Mutu 26
1Ndipo Agripa anati kwa Paulo, ndi kololedwa kudziyankhulira mwini wekha. Pamenepo Paulo anatambasula dzanja lake nalankhula modziteteza: 2Ndikuzitenga ndekha kukhala wa mwayi, mfumu Agripa, podziyankhira ndekha lero pamaso panu zokhudza zinthu zonse zimene ndakhala ndikutsutsidwa ndi Ayuda, 3makamaka chifukwa mukudziwa miyambo ndi mafunso amene ali pakati pa Ayuda; chomwecho ndikupemphani kuti mundimvere moleza mtima. 4Mayendedwe a moyo wanga pamenepo kuyambira pa ubwana wanga, umene kuyambira pachiyambi unadutsa pakati pa mtundu wanga mu Yerusalemu, adziwa Ayuda onse, 5amene anandidziwa ine kuyambira pachiyambi [pa moyo wanga], ngati angachitire umboni iwowa, kuti molingana ndi mfundo zokhwima za chipembedzo chathu ndinakhala Mfalisi. 6Ndipo tsopano ine ndiyimilira kufuna kuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo cha lonjezano lopangidwa ndi Mulungu1 kwa makolo athu, 7kwa mafuko onse khumi ndi awiri akutumikira usana ndi usiku kuti chiyembekezo chifike; chiyembekezo chake chiti, mfumu, chimene akunditsutsa nacho Ayudawa. 8Chifukwa chiyani chiweruzidwa chinthu chosakhulupirika pamaso panu ngati Mulungu2 aukitsa akufa? 9Inedi ndinaganiza kuchita koposa kutsutsana ndi dzina la Yesu Mnazarayo. 10Chimenenso ndinachita m’Yerusalemu, ndipo ine mwini ndinatsekera mndende oyera mtima ambiri, nditalandira chilolezo kuchoka kwa akulu ansembe; ndipo pamene iwo amaphedwa ndimavomerezana nawo. 11Ndipo kawirikawiri ndinawazunza iwo m’masunagoge monse, ndi kuwakakamiza anene za mwano. Ndipo ndinachita ukali owirikiza motsutsana nawo, ndinawazunza ngakhale m’mizinda imene [ili kunja kwa dziko lathu]. 12Ndipo pamene, [zinachitika] izi, ndimayenda kupita ku Damasiko, ndi ulamuliro komanso mphamvu kuchokera kwa akulu ansembe, 13masana, pamene ndimayenda, amfumu, ndinaona kuwala kwa dzuwa kuchoka kumwamba mozungulira ine pamodzi ndi iwo amene ndimayenda nawo pamodzi. 14Ndipo, pamene tonse tinagwa pansi, ndinamva mau akunena kwa ine m’chilankhulo cha Chiheberi, Saulo, Saulo, undizunziranji Ine? Ndi kovuta kwa iwe kulimbana ndi pachothwikira. 15Ndipo ine ndinati, Ndinu ndani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati, Ndine Yesu amene iwe ukumzunza: 16koma imilira nunyamuke pamapazi pako; pakuti, pa cholinga ichi Ine ndaonekera kwa iwe, kukusankha kukhala mtumiki ndi mboni ya zimene waonazi, ndi zimene Ine ndidzakuonetsera m’menemo, 17kukuchotsa iwe pakati pa anthu, ndi amitundu, kupita kumene Ine ndidzakutuma, 18kutsegula maso awo, kuti iwo akachoke mu mdima ndi kupita ku kuwala, ndi kuchoka ku mphamvu ya Satana kupita kwa Mulungu3, kuti akalandire chikhululukiro cha machimo ndi cholowa pakati pa iwo amene ayeretsedwa pa kukhulupilira mwa Ine. 19Pamenepo, mfumu Agripa, ndinali wosamvera ku masomphenya akumwamba; 20komatu koyamba kwa iwo a m’Damasiko ndi Yerusalemu, ndi zigawo zonse za Yudeya, ndi kwa amitundu, kukalengezedwe kuti iwo alape ndi kutembenukira kwa Mulungu4, kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima. 21Chifukwa cha zinthu izi Ayuda, anandigwira ine mkachisi, anayesera kundimanga ndi kufuna kundipha. 22Pamenepo ndinakumana ndi thandizo limene linali lochokera kwa Mulungu5, ine ndayimikika chilili kufikira tsiku la lero, kuchitira umboni ana ndi akulu omwe, sindinalankhule kena kalikonse kupatula zinthu zimene aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika, 23[monga,] ngati Khristu akamve zowawa; ngati woyamba, kuuka kwa akufa, kuti akalengeze kuwala kwa anthu komanso kwa amitundu. 24Ndipo pamene iye amayankhula mau odziteteza ndi zinthu izi, Festo anati ndi mau okweza, Kodi wapenga, Paulo; kuphunzira udyo kwako kwakupangitsa misala. 25Koma Paulo anati, Sindinapenge ine, wolemekezeka kwambiri Festo, koma ndikulankhula mau a choonadi ndiponso modekha; 26pakuti mfumu yadziwitsidwa zinthu zimenezi, kwa iyenso ndalankhula naye mwa ufulu. Pakuti ndatsimikizika kuti zinthu zimenezi palibe chimene chabisidwa kwa iye; pakuti izi sizinachitike mseri. 27Mfumu Agripa, mumakhulupilira aneneri kodi? Ndikudziwa kuti mumakhulupilira. 28Ndipo Agripa [anati] kwa Paulo, Mu kanthawi kochepa ukufuna kundikopa ine kukhala Mkhristu. 29Ndipo Paulo [anati], Ndikhoza kutero kwa Mulungu6, mu kanthawi kochepa ngakhale nthawi yambiri, osati kwa inu nokha, koma kwa onse amene andimva lero, akhale chimene ine ndili, kupatula nsinga izi. 30Ndipo mfumu inayimilira, ndi kazembe ndi Bernike ndi onse amene anakhala nawo, 31ndipo atapita padera, analankhulana wina ndi mzake nanena, Munthu uyu sanachite kanthu koyenera kuphedwa kapena kumangidwa. 32Ndipo Agripa anati kwa Festo, Munthu uyu anakamasulidwa akadakhala kuti sanakadandaule kwa Kaisara.
1Elohimu2Elohimu3Elohimu4Elohimu5Elohimu6Elohimu