Mutu 4
1Koma Mzimu alankhula monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzachoka ku chikhulupiliro, kupereka malingaliro awo ku mizimu yonyenga ndi ziphunzitso za ziwanda 2kulankhula mabodza m’chinyengo, kulochedwa ngati chitsulo cha moto m’chikumbumtima chao chomwe, 3kuletsa ukwati, kusiyitsa kudya nyama, imene Mulungu1 anayilenga kuti tiyilandire ndi chiyamiko kwa iwo amene akhulupirika ndi kudziwa choonadi. 4Pakuti chilengedwe chilichonse cha Mulungu2 ndi chabwino, ndipo palibe choti chikanidwe, chilandiridwe ndi chiyamiko; 5pakuti chinayeretsedwa ndi mau a Mulungu3 ndipo momasuka chilankhula ndi iye. 6Poyikiza zinthu zimenezi pakati pa abale, iwe udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa ndi mau a chikhulupiliro ndi achiphunzitso chabwino chimene udachitsatira kwathunthu. 7Komatu chipongwe ndi nkhani zopanda pake za akazi okalamba uzipewe, koma uzizolowetse wekha mwa umulungu; 8pakuti chizolowezi cha thupi chipindulitsa kwa kanthawi, koma umulungu upindulitsa mu zonse, pokhala nalo lonjezano la moyo, umene ulipo pano, komanso umene uli nkudza. 9Mau ali okhulupirika ndi oyenera nkulandiridwa konse; 10pakuti, pachimenechi tigwiritsa ntchito ndi kupilira, chifukwa tiyembekezera mwa Mulungu4 wa moyo, amene ali wosunga anthu onse, makamaka iwo akukhulupilira. 11Ulamulire ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12Usalole munthu apeputse chinyamata chako, koma khala chitsanzo chabwino kwa okhulupirira, m’mau, m’chikhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’chiyero. 13Kufikira ndikabwera, udzipereke wekha m’kuwerenga, kulimbikitsa, kuphunzitsa. 14Usanyalapse za mphatso imene ili mwa iwe, imene inaperekedwa kwa iwe kudzera mwa uneneri, pamodzi ndi kuika manja kwa akulu. 15Udzadzidwe ndi zinthu zimenezi; ukhazikike kwathunthu m’zimenezi, kuti kuchita bwino kwako kuonekere kwa onse. 16 Udzipenyerere wekha ndi chiphunzitsocho; chipitilire mwa iwo; pakuti, pakuchita ichi, uzadzipulumutsa wekha ndi iwo akumvera iwe.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu