Mutu 17
1Ndipo m’modzi wa angelo asanu ndi awiri aja, amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri, anabwera ndipo analankhula ndi ine, nanena, Bwera kuno, ndikuonetsa chigamulo cha mkazi wa chigololo wamkulu amene akhala pamadzi ambiri; 2amene mafumu adziko lapansi anachita naye chigololo; ndipo iwo akukhala padziko lapansi analedzeretsedwa ndi vinyo wa chigololo chake. 3Ndipo iye ananditenga mu mzimu kupita ku chipululu; ndipo ndinaona mkazi wakukhala pa msana pa chirombo chofiira, odzala ndi maina a mwano, wokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4Ndipo mkaziyo anavala zovala za chibakuwa ndi mlangali, ndipo anali nazo zokongoletsa za golide ndi miyala ya mtengo wapatali ndi ngale, ananyamula chikho cha golide mdzanja lake chodzala ndi zonyansa ndi zinthu zodetsa za chigololo chake; 5ndipo pamphumi pake dzina linalembedwa, Chinsinsi, Babulo wamkulu, mayi wa akazi achigololo, ndi wa zonyansa za dziko lapansi. 6Ndipo ndinaona mkazi ataledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu. Ndipo ndinadabwa pakumuona iye, ndi kuzizwa kwakukulu. 7Ndipo mngelo anati kwa ine, Chifukwa chiyani uli kudabwa? Ine ndikuuza chinsinsi cha mkaziyu, ndi cha chirombo chimene chamnyamula, chimene chili ndi mitu isanu ndi iwiri komanso nyanga khumi. 8Chirombo chimene wachionacho chinali, ndipo kulibe, ndipo chatsala pang’ono kutuluka ku phompho ndi kukaonongedwa: ndipo iwo akukhala padziko lapansi, amene maina awo sanalembedwe kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi m’buku la moyo, adzakhala odabwa, kuona chirombocho, kuti chinali, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako. 9Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru: Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri, amene mkaziyo wakhalapo. 10Ndipo pali mafumu asanu ndi awiri: asanu adagwa, imodzi ilipo, inayo sanafike kaye; ndipo pamene idzafika idzangokhala [chabe] kwa kanthawi. 11Ndipo chirombo chimene chinali ndipo kulibe, ndichonso chachisanu ndi chitatu, ndipo chili chachisanu ndi chiwiri, ndipo chikupita ku chionongeko. 12Ndipo nyanga khumi zimene waona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu, koma analandira ulamuliro monga mafumu, ola limodzi ndi chirombocho. 13Amenewa ali ndi mtima umodzi, ndipo anapereka mphamvu yawo ndi ulamuliro kwa chirombocho. 14Iwo adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa; pakuti iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu: ndipo iwo [amene ali] ndi iye oitanidwa, ndi osankhidwa, ndi okhulupirika.
15Ndipo anati kwa ine, Madzi amene waona, pamene mkazi wa chigololo wakhalapo, ndiwo anthu ndi makamu ndi mitundu ndi manenedwe. 16Ndipo nyanga khumi zimene waona, ndi zirombozo, zimenezi zidzadana naye mkazi wa chigololoyu, ndipo adzamupanga kukhala wabwinja ndi wamaliseche, ndipo zidzadya mnofu wake, ndipo adzamutentha ndi moto; 17pakuti Mulungu1 wapereka ku mitima yawo kuchita malingaliro ake, ndi kuchita ndi mtima umodzi, ndi kupereka ufumu wao kwa chirombocho kufikira mau a Mulungu2 akakwaniritsidwe. 18Ndipo mkazi amene waonayo ndiwo mzinda waukulu, umene uli ndi maufumu pamwamba pa mafumu adziko lapansi.
1Elohimu2Elohimu