Mutu 1

1Chimene chinalipo kuyambira pachiyambi, chimene tinachimva, chimene tinachiona ndi maso athu; chimene tinachilangalira, ndipo manja athu anachigwira, chokhudza mau a moyo; 2 (ndipo moyo waonekera, ndipo tauona ndi kuchitira umboni, ndipo tilalikira kwa inu moyo wosathawo, umene unali ndi Atate, ndipo waonekera kwa ife:) 3kuti chimene tachiona ndi kuchimva tikulalikirani, kuti inunso mukakhale ndi chiyanjano pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilidi ndi Atate, ndi Mwana wake Yesu Khristu. 4Ndipo zinthu izi tikulemberani ife kwa inu kuti chimwemwe chanu chikhale chodzadza.

5Ndipo umenewu ndi uthenga umene tinaumva kuchokera kwa iye, ndipo tinalalikira kwa inu, kuti Mulungu1 ndiye kuunika, ndipo mwa iye mulibe mdima konse.

6Ngati ife tinena kuti tiyanjana ndi iye, ndipo tikhala mu mdima, tili abodza, ndipo sitikuchita choonadi.

7Koma ngati tiyenda m’kuwala monga iye ali kuunika, tili nacho ife chiyanjano wina ndi mzake, ndipo mwazi wa Yesu Khristu Mwana wake utitsuka ku machimo athu onse.

8Ngati tinena kuti ife tilibe tchimo, tizinyenga tokha, ndipo choonadi mulibe mwa ife.

9Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulipirika ndi wolungama iye kutikhululukira machimo [athu], ndi kutiyeretsa ku chosalungama chilichonse.

10 Ngati ife tinena kuti sitinachimwe, timpanga iye kukhala wabodza, ndipo mau ake mulibe mwa ife.

1Elohimu