Mutu 12

1Mu [nthawi] imeneyo, pamene khamu la anthu okwana zikwi khumi anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana wina ndi mzake, Iye anayamba kulankhula kwa ophunzira ake poyamba, Mudzichenjera ndi chotupitsa cha Afarisi, chimene chili chinyengo; 2komatu palibe chobisika chimene sichizavumbulutsidwa, kapena chinsinsi chimene sichizadziwika; 3chomwecho chilichonse chimene mudzanena mu mdima chidzamveka poyera, ndipo chimene mudzalankhulira mkhutu m’zipinda za mkati zidzalengezedwa pamwamba panyumba. 4Koma ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi ndipo akachita ichi palibenso china chimene iwo akhoza kuchita. 5Koma Ine ndikuonetsani amene mukuyenera kumuopa: Mudziopa Iye amene atapha ali nawonso ulamuliro wakuponya ku gehena; inde, ndinena kwa inu, mudzimuopa Iye. 6Kodi mpheta zisanu sizigulidwa ndi makobiri awiri? Ndipo imodzi mwa izo simaiwalika pamaso pa Mulungu1. 7Komatu ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu lonse limawerengedwa. Chomwecho musaope, inuyo muposa mpheta. 8Koma ndinena kwa inu, Aliyense amene azandivomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa munthu azamuvomereza iyenso pamaso pa angelo a Mulungu2; 9koma iye amene azandikana Ine pamaso pa anthu azakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu3; 10ndipo aliyense wakulankhula mau motsutsana ndi Mwana wa munthu chidzakhululukidwa kwa iye; koma kwa iye wakulankhula mokhumudwitsa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. 11Komatu pamene iwo adzakutengerani pamaso pa a m’sunagoge ndi kwa akulu ndi aulamuliro, musadandaule kuti mudzayankha bwanji kapena mudzayankha chiyani, kapenanso chimene mudzalankhula; 12pakuti Mzimu Woyera adzakuphunzitsani munyengo yake chimene mukuyenera kulankhula.

13Ndipo munthu wina kuchokera mu khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, lankhulani kwa m’bale wanga agawane ndi ine chuma cha masiye. 14Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandikhazikitsa Ine [monga] woweruza kapena wakugawira inu? 15Ndipo Iye anati kwa iwo, Ziyang’anireni, muzisungire nokha ku msiliro uliwonse, pakuti sichifukwa chakuti munthu ali nazo zochuluka kuti zikhoza kulingana ndi moyo wake umene ali nawo. 16Ndipo analankhula fanizo kwa iwo, nanena, Munda wa munthu wina wolemera unapereka zochuluka. 17Ndipo anaganiza mwa iye yekha nanena, Ndidzachita chiyani? Pakuti ndilibe [malo] amene ndikhoza kusungira zipatso zanga. 18Ndipo anati, Ndidzapanga ichi: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga ndi kumanga zazikulu, ndipo m’menemo ndidzaikamo zokolola zanga ndi zinthu zanga zabwino; 19ndipo ndidzanena kwa moyo wanga, Moyowe, uli nazo zinthu zabwino zochuluka zoikidwa kufikira zaka zambiri; udekhe wekha, nudye, numwe, nusangalale. 20Koma Mulungu4 anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku uno moyo wako udzafunidwa kwa iwe; ndipo zidzakhala za yani zimene wakonzazi? 21Uyu ndi munthu woziyikira yekha chuma, koma sali wolemera pa Mulungu5.

22Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Pachifukwa chimenechi ndinena kwa inu, Musadere nkhawa za moyo wanu, chimene mudzadya, kapena pa thupi lanu, chimene mudzavala. 23Moyo umaposa chakudya, ndipo thupi liposa chovala. 24Ganizirani za maku ngubwi, kuti samafesayi kapena kukolola; amenenso alibe nyumba yosungira kapena nkhokwe; ndipo Mulungu6 awadyetsa. Kodi inu muposa bwanji mbalame? 25Koma ndani mwa inu pakudera nkhawa akhoza kuonjezera mkono pa msinkhu wake? 26Chotero ngati inu simungathe kuchita ngakhale chaching’ono, chifukwa chiyani mudera nkhawa zina zonse? 27Ganizirani maluwa momwe amakulira; komatu ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo mu ulemelero wake sanavaleko monga mwa awa. 28Koma ngati Mulungu7 amaveka udzu, umene lero ukhalako ndipo mawa uponyedwa pa moto, koposa kotani inu, a chikhulupiliro chochepa? 29Ndipo inu, musafunefune chimene mudzadya kapena chimene mudzamwa, ndipo musamadere nkhawa; 30pakuti zinthu zonsezi mafuko a dziko lapansi amazifuna, ndipo Atate wanu wakumwamba amadziwa kuti muzisowa zinthu zimenezi; 31koma funani ufumu wake, ndipo izi [zonse] zidzaonjezedwa kwa inu. 32Musachite mantha, kagulu ka nkhosa inu, pakuti chikomera Atate wanu kukupatsani ufumu. 33Gulitsani zimene muli nazo ndi kupereka za chifundo; zikonzereni nokha matumba a ndalama amene sakutha, chuma chimene sichilephera kumwamba, kumene mbava siziwandikirako kapena njenjete kuchiononga. 34Pakuti kumene kuli chuma chako, kumenekonso mtima wako umakhalako. 35Muzimangire nonkha m’chiuno mwanu, ndi nyali zanu zikhale zoyaka; 36ndipo inu ngati anthu odikilira mbuye wao pamene abwera kuchokera ku ukwati, kuti pamene adzabwera ndi kugogoda, adzamutsegulire iye nthawi yomweyo. 37Odala ali akapolowo amene mbuye wao pobwera adzawapeza ali odikira; zoonadi ndinena kwa inu, kuti iye azazimangira yekha m’chiuno nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzawatumikira iwo. 38Ndipo ngati iye abwera mu ulonda wachiwiri, ndi kubweranso mu ulonda wachitatu, nawapeza [iwo] chomwecho, ali odala [akapolo] awa. 39Koma dziwani ichi, kuti ngati mbuye wa nyumba akadadziwa ola limene mbava ikubwera, akadakhala wodikira, ndipo sakanalola kuti nyumba yake ibowoledwe. 40Ndipo inu pamenepo, khalani tcheru, pakuti mu ola limene simukuganizira, Mwana wa munthu adzabwera. 41Ndipo Petro anati kwa iye, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa tonse? 42Ndipo Ambuye anati, Ndani pamenepo amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuyika woyang’anira nyumba yake, kuwapatsa iwo mlingo wa chakudya mu nyengo yake? 43Wodala ali kapolo amene mbuye wake pobwera adzamupeza chomwecho; 44zoonadi ndinena kwa inu, kuti azamuyika iye kukhala woyang’anira zimene ali nazo. 45Koma ngati kapoloyo anena mu mtima mwake, Mbuye wanga akuchedwa kubwera, ndi kuyamba kumenya anyamata ndi azakazi, ndi kudya ndi kumwa ndi kuledzera, 46mbuye wa kapoloyo adzafika mu tsiku limeneli iye sakuyembekezera, ndi ola limeneli iye sakulidziwa, ndipo adzamudula iye pawiri ndipo adzapereka gawo lake kwa osakhulupilira. 47Koma kapolo amene anadziwa cholinga cha mbuye wake, ndipo sadzikonzekeretsa [iye mwini] kapena kuchita chifuniro chake, adzakwapulidwa ndi [zikwapu] zochuluka; 48koma iye amene sanadziwe [ichi], ndipo anachita zinthu zoyenera mkwapulo, adzakwapulidwa ndi zikwapu zochepa. Ndipo kwa iye amene zaperekedwa zambiri, zambirinso zizafunidwa kuchokera kwa iye; ndipo kwa [munthu] amene anamuyikiza zambiri, adzafunsidwanso kubwezera zoposa. 49Ine ndabwera kudzaponya moto padziko lapansi; ndipo ndidzatani ngati unatha kuyatsidwa? 50Komatu ndili ndi ubatizo woti ndibatizidwe nawo, kodi ndidzakanizidwa bwanji kufikira utakwanitsidwa! 51Inu muganiza kuti ndabwera kudzapereka mtendere padziko lapansi? Ayi ndithu, ndinena kwa inu, komatu magawano: 52pakuti kudzatero kuti padzakhala asanu mnyumba ogawikana; atatu adzatsutsana ndi awiri: 53tate kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wa mwamuna kutsutsana ndi tate wake; mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi, ndi mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi wake; mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkazi kutsutsana ndi mpongozi wake.

54Ndipo Iye anati kwa makamuwo, Pamene muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo mumanena kuti mvula ikubwera; ndipo zimachitkadi. 55Ndipo pamene [inu muona] mphepo yowomba kum’mwera, mumanena, Kutentha; ndipo zimachitikadi. 56Achinyengo inu, mumadziwa kuweruza maonekedwe a dziko lapansi ndi kumwamba; nanga [kuli kotani kuti] inu simudziwa nthawi iyi? 57Ndipo chifukwa chiyani pa inu nokha simutha kuweruza chimene chili chabwino? 58Pakuti pamene ukupita naye mzako wa mlandu ku bwalo la milandu, yetsetsabe poyenda m’njira kukambirana kuti uyanjane naye, kuti mwina angakutengere kwa woweruza, ndipo woweruza angakupereke kwa msilikali, ndipo msilikali angakuponye iwe mndende. 59Inetu ndinena kwa iwe, Sudzatuluka kumeneko mwanjira ina iliyonse kufikira utalipira kobiri lomaliza.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu7Elohimu