Mutu 16

1Ndipo sabata litapita [tsopano], Mariya wa Magadala, ndi Mariya [amake] a Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira kuti akadze ndi kumdzodza Iye. 2Ndipo m’bandakucha wa [tsiku] loyamba la sabata anadza kumanda wosemawo, dzuwa litatuluka. 3Ndipo iwo anati kwa wina ndi mzake, Ndani amene adzatikunkhunizira mwala pa khomo la manda? 4Ndipo pamene iwo anayang’ana, anaona kuti mwala unali wokunkhunizidwa, pakuti unali waukulu kwambiri. 5Ndipo pakulowa m’mandamo, iwo anaona mnyamata atakhala mbali ya dzanja lamanja, atavala mwinjiro woyera, ndipo iwo anali odabwa ndi odzidzimuka; 6koma iye anati kwa iwo, musadzidzimuke. Mukufuna Yesu, Mnazarayo, wopachikidwa. Iye wauka, sali muno; taonani malo amene iwo anamuika. 7Komatu pitani, kauzeni ophunzira ake ndi Petulo, Iye watsogola kale kupita m’Galileya; kumeneko inu mudzamuona Iye, monga ananenera kwa inu. 8Ndipo iwo anatuluka, nachokako kumandako. Ndipo mantha ndi kudabwa kwakukulu zinawagwira iwo, ndipo sanalankhule kanthu kwa wina aliyense, pakuti anali ndi mantha.

9Tsopano pamene Iye anauka m’bandakucha, [tsiku] loyamba la sabata, anawonekera koyamba kwa Mariya wa Magadala, amene mwa iye anatulutsamo ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10Iye anapita ndi kubweretsa mau kwa iwo amene anali ndi Iye, [amene anali] kubuma ndi kulira. 11Ndipo pamene awa anamva kuti Iye ali ndi moyo ndipo wawonedwa ndi iye, sanakhulupilire [chimenechi]. 12Ndipo zitapita zimenezi Iye anaonekera mwa mtundu wina kwa awiri mwa iwo pamene iwo anali kuyenda, kulowa m’mudzi; 13ndipo iwo anapita nabweretsa mau kwa ena aja; awanso iwo sanawakhulupilire. 14Pomwepo pamene iwo anali kuseyama pa gome Iye anaonekera kwa khumi ndi m’modziwo, ndipo anawadzudzula [iwo ndi] kusakhulupilira kwawo ndi kuuma kwa mtima, chifukwa sanakhulupilire iwo amene anamuona Iye ataukitsidwa. 15Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani dziko lonse lapansi, ndi kulalikira uthenga wabwino kwa olengedwa onse. 16Iye wakukhulupilira ndi kubatizidwa adzapulumuka, ndipo amene sakhulupilira adzaweruzidwa. 17Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupilira: m’dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malilime atsopano; 18adzatola njoka; ndipo ngati adzamwa kanthu kakufa nako sikadzawapweteka iwo; adzaika manja pa odwala ndipo iwo adzakhala bwino.

19Pomwepo Ambuye, atamaliza kulankhula kwa iwo, anatengedwa kupita kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu1. 20Ndipo iwo, pakupita, analalikira konseko, Ambuye nachita nawo [iwo], ndi kutsimikizira mau ndi zozizwa zotsatira mauwo.

1Elohimu