Mutu 4

1Ndipo anayambanso kuphunzitsa mphepete mwa nyanja. Ndipo khamu lalikulu linasonkhanira kwa Iye, kotero kuti pakulowa m’ngalawa anakhala m’nyanja, ndipo khamu lonse linaima kumtunda pafupi ndi nyanjayo. 2Ndipo Iye anawaphunzitsa iwo zinthu zambiri m’mafanizo. Ndipo Iye analankhula nawo m’chiphunzitso chake, 3Mverani: Taonani, wofesa anapita kukafesa. 4Ndipo kunachitika kuti pamene amafesa, zina zinagwera m’mbali mwanjira, ndipo mbalame zinabwera ndi kudya. 5Ndipo zina zinagwera pa nthaka ya mwala, pamene panalibe dothi lambiri, ndipo pomwepo zinamera [pa nthakapo] chifukwa panalibe dothi lakuya; 6ndipo pamene dzuwa linakwera zinapserera, ndipo chifukwa chakuti zinalibe mizu, zinafota. 7Ndipo zina zinagwera pakati pa minga, ndipo minga inakula ndi kutsamwitsa izo, ndipo sizinabereke chipatso. 8Ndipo zina zinagwera mu nthaka yabwino, ndi kubereka chipatso, pakukula ndi kuchuluka; ndipo zinabereka, china makumi atatu, ndi china makumi asanu ndi limodzi, ndi china zana limodzi. 9Ndipo Iye anati, Amene ali nawo makutu akumva, amve. 10Ndipo pamene Iye anali payekha, iwo amene anamzungulira Iye pamodzi ndi khumiwo anamfunsa Iye [zokhudza] mafanizowo. 11Ndipo Iye anati kwa iwo, Kwa inu kwapatsidwa [kudziwa] zinsinsi za ufumu wa Mulungu1; koma kwa iwo amene ali kunja, zonse zimachitidwa m’mafanizo, 12kuti pakupenya apenye koma asaone, ndi pakumva amve koma asazindikire, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa. 13Ndipo anati kwa iwo, Kodi inu simudziwa za fanizo limeneli? Ndipo nanga mukazindikiritsidwa bwanji ndi mafanizo onsewa? 14Wofesa anafesa mau: 15ndipo awa ndiwo a m’mbali mwanjira m’mene mau afesedwa, ndipo pamene amva, nthawi yomweyo Satana amabwera ndi kutenga mau amene anafesedwa mwa iwo. 16Ndipo awa ndiwo amene chimodzimodzi afesedwa pa nthaka ya mwala, amene pakumva mau, mwachangu amawalandira ndi chimwemwe, 17ndipo amakhala opanda mizu mwa iwo okha, koma akhala mwa kanthawi: pomwepo, masautso akadza, kapena mazunzo chifukwa cha mau, nthawi yomweyo amakhumudwa. 18Ndipo enawo ndiwo ofesedwa pakati pa minga: amenewa ndiwo akumva mau, 19ndipo malabadiro a moyo, ndi chinyengo cha chuma, ndi zikhumbokhumbo za zinthu zina, zimalowa mkati, ndi kutsamwitsa mau, ndipo umakhala wosabereka chipatso. 20Ndipo awa ndiwo akufesedwa pa nthaka yabwino, kotero kuti akamva mau ndi kuwalandira, amabereka chipatso; china makumi atatu, ndi china makumi asanu ndi limodzi, ndi china zana limodzi. 21Ndipo Iye anati kwa iwo, Kodi nyali imabwera kuti ivundikiridwe pansi pa mbiya kapena pansi pa kama? [Kodi imeneyi] simaikidwa pa choikapo chake? 22Pakuti palibe chobisika chimene sichidzaululika; kapena kalikonse kochitika mseri, koma kadzabwera poyera. 23Ngati wina ali nawo makutu akumva, amve. 24Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang’anirani chimene inu mwamva; pakuti ndi muyeso umene muyesera ena, udzayesedwanso kwa inu; ndipo zidzaonjezedwa [kwambiri] kwa inu. 25Pakuti kwa amene ali nazo, kwa iye kudzapatsidwa; ndipo iye amene alibe, ngakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.

26Ndipo Iye anati, Chomwechonso ufumu wa Mulungu2, monga munthu wakuponya mbeu mu nthaka, 27ndipo agona ndi kuuka usiku ndi usana, ndipo mbeu pakuphuka ndi kukula, iye samadziwa kuti zachitika bwanji. 28Nthaka imabereka zipatso payokha, choyamba m’mera, kenako ngala, kenako ngala yaphumphu yokhwima. 29Komatu pamene chipatso chicha, nthawi yomweyo iye amatumiza zenga, pakuti zokolola zafika. 30Ndipo Iye anati, Kodi ufumu wa Mulungu3 tiufanizira chiyani, kapena tizaulinganiza ndi fanizo lotani? 31Monga [mbeu] ya mpiru, imene, pofesedwa mu nthaka, ikhala yochepa pa mbeu zonse zimene zili pa nthaka, 32ndipo pamene zafesedwa, imera ndi kukhala yaikulu kuposa zitsamba zonse, ndi kutulutsa nthambi zikuluzikulu, kotero kuti mbalame za mlengalenga ziutsa pa mthunzi wake. 33Ndi mafanizo ochuluka otere Iye analankhula nawo, pakuti iwo anakwanitsa kumva, 34koma popanda mafanizo Iye sanalankhule ndi iwo; ndipo mseri Iye amawafotokozera zinthu zonse ophunzira ake.

35Ndipo tsiku limenelo, pamene madzulo anafika, Iye anati kwa iwo, Tiyeni tiwolokere kutsidya linalo: 36ndipo atalichotsa khamulo, anatengana naye pamodzi ndi [iwo], pakuti Iye anali mungalawa. Komatu ngalawa zinanso zinali naye pamodzi. 37Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndipo mafunde anagavira mungalawa, kotero kuti inayamba kudzala. 38Ndipo Iye anali kugona tulo tatikulu pa mtsamiro. Ndipo iwo anamudzutsa nati kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti tikuonongeka? 39Ndipo pakuuka Iye anadzudzula mphepoyo, ndipo analankhula kwa nyanja, Tonthola; khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo panali bata lalikulu. 40Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chiyani muli ndi mantha [choncho]? Bwanji kuti [zili chonchi] kuti mulibe chikhulupiriro? 41Ndipo iwo anachita mantha [ndi] mantha akulu, ndipo anati kwa wina ndi mzake, Ndani uyu, kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

1Elohimu2Elohimu3Elohimu