Mutu 27

1Koma pamene zinatsimikizika kuti tikwere ngalawa kupita ku Italiya, iwo anampereka Paulo pamodzi ndi andende ena kwa kentuliyo, dzina lake Yuliyo, wa gulu la Augusto. 2Ndipo pamene tinakwera ngalawa ya Adramutiyo imene imapita ku malo amphepete mwa Asiya, ife tinanyamuka, Aristarko, m’Makedoniya waku Tesalonika anali nafe. 3Ndipo tsiku lotsatiralo tinafika ku Sidoni. Ndipo Yuliyo anamsamalira bwino Paulo ndipo anamlola kupita kwa abwenzi ake kukadzipumulitsa yekha. 4Ndipo poyamba ulendo wathu panyanja tinayenda mokankhidwa ndi mphepo ya Kupro, chifukwa mphepoyi inalimbana nafe. 5Ndipo titayenda panyanja ya Kilikiya ndi Pamfiliya tinafika ku Mura ndi Lukiya: 6ndipo kumeneko kentuliyo pamene anapeza ngalawa ya Alesandriya ikupita ku Italiyo, anatikweza ife m’ngalawamo. 7Ndipo tinayenda pang’onopang’ono kwa masiku ambiri, ndipo movutika tinafika pandunji pa Knido, mphepo sinatilole ife, tinayenda mokankhidwa ndi mphepo ya Krete pandunji pa Salimone; 8ndipo pokocheza movutika tinafika pamalo ena otchedwa Pokocheza Pokoma, pamene panali pafupi ndi mzinda wa Laseya. 9Ndipo nthawi yochuluka itapita, komanso ulendo wa panyanja utakhala oopsa, chifukwa nyengo ya kusala kudya inali itapita kale, Paulo anawachenjeza iwo, 10nanena, Amuna inu, ndikutha kuona kuti ulendowu ukhala ovuta komanso tiwononga zambiri, osati katundu yekha ndi ngalawayi, komanso ngakhale miyoyo yathu. 11Koma kenturiyo anakhulupilira watsigiro ndi mwini ngalawa kusiyana ndi zimene Paulo analankhula. 12Ndipo pokhala kuti dooko linali ndi mphepo yozizira, ambiri anapangira kuti achokepo pamenepo, kuti mwina akhoza kukafika ku Foinika kukutentha, dooko la ku Krete loyang’ana kumpoto cha kuvuma ndi kumwera cha kuvuma. 13Ndipo mphepo ya mwera imaomba pang’onopang’ono, naganiza kuti apeza chinthu, atayeza anaponya nangula napita mphepete mwa Krete. 14Koma pasanapite nthawi kunabwera mphepo ya namondwe yotchedwa Eurokulo. 15Ndipo ngalawa inakodwa ndi kukankhidwa, ndipo sinakhoze mutu wake kulimbana ndi mphepoyo, ndipo ngalawa inakankhidwa ndi namondweyo. 16Koma pokankhidwa mwa liwiro ndi mphepoyo tinafika pa chilumba china chotchedwa Klauda, tinavutika kwambiri kuti tikhoze kuongolera ngalawayo; 17imene povutika kwambiri, iwo anagwiritsa ntchito zothandizira, nakulunga nazo ngalawayo; ndipo poopa kuti akhoza kukafika m’Surti ndi kugwera kumeneko, ndipo anatsitsa matanga ndipo anatengedwa motero. 18Koma namondweyo anakula mphamvu pa ife, ndipo tsiku lotsatiralo iwo anaponya katundu m’nyanja, 19ndipo tsiku lachitatu ndi manja awo anataya zipangizo za m’ngalawamo. 20Ndipo dzuwa kapena nyenyezi sizinaoneke kwa masiku ambiri, ndipo namondwe wamkulu anali pakati pathu, pamapeto pake chiyembekezo cha kupulumuka kwathu chinachoka. 21Ndipo pamene iwo anakhala nthawi yaitali osadya chakudya, pamenepo Paulo anayimilira pakati pawo nati, Amuna inu, mukanamvera ine, ndi kusayenda kuchoka ku Krete sitikadakumana ndi chionongeko komanso kutayika uku. 22Ndipo tsopano ndikulimbikitsani kuti mulimbe mtima, pakuti palibe amene atataye moyo mwa inu, koma kupatula ngalawa yokhayi. 23Pakuti mngelo wa Mulungu1, amene ine ndimtumikira, anayima pambali panga usiku wapitawu, 24nanena, Usaope, Paulo; iwe ukuyenera ukayime pamaso pa Kaisara; ndipo taona, Mulungu2 wapereka kwa iwe awa onse amene akuyenda nawe. 25Pamenepo khalani olimba mtima, amuna inu, pakuti ndikukhulupilira Mulungu3 kuti izi zikhala chonchi, monga zanenedwa kwa ine. 26Koma tikuyenera kutayika pa chisumbu china chake. 27Ndipo pamene linafika tsiku la khumi ndi chinayi, pokankhidwa nayo mphepo tinafika m’Adriya, pakati pa usiku amarinyero anaganiza kuti nthaka inawandikira iwo, 28ndipo atayesa madzi anapeza mikwamba makumi awiri, ndipo atapita patsogolo pang’ono anayesanso napeza mikwamba khumi ndi isanu; 29ndipo poopa kuti tingatayike pa malo amiyala, tinaponya anangula anayi kumakaliro, iwo anakhumba kukanacha.

30Koma amalinyero anafuna kuthawa mu ngalawamo, ndipo anatsitsira mabwato m’nyanja monga ngati akuponya anangula kumakaliro, 31Paulo anati kwa kenturiyo ndi asilikali, ngati awa sakhala mngalawamu simungapulumuke. 32Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwa. 33Ndipo pamene kumacha, Paulo anawalimbikitsa iwo onse kuti adye, nanena, Inu mwakhala masiku khumi ndi anayi mukupenyerera m’chiyembekezo osadya chakudya. 34Pamenepo ndikulimbikitsani kuti mudye, pakuti zimenezi zikukhudza chitetezo chanu; pakuti palibe ngakhale tsitsi limodzi la m’mutu mwanu lidzaonongeka. 35Ndipo atanena zinthu zimenezi anatenga mkate, nalemekeza Mulungu4 pamaso pa onse, ndipo atanyema anayamba kudya. 36Ndipo onse analimba mtima, nawonso anadya. 37Ndipo ife tonse amene tinali m’ngalawa, miyoyo yonse, tinalipo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi limodzi. 38Ndipo atakhuta chakudya, anapeputsa ngalawayo, natayira tirigu m’nyanja. 39Ndipo pamene unali masana sanathe kuuzindikira mtundawo; koma anaona mulu wa mchenga, umene anaganizira ngati angakwanitse kukocheza ngalawayo; 40ndipo, m’mene anaponya anangula, anawasiya m’nyanjamo, nthawi yomweyo anamasulanso zingwe zomangira tsigiro ndipo anakweza thanga ku likulu, nalunjikitsa ku mchengawo. 41Ndipo pogwera pamalo pamene nyanja ziwiri zimakumana anakocheza ngalawayo, ndipo makaliro anaombedwa mwamphamvu ndi mafunde. 42Ndipo upangiri wa asilikali unali wakuti aphe andendewo, kuti mwina akhoza kusambira ndi kuthawa. 43Koma kenturiyo anafunitsitsa kupulumutsa Paulo, napondereza cholinga chawocho, ndipo analamulira iwo amene akhoza kusambira kuti asambire, anaziponya kaye iwo poyamba [m’nyanjamo], nafika ku mtunda; 44ndipo ena onse, anakwera matabwa, ena pa zinthu zina [zimene zinachoka] ku ngalawayo; ndipo kunachitika kuti onse anapulumukira ku mtunda.

1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu