Mutu 21
1Ndipo Iye anakweza maso naona anthu olemera akuponya zopereka zawo mosungiramo ndalama; 2koma Iye anaonanso mkazi wina wamasiye waumphawi akuponya momwemo timakobiri tiwiri. 3Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, kuti mkazi waumphawi uyu waponya zochuluka kuposa onse; 4pakuti onsewa mkuchuluka kwao aponya zopereka zawo [za Mulungu1]; koma iye mkusowa kwake wapereka zonse anali nazo za moyo wake.
5Ndipo pamene ena amakambirana za kachisi, kuti anakonzedwa ndi miyala yokongola ndi zopereka zopatulika, Iye anati, 6[Monga mwa] zinthu izi zimene mukuziona, masiku akubwera amene mwala sudzasiyidwa pamwamba pa mwala umzake umene sudzagwetsedwa. 7Ndipo iwo anamufunsa Iye nanena, Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti; ndipo chizindikiro chake ndi chiyani pamene zinthu zimenezi zizachitika? 8Ndipo Iye anati, Onetsetsani kuti musasocheretsedwe, pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, nanena, Ndine amene ali [Iye], ndipo nthawi ikuwandikira: [pamenepo] musawatsatire iwo. 9Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mipanduko, musachite mantha, pakuti zinthu zimenezi poyamba zikuyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike. 10Pamenepo Iye anati kwa iwo, Mtundu udzaukirana ndi mtundu, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu; 11padzakhala zivomezi zazikulu malo osiyanasiyana, ndi njala ndi miliri; ndipo padzakhala zinthu zoopsa ndi zizindikiro zochokera kumwamba. 12Koma zisanachitike izi adzakugwirani ndi kukuzunzani, adzakuperekani ku masunagoge ndi kundende, adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi akazembe pachifukwa cha dzina langa; 13koma chidzasanduka kwa inu ngati umboni. 14Chotero tsimikizani mu mtima mwanu kusalingaliratu chimene mudzayankha pa mlandu [wanu], 15pakuti Ine ndidzakupatsani kamwa ndi nzeru zimene otsutsana nanu sadzakwanitsa kuziyankha kapena kuzikana. 16Komatu mudzaperekedwa ngakhale ndi makolo ndi abale ndi alongo ndi amzanu, ndipo iwo adzakuphani [ena] mwa inu, 17ndipo adzakudani onse chifukwa cha dzina langa. 18Ndipo tsitsi limodzi la m’mutu mwanu mwanjira ina iliyonse silidzaonongeka. 19Mwa kupilira kwanu ipindula miyoyo yanu. 20Koma mukadzaona Yerusalemu wazingidwa ndi asilikali, dziwani kuti chiwonongeko chawandikira. 21Pamenepo iwo amene ali mu Yudeya athawire ku mapiri, ndipo amene ali mkati mwake atuluke, ndipo amene ali ku miraga asalowemo; 22pakuti amenewa ndiwo masiku akubwezera, kuti zinthu zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe. 23Koma tsoka kwa iwo akukhala ndi mwana ndi iwo akuyamwitsa m’masiku amenewo, pakuti padzakhala chionongeko chachikulu pa dziko ndi mkwiyo pa anthu amenewa. 24Ndipo iwo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, ndi kugwidwa ukapolo ku mitundu yonse; ndipo Yerusalemu adzapondedwa ndi amitundu kufikira nthawi ya amitundu itakwaniritsidwa. 25Ndipo padzakhala zizindikiro m’dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, ndipo dziko lonse mkuthedwa nzeru kwa amitundu pa mkokomo wake wa nyanja ndi kuwinduka kwa mafunde, 26anthu adzakonzekera kufa kudzera m’mantha ndi chiyembekezo cha zimene zikubwera padziko lokhalamo, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27Ndipo pamenepo iwo adzaona Mwana wa munthu akubwera m’mitambo ndi mphamvu ndi ulemelero waukulu. 28Komatu zinthu zimenezi zikadzayamba kuchitika, tukulani maso anu ndi kuyang’ana kumwamba, chifukwa chiombolo chanu chawandikira.
29Ndipo Iye analankhula fanizo kwa iwo: Taonani mtengo wa mkuyu ndi mitengo ina yonse; 30pamene iphuka, mumadziwa mwa inu nokha, [pa] kuiyang’ana [iyo], kuti dzinja lili pafupi. 31Chomwechonso inuyo, mukaona zimenezi zikuchitika, dziwani kuti ufumu wa Mulungu1 wayandikira. 32Zoonadi ndinena kwa inu, kuti m’badwo umenewu sudzachoka kufikira zonse izi zitachitika. 33Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma mau anga sadzapita. 34Koma ziyang’anireni nokha kuti kapena mwina mitima yanu ingalemetsedwe ndi maidyaidya ndi kuledzera ndi zosamalira za moyo, ndi kuti tsiku ilo lingadze kwa inu modzidzimutsa; 35pakuti ngati msampha lidzafika pa iwo onse akukhala pa nkhope ya dziko lonse lapansi. 36Chomwecho yang’anirani, ndi kupemphera nyengo zonse, kuti mukawerengedwe oyenera kuthawa zinthu zonse izi zimene zatsala pang’ono kukwaniritsidwa, ndi kuyima pamaso pa Mwana wa munthu.
37Ndipo masana amaphunzitsa m’kachisi, ndi usiku, amatuluka, Iye anatsalira pa phiri pomwepo lotchedwa la Azitona; 38ndipo anthu onse anabwera mamawa kwa Iye m’kachisi kudzamvera Iye.
1Elohimu2Elohimu