Mutu 11

1Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake, 2ndipo anati kwa iwo, Pitani m’mudzi umene wayang’anizana ndi inu, ndipo pomwepo pamene mukalowamo mukapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe [mwana] wa munthu anakhalapo: m’masuleni ndipo mubwere naye [kuno]. 3Ndipo ngati aliyense akanena kwa inu, Muchitiranji ichi? nenani, Ambuye akumfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza. 4Ndipo iwo ananyamuka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo kunja kwa khwalala, ndipo iwo anam’masula. 5Ndipo ena mwa iwo akuimilira pamenepo anati kwa iwo, Kodi mukuchita chiyani, mukumasula mwana wa bulu? 6Ndipo anati kwa iwo monga anawalamulira Yesu. Ndipo iwo anawaleka [kuchita ichi]. 7Ndipo iwo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, ndipo anaika zovala zawo pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo; 8ndipo ambiri anayala zovala zawo panjira, ndi ena anadula nthambi za mitengo [ndipo anaziyala panjira]. 9Ndipo iwo akutsogolera ndi iwo otsatira anafuula, Hosana! Wodala [akhale] iye wakudza m’dzina la Ambuye. 10Wodala [ukhale] ufumu ulinkudza wa atate wathu Davide. Hosana m’mwambamwamba! 11Ndipo Iye analowa m’Yerusalemu ndi m’kachisi; ndipo ataunguza zinthu zonse, popeza anali madzulo, Iye anapita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

12Ndipo m’mawa mwache, pamene iwo anapita ku Betaniya, Iye anamva njala. 13Ndipo pakuona chapatali mtengo wa mkuyu umene unali ndi masamba, Iye anafika, kuti kapena apeza kenakake pa iwo. Ndipo pakufika pa iwo sanapeza kanthu koma masamba okha, pakuti sinali nyengo ya mkuyu. 14Ndipo pakuyankha anati kwa iwo, Sadzapezekanso munthu wakudya chipatso mwa iwe nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva za [ichi].

15Ndipo anadza ku Yerusalemu, ndipo pakulowa m’kachisi, Iye anayamba kutulutsa iwo amene amagulitsa ndi kugula m’kachisimo, ndipo Iye anagubuduza magome a anthu osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, 16ndipo sanalole kuti wina aliyense anyamule katundu kulowetsa m’kachisimo. 17Ndipo Iye anawaphunzitsa nati kwa iwo, Kodi sikunalembedwe, nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya kupemphereramo kwa anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba. 18Ndipo ansembe akulu ndi alembi anamva za [ichi], ndipo anafuna njira m’mene angamuwonongere Iye; pakuti iwo amamuopa Iye, chifukwa khamu lonse linali lozizwa ku chiphunzitso chake. 19Ndipo pamene anafika madzulo anatuluka Iye m’mudzi.

20Ndipo podutsa m’mamawa zedi iwo anaona mkuyu uja utauma kuyambira ku mizu. 21Ndipo Petro, pakukumbukira [zimene Yesu anayankhula], anati kwa Iye, Rabi, taonani, mtengo wa mkuyu umene Inu munautemberera wauma. 22Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Khalani ndi chikhulupiliro mwa Mulungu1. 23Zoonadi ndinena kwa inu, kuti aliyense wakunena kwa phiri ili, Chotsedwa ndipo uponyedwe m’nyanja, ndipo wosakayika mu mtima mwake, koma kukhulupilira kuti chimene alankhula chidzachitika, chilichonse chimene adzalankhula chidzachitika kwa iye. 24Pachifukwa ichi ndinena kwa inu, Zinthu zonse zimene mupempherera ndi kupempha, khulupilirani kuti mudzalandira, ndipo zidzachitika kwa inu. 25Ndipo pamene muimilira ndi kupemphera, khululukirani ngati muli nako kanthu kotsutsana ndi wina, kuti Atate wanunso amene ali kumwamba akukhululukireni zolakwa zanu. 26Koma ngati inu simukhululukira, Atate wanunso amene ali kumwamba sangakukhululukireni zolakwa zanu.

27Ndipo iwo anafikanso ku Yerusalemu. Ndipo pamene anali kuyenda m’kachisi, ansembe akulu ndi alembi ndi akulu anabwera kwa Iye, 28ndipo iwo anati kwa Iye, Mumachita izi ndi ulamuliro wa ndani? Ndipo ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu? 29Ndipo Yesu poyankha anati kwa iwo, Inenso ndikufunseni kanthu kamodzi, ndipo mundiyankhe, ndipo ndikuuzani kuti ndimapanga zonse izi pa ulamuliro wa ndani: 30Ubatizo wa Yohane, unali wakumwamba, kapena wa anthu? Ndiyankheni. 31Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Ngati tinganene kuti, Wakumwamba, Iye atifunsa, Nanga [bwanji] simunamkhulupilire iye? 32komanso tikanena kuti, Wa anthu — iwo anaopa anthu; pakuti onse anamva za Yohane kuti analidi mneneri. 33Ndipo iwo poyankha anati kwa Yesu, Sitikudziwa. Ndipo Yesu [poyankha] anati kwa iwo, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimapangira zonsezi.

1Elohimu