Mutu 13

1?Lolani chikondi cha pa abale chikhazikike. 2Musaiwale za kuchereza lendo; pakuti mwa ichi ena posadziwa anachereza angelo. 3Kumbukirani amndende, monga womangidwa nawo pamodzi; iwo ochitidwa nkhanza, monga inunso muli m’thupilo. 4[Lolani] banja [lisungidwe] mnjira zonse mwa ulemu, ndipo pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo Mulungu1 adzawaweruza. 5[Lolani kuti] zokamba zanu zisakhale zokonda chuma, mukhutitsidwe ndi zomwe muli nazo pano; pakuti iye anati, Ine sindidzakusiyani inu, kapena kukutayani inu. 6Chotero kuti, molimba mtima ife tinena, Ambuye ndiye mthandizi wanga, ndipo sindidzachita mantha: kodi munthu adzandichitira chiyani ine?

7Kumbukirani atsogoleri anu amene analankhula kwa inu mau a Mulungu2; ndipo poganizira zolankhula zawo, tsanzani chikhulupiliro chawo. 8Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi nthawi zikudza mtsogolomo. 9Musatengeke ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo; pakuti ndi kwabwino kuti mtima utsimikizike ndi chisomo, osati zakudya nyama; zomwe iwo akuyendamo sanapindule nazo. 10Ife tili nalo guwa limene alibe nalo ufulu wakudya iwo otumikira m’chihema; 11pakuti pa zilombo zimene mwazi wawo unatengedwa [monga nsembe ya tchimo] kulowa m’malo oyeretsetsa ndi mkulu wa ansembe, mwa zimenezi matupi awo anatenthedwa kunja kwa msasa. 12Pameneponso Yesu, kuti akawayeretse anthu ndi mwazi wake omwe, anazunzika kunja kwa chipata: 13chomwecho tiyeni tipite kwa iye kunja kwa msasa, kunyamula chitonzo chake: 14pakuti ife tilibe mzinda wokhalamo, koma tifunitsitsa wakudzayo. 15Mwa iyeyo pamenepo tiyeni tipereke kwa Mulungu3 nsembe ya mayamiko mosalekeza, imene ili, chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. 16Koma pochita zabwino ndi kugawira ena [zinthu zanu] musaiwale, pakuti ndi nsembe zotere Mulungu4 akondwera nazo bwino lomwe. 17Mverani atsogoleri anu, ndipo muwagonjere; pakuti iwo amayang’anira miyoyo yanu monga odzafotokozera za inu; kuti athe kuchita izi ndi chimwemwe, ndipo osati ndi kubuula, pakuti ichi chikhoza kukhala chopanda phindu kwa inu.

18Mutipempherere: pakuti ife tikakamizika tokha kuti tili nacho chikumbumtima chabwino, mu zinthu zonse kufuna kuyenda moyenera. 19Koma ine kwambiri ndikudandaulirani inu kuti muchite chimenechi, kuti mwachangu ndibwenzeretsedwe kwa inu.

20Koma Mulungu5 wa mtendere, amene anam’bweretsanso kuchoka kwa akufa Ambuye wathu Yesu, m’busa wamkulu wa nkhosa, mu [mphamvu ya] mwazi wa pangano la muyaya, 21akuyeretseni inu mu ntchito iliyonse pakuchita mwachifuniro chake, kuchita mwa inu chimene chili chosangalatsa pamaso pake kudzera mwa Yesu Khristu; kwa iye kukhale ulemelero kwa nthawi za nthawi. Amen. 22Koma ndikudandaulirani inu, abale, mubereke mau a chilimbikitso, pakuti ndalemba mau ochepa awa kwa inu.

23Dziwani kuti m’bale wathu Timoteyo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati atabwera posachedwapa, ndidzakuonani inu. 24Muwalonjere atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Iwo aku Italiya akulonjerani inu. 253 Chisomo chikhale ndi inu nonse. Amen.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu