhumba zija. 17Ndipo iwo anayamba kumupempha Iye kuti achoke ku malire awo. 18Ndipo pamene amapita kukakwera ngalawa, munthu amene anali wodzazidwa ndi ziwanda anamupempha Iye kuti akhale naye limodzi. 19Ndipo Iye sanamlole, koma anamuuza kuti, Pita kunyumba kwako kwa anthu ako, ndipo ukawauze iwo zimene Ambuye wakuchitira, ndi kuti anakuchitira chifundo iwe. 20Ndipo iye anachoka nayamba kulalikira ku Dekapoli m’mene Yesu anachitira zinthu zazikulu kwa iye; ndipo onse anali odabwa.

21Ndipo Yesu pamene anawoloka mu ngalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhanira kwa Iye; ndipo Iye anali m’mbali mwa nyanja. 22Ndipo [taonani] panadza wina wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo, ndipo pakumuona Iye, anagwa pansi pa mapazi ake; 23ndipo anampempha Iye kwambiri, nanena, Mwana wanga wamkazi wachichepere akuthatha; [Ndikupemphani] kuti Inu mukasanjike manja pa iye akachiritsidwe, ndi kukhala ndi moyo. 24Ndipo Iye anapita naye, ndipo khamu lalikulu linamulondola ndi kumukanikiza Iye.

25Ndipo munthu wina wa mkazi anali ndi nthenda ya nsambo wosalekeza kwa zaka khumi ndi ziwiri, 26ndipo anasautsika kwambiri pansi pa asing’anga ochuluka, ndipo anapereka chilichonse chimene anali nacho koma sanachire konse, koma matenda amangokulirakulira, 27atamva zokhudza Yesu, iye anafika mu khamu lija ndi kukhudza zovala zake; 28pakuti iye anati, Ngatitu nditangokhudza zovala zake ine ndidzachiritsidwa. 29Ndipo pomwepo kasupe wa magazi anaphwa, ndipo iye anadziwa mthupi mwake kuti anachiritsidwa ku chipweteko. 30Ndipo pomwepo Yesu, podziwa mwa Iye yekha mphamvu imene inachoka mwa Iye, potembenukira khamulo anati, Ndani amene wakhudza zovala zanga? 31Ndipo ophunzira ake anati kwa Iye, Kodi simukuona khamu likukupanikizani Inu, ndipo munena, Ndani wandikhudza Ine? 32Ndipo Iye anaunguzaunguza kufuna kuwona amene wachita ichi. 33Komatu mkaziyu, mwamatha ndi monjenjemera, podziwa zimene zachitika mwa iye, anabwera ndi kugwa pamaso pake, namuuza Iye choonadi chonse. 34Ndipo anati kwa iye, Mwana wa mkaziwe, chikhulupiliro chako chakuchiritsa iwe; pita mu mtendere, ndipo konzeka ku chipweteko chako.

35Adakali chilankhulire choncho, adafika iwo a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wanu wamwalira, chifukwa chiyani mukuvutitsabe Mphunzitsi? 36Koma Yesu [pomwepo], pakumva mau olankhulidwa, anati kwa mkulu wa sunagoge, Usachite mantha; ingokhulupilira kokha. 37Ndipo Iye sanalole wina aliyense kupita naye kupatula Petro ndi Yakobo, komanso Yohane m’bale wake wa Yakobo. 38Ndipo Iye anafika kunyumba kwa mkulu wa sunagoge, ndipo anaona chipiringu, ndi anthu akulira ndi kubuma kwakukulu. 39Ndipo pakulowa Iye anati kwa iwo, chifukwa chiyani mukubuma ndi kulira? Mwanayu sanafe, koma akugona. 40Ndipo iwo anamnyogodola Iye. Koma Iye, pamene anawatulutsa [iwo], anatenga atate wake wa mwanayo, ndi mayi wake, ndi iwo amene anali naye, ndipo analowa m’mene munagona mwanayo. 41Ndipo pamene anagwira dzanja la mwanayo, anati kwa iye, Talitha koumi, chimene chili, potanthauzira, Buthu, ndinena kwa iwe, Dzuka. 42Ndipo pomwepo buthulo linauka ndi kuyenda, pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo iwo anali odabwa ndi kudabwa kwakukulu. 43Ndipo Iye anawalamulira iwo kwakukulu kuti wina aliyense asadziwe ichi; ndipo anawauza kuti [kenakake] kaperekedwe kwa iye kuti adye.

1Elohimu2Elohimu