Mutu 4

1M’menemo pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi anamva kuti Yesu akupanga komanso kubatiza ophunzira ambiri kuposera Yohane 2(komabe, Yesu mwini sanabatize, koma ophunzira ake), 3Iye anachoka ku Yudeya napitanso m’Galileya. 4Ndipo anafuna kudutsira ku Samariya. 5Pamenepo Iye anafika ku mzinda wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapereka kwa mwana wake Yosefe. 6Tsopano chitsime cha Yakobo chinali pamenepo; Pomwepo Yesu, atatopa ndi ulendo umene anayenda, anakhala pa chitsimecho. Inali ngati ola lachisanu ndi chimodzi. 7Mkazi wina anatuluka m’Samariya kudzatunga madzi. Yesu anati kwa iye, Undipatse Ine ndimwe 8 (pakuti ophunzira ake anali atapita mu mzinda kukagula chakudya). 9Pamenepo mkazi wa ku Samariya anati kwa Iye, Zitheka bwanji inu, wokhala m’Yuda, mupempha madzi kwa ine mkazi waku Samariya? Pakuti Ayuda sayenderana ndi Asamariya. 10Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mphatso ya Mulungu1, ndikuti ndi ndani amene akunena kwa iwe, Undipatse Ine ndimwe, ukanapempha kwa Iye, ndipo Iye akanakupatsa iwe madzi amoyo. 11Mkaziyo anati kwa Iye, Ambuye, inu mulibe chotungira madzi, ndipo chitsimechi ndi chakuya: pamenepo mudzawatenga kuti madzi amoyo? 12Kodi ndinu wamkulu kuposa atate wathu Yakobo, amene anatipatsa ife chitsimechi, ndipo iye mwini anamweranso pa chimenechi, ndi ana ake amuna, ndi ng’ombe zake? 13Yesu anayankha nati kwa iye, Aliyense amene adzamwa madzi awa adzamvanso ludzu; 14koma aliyense wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamvanso ludzu kwamuyaya, komatu madzi amene ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi, wakutumphuka m’moyo wosatha. 15Mkaziyo anati kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amenewa, kuti ndisadzamvenso ludzu kapena kubwera kuno kudzatunga madzi. 16Yesu anati kwa iye, Pita, ukayitane mwamuna wako, ndipo ubwere kuno. 17Mkaziyo anayankha nati, Ndilibe mwamuna ine. Yesu anati kwa iye, Wanena bwino, ndilibe mwamuna; 18pakuti unali nawo amuna asanu, ndipo amene uli naye pano simwamuna wako: ichi wanena zoona. 19Mkaziyo anati kwa Iye, Ambuye, Ndaona kuti ndinu mneneri. 20Makolo athu analambira m’phiri ili, ndipo Inu mukuti m’Yerusalemu ndi malo amene munthu akuyenera kulambira. 21Yesu anati kwa iye, Mkaziwe, khulupilira Ine, ola likubwera limene simudzalambira Atate m’phiri ili kapena m’Yerusalemu. 22Inu mumalambira chimene simuchidziwa; ife timalambira chimene timachidziwa, pakuti chipulumutso ndi cha Ayuda. 23Komatu ola likubwera ndipo lafika, pamene olambira enieni adzamlambira Atate mu mzimu ndi m’choonadi; pakutinso Atate afuna otere kuti akhale omlambira ake. 24Mulungu2 [ndi] mzimu; ndipo iwo akumlambira Iye amlambire mu mzimu ndi choonadi. 25Mkaziyo anati kwa Iye, Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera, amene akutchedwa Khristu; pamene Iye adzabwera adzatiuza zinthu zonse. 26Yesu anati kwa iye, Ine amene ndikulankhula ndine amene ndili. 27Ndipo pamwamba pa izi ophunzira ake anabwera, ndipo anali odabwa kuti Iye amalankhula ndi mkazi; komabe palibe amene ananena, Ukufuna chiyani? kapena, Chifukwa chiyani mumalankhula ndi iye?

28Mkaziyo anasiya mtsuko wake wa madzi napita mu mzinda, ndipo anati kwa anthu, 29Bwerani, mudzaone munthu amene wandiuza zinthu zonse ndinazichita: kodi ameneyu si Khristu? 30Iwo anatuluka mu mzinda nabwera kwa Iye.

31Koma nthawi imeneyi ophunzira anamufunsa Iye nanena, Rabi, idyani. 32Koma Iye anati kwa iwo, Ndili nacho chakudya chimene inu simuchidziwa. 33Pamenepo ophunzira anati kwa wina ndi mzake, Alipo wina amene anamubweretsera Iye [kalikonse] kakudya? 34Yesu anati kwa iwo, Chakudya changa ndiko kuti ndikachite chifuniro cha Iye amene anandituma, ndi kuti ndikatsirize ntchito yake. 35Kodi inu simunena, kuti yatsala miyezi inayi ndipo kukolola kufika? Taonani, ndinena kwa inu, Tukulani maso anu ndipo taonani m’munda, pakuti zokolola zacha. 36Iye amene akolola alandira malipiro ndipo asonkhanitsa zipatso m’moyo wosatha, kuti onse iye amene afesa ndi wokolola akasangalale pamodzi. 37Pakuti mu ichi [chatsimikizika] chonenedwa choonadi, Ali wina wakufesa ndi winanso wokolola. 38Ine ndatumiza inu kukolola zimene simunagwirire ntchito; ena agwirira ntchito, ndipo inu mwalowa mu ntchito yawo.

39Koma ambiri a Asamariya a mumzindamo anakhulupilira pa Iye chifukwa cha mau a mkazi amene anamuchitira umboni, Iye wandiuza zinthu zonse ndinazichita. 40Kotero pamene Asamariya anabwera kwa Iye anamfunsa Iye akhale ndi iwo, ndipo anakhala kumeneko masiku awiri. 41Ndipo ambiri oposa anakhulupilira pa mau ake; 42ndipo iwo anati kwa mkaziyo, Sichifukwanso chakuti unalankhula kuti ife takhulupilira, pakuti tamumva Iye tokha, ndipo tikudziwa kuti ameneyu ndi mpulumutsi wa dziko lapansi.

43Koma pakutha pa masiku awiri Iye anachoka kumeneko napita m’Galileya, 44pakuti Yesu mwini anachitira umboni kuti mneneri salemekezedwa m’dziko lake lomwe. 45Pamene tsono Iye anabwera m’Galileya, Agalileya anamlandira Iye, pakuona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu nthawi ya phwando, pakutinso iwo anapita ku phwandoko.

46Iye anabweranso pamenepo ku Kana wa Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo panali munthu wina wa mfumu m’Kapernao amene mwana wake anadwala. 47Iye, pakumva kuti Yesu anatuluka mu Yudeya kulowa m’Galileya, anapita kwa Iye namfunsa kuti apite naye ndi kuchiritsa mwana wake, pakuti anatsala pang’ono kumwalira. 48Pamenepo Yesu anati kwa iye, Pokhapokha utaona zizindikiro ndi zozizwa sungakhulupilire. 49Mkuluyu anati kwa Iye, Ambuye, tsikani mwana wanga akufa. 50Yesu anati kwa iye, Pita, mwana wako ali ndi moyo. Ndipo munthuyu anakhulupilira mau amene Yesu ananena kwa iye, napita njira yake. 51Komatu pamene ananyamuka kale, akapolo ake anakumana naye nam’bweretsera mau nanena, Mwana wanu ali ndi moyo. 52Iye anafufuza pamenepo kwa iwo ola limene iye anachira. Ndipo iwo anati kwa iye, Dzulo pa ola lachisanu ndi chiwiri malungo anamusiya. 53Pamenepo atatewo anadziwa kuti inali ola limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo iye anakhulupilira, iye mwini ndi nyumba yake yonse. 54Chizindikiro ichi chachiwiri anachitanso Yesu, atachoka ku Yudeya kupita m’Galileya.

1Elohimu2Elohimu