Mutu-2

1Chomwecho iwe, mwana wanga, khala wolimba m’chisomo chimene chili mwa Khristu Yesu. 2Ndi zinthu zimene wamva za ine pamaso pa mboni zambiri, zimenezi uyikize kwa anthu okhulupirika, oterewa adzakhoza kuphunzitsanso ena. 3Utenge gawo lako m’kumva zowawa monga msilikali wabwino wa Yesu Khristu. 4Palibe amene amakhala msilikali nakodwa yekha ndi zochitika za moyo, kuti akasangalatse amene anamulemba ntchito ya usilikali. 5Ndiponso ngati wina atenga nawo gawo [mu mpikisano], samalandira mphoto pokhapokha ngati apikisana nawo monga mwa lamulo. 6Mlimi akuyenera kugwiritsa ntchito asanadye zipatsozo.

7Ganizira chimene ndanena, pakuti Ambuye adzakupatsa iwe kumvetsetsa mu zinthu zonse. 8Kumbukira Yesu Khristu anaukitsidwa pakati pa akufa, wa mbewu ya Davide, kolingana ndi uthenga wanga wabwino, 9umene ine ndinazunzikamo kufikira kumangidwa monga wochita zoipa: koma mau a Mulungu1 samangika. 10Pachifukwa chimenechi ndipilira m’zinthu zonse chifukwa cha iwo osankhika, kuti iwo akapezenso chipulumutso chimene chili mwa Khristu Yesu ndi ulemelero wamuyaya. 11Mau ali okhulupirika; ngatitu ife tinafa pamodzi ndi [iye], tidzakhalanso pamodzi; 12ngati ife tipilira, tidzalamuliranso pamodzi; ngati timkana, iyenso adzatikana ife; 13ngati tili okhulupirika, iye akhala wokhulupirika, pakuti sangazikane yekha.

14Pa zinthu zimenezi uwakumbutse, kuchitira umboni modzipereka pamaso pa Ambuye kuti asatsutsane m’mau, osapindulitsa kanthu, kusokoneza iwo akumva. 15Ulimbike kwambiri kudzionetsera wekha wovomerezeka kwa Mulungu2, wantchito amene sakuyenera kuchita manyazi, kulankhula mwachindunji mau achoonadi. 16Koma upewe, nkhani zopanda pake, pakuti zitsogolera ku kunyozetsa kwakukulu, 17ndipo mau awo adzabuka ngati chiphunzitso chonyenga; amene mwa iwo ndi Humenayo ndi Fileto; 18[amuna] amene monga mwa choonadi adasokera, kunena kuti chiukitso chachitika kale; ndi kupasula chikhulupiriro cha ena. 19Komabe maziko olimba a Mulungu3 ayimabe, pokhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye awadziwa iwo amene ali ake; ndipo, aliyense amene atchula dzina la Ambuye adzipatule ku choipa. 20Komatu mnyumba yayikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komanso za matabwa ndi dongo; ndipo zina za ulemu, ndi zina zopanda ulemu. 21Ngatitu pamenepo munthu adziyeretsa yekha ku izi, [kudzipatula yekha ku zimenezi], adzakhala chotengera cha ulemu, chopatulidwa, chogwiritsidwa ntchito ndi Mbuye, chokonzedwa kukachita ntchito iliyonse yabwino. 22Koma uthawe zilakolako za unyamata, ndipo utsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, ndi onse amene ayitanira pa Ambuye ndi mtima wangwiro. 23Koma upewe mafunso opusa ndi opanda pake, podziwa kuti amabweretsa mikangano. 24Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kukangana, koma akhale wodzichepetsa kwa onse; wokhoza kuphunzitsa; wopilira; 25m’kufatsa aonetsere choonadi iwo amene ali otsutsa, ngati mwina Mulungu4 akhoza kuwapatsa mwayi olapa kukadziwa choonadi, 262 ndi kuti iwo akadzuke ndi kudzipulumutsa ku msampha wa mdierekezi, [ameneyo iwo] anatengedwa naye, ku cholinga chake.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu